Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 7/8 tsamba 17-19
  • Kodi Ndiloŵe m’Timu Yasukulu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndiloŵe m’Timu Yasukulu?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Ali Otchuka
  • “Mbali Yoipa”
  • Chitsenderezo cha Ausinkhu Wanu
  • Zoloŵa M’malo Zabwino
  • Kodi Ndiyenera Kuloŵa Timu Yamaseŵero?
    Galamukani!—1996
  • Maseŵero a Timu Kodi Ali Bwino kwa Ine?
    Galamukani!—1996
  • Kuika Maseŵera m’Malo Ake Oyenera
    Galamukani!—1991
  • Mavuto Okhala m’Maseŵera Lerolino
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 7/8 tsamba 17-19

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndiloŵe m’Timu Yasukulu?

“Kuseŵera kunali kosangalatsa ndiponso kokondweretsa. Kunandipangitsa kudzimva bwino. Pamene uli wachichepere ndiyeno pomalizira pake nkupeza chinachake chimene umachichita bwino zedi, sumafuna kuchileka.”—Robert.

MWINAMWAKE nanunso mumasangalala ndi kuseŵera maseŵera a m’timu. Mumawakonda maseŵerawo, ubwenzi wabwino, ndi chisangalalo. Mungamalingaliredi zokhala ngwazi, mukumalingalira za kuchemerera kwa khamu pamene mugoletsa pamaseŵera a basketball, kuugwira mpirawo, kapena kumwetsa chigoli chimene chimapatsa timu yanu chilakiko.

Chirichonse chimene chingakhale chifukwa chanu cha kutenthedwa maganizo ndi maseŵera, achichepere ambiri amakhala ndi chifukwa chofananacho. Iwo amasangalala kwenikweni kukhala ndi phande m’maseŵera a m’timu, monga ngati mpira wamiyendo, mpira wachitanyu, basketball, baseball, ndi hockey. The Education Digest ikufotokoza kuti: “Ophunzira a ku [United States] oposa pa 5.2 miliyoni analoŵetsedwa m’maseŵera olira nyonga kusukulu yasekondale m’chaka chasukulu cha 1986-87, chiŵerengero chapamwamba koposa m’zaka zinayi. Ndiponso, sukulu zasekondale zinawonjezera maseŵera atsopano m’zaka 10 zapitazo, maseŵera ambiri olinganizidwira asungwana.”

Chifukwa Chake Ali Otchuka

Kutchuka kwakukuku kwa maseŵera kunatchulidwa m’mawu aŵa a mwamuna wanzeru wakale amene ananena kuti: “Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yao.” (Miyambo 20:29) Maseŵera amapereka njira yotsitsimula yotulutsira mphamvu ndi nyonga zimene zimachuluka m’zaka za uchichepere. Iwo angapereke chitokoso chabwino ponse paŵiri kuthupi ndi maganizo. Kukhala ndi phande m’maseŵera kungakhalenso kosangalatsa ndiponso koseketsa, kumasuka ku dongosolo lanthaŵi zonse la ntchito yakusukulu ndi ntchito yapambuyo pa sukulu.

Kuwonjezerapo, ena amatsutsa kuti kuseŵera m’maseŵera a m’timu kumamangirira makhalidwe. Bukhu lakuti The High School Survival Guide, lolembedwa ndi Barbara Mayer likuti: “Kuphunzira ndi lingaliro la kudzipereka limene mumafunikira kulisonyeza lidzakuphunzitsani mmene mungadziperekere ku chonulirapo chopindulitsa. . . . Kukhala ndi phande m’maseŵera kungakuthandizeni kukhala mtsogoleri.”

Komabe, siachichepere onse amene ali ndi zolinga zabwino zoseŵerera maseŵera. Ulemerero, kutchuka, ndi ulemu zirinso zisonkhezero zamphamvu. “Ngati munali m’timu,” akukumbukira motero Reggie, “munalingaliridwa kukhala mmodzi wa anyamata okhumbirika koposa yemwe anakhalapo pasukulupo.”

