MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kudzipereka kwa Mulungu N’kofunika Kuposa Kuchita Masewera
Kodi kuchita masewera n’kofunika? Inde, koma si kofunika kwambiri tikayerekezera ndi kuchita zinthu zomwe zingatithandize kuti tikhale paubwenzi wabwino ndi Yehova. (1 Tim. 4:8) Choncho, n’zofunika kwambiri kuti Akhristu asamalole kuti masewera aziwalepheretsa kuchita zinthu zauzimu.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE MUYENERA KUDZIWA PA NKHANI YOCHITA MASEWERA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
1. Kodi tingaphunzire maluso ati tikamachita masewera?
2. Kodi ndi mfundo ziti zomwe zingatithandize kudziwa ngati masewera enaake ali abwino kapena ayi?
3. Kodi lemba la Salimo 11:5 lingatithandize bwanji kusankha masewera abwino?
4. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji lemba la Afilipi 2:3 komanso la Miyambo 16:18 tikamachita masewera?
5. Kodi lemba la Afilipi 1:10 lingatithandize bwanji kuti tisamawononge nthawi yathu yambiri tikuonera kapena kuchita masewera enaake?