Baibulo limavomereza kuti “maseŵera athupi ali ndi phindu lina.” (1 Timoteo 4:8, Today’s English Version) Ndipo kungawoneke kuti kuloŵa m’timu yasukulu kungakhale njira yopezera phindu limenelo. Komabe, achichepere ambiri apeza kuti kuipa kwakuloŵa m’timu yasukulu kumaposa mapinduwo.

“Mbali Yoipa”

Magazini a Seventeen akusimba kuti: “Maseŵera ali ndi mbali yoipa, kumene anthu amaika phindu lopambanitsa pa kupambana. Kwa wotsogolera, kupambana kungatsogolere ku kukwezedwa pantchito kapena kuwonekera pawailesi yakanema. Kwa kholo, kupambana kungatanthauze kuyenera kwakunyadira mwana kapena lingaliro lakukhala wokhutiritsidwa ndi chikwaniritso cha mwanayo. Kwa wochita maseŵera olira nyongayo, kupambana kungatanthauze kulipiriridwa kumka kukaphunzira kudziko lakunja, kutchulidwa m’lipoti lanyuzipepala, kukhumbiridwa ndi anzake a m’kalasi ndi achinansi.”

Ochita maseŵera olira nyonga ena apasukulu amaganizanso zokhala akatswiri oseŵera. “Ndinkaganiza zoseŵera m’mipikisano ya mzinda ndi dziko ndipo kenaka ndi akatswiri kwenikweni,” anatero Gerald wachichepere. “Ndinadzilingalira nditalemera, kusonyeza zinthu zanga m’malonda osatsidwa, kukhala wotchuka, kukhala chitsanzo, ndi kumapita kocheza ndi msungwana wokongola koposa pasukulu.”

Pamenepo, nkosadabwitsa kuti maseŵera m’masukulu ambiri amaseŵeredwa mofunika koposa! Kusangalala ndi kulimbitsa thupi kumaiwalidwa. Monga momwe magazini a Seventeen akupitirizira kunena kuti: “Mwadzidzidzi kupambana kumafafaniza kuda nkhaŵa ndi kuwona mtima, ntchito yakusukulu, thanzi, chimwemwe, ndi mbali zina zofunika za moyo. Kupambana kumakhala chinthu chofunika koposa, ndipo chisonkhezero chimakula.”

Pokhala ndi mkhalidwe uwu wakupambana pa mtengo uliwonse, nzosadabwitsa kuti kuvulala kwakantha oseŵera maseŵera olira nyonga ambiri pasukulu. Chiwawa chochitidwa ndi oseŵerawo, ochemerera, ndipo ngakhale makolo nthaŵi zina chimakhalamo m’maseŵerawo. Ndipo kutemera mangolomera, monga ngati masteroid, kukufalikira ngakhale pakati pa oseŵera maseŵera olira nyonga achichepere.

Chotero pamene kuli kwakuti kuseŵera m’timu kungakhale ndi maubwino ena ake, kungayambitsenso mzimu wakupikisana wopambanitsa, maloto akukhala ndi chuma chambiri, ndi chikhumbo chodzikuza chakukhala ndi ulemerero. Zinthu zimenezi zimatsutsana kotheratu ndi uphungu Wabaibulo wakuti ‘tisakhale . . . outsana,’ tisakonde ndalama, ndiponso tisafune ulemerero waumwini. (Agalatiya 5:26; Miyambo 25:27; 1 Timoteo 6:10) Kuloŵa m’timu yasukulu kungakuvumbuleni bwino lomwe ku zisonkhezero zoipa m’njira yamphamvu kwambiri.

Chitsenderezo cha Ausinkhu Wanu

Ophunzitsa kaŵirikaŵiri amatamanda mwaŵi umene maseŵera amapereka wakumanga maunansi athithithi ndi ausinkhu wanu. Modabwitsa, ndimwaŵi umodzimodziwu umene umapangitsa mavuto kwa achichepere Achikristu. Baibulo limati: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.”—1 Akorinto 15:33; 2 Akorinto 6:14.

Kunena zowona, kodi ndimtundu wanji wamayanjano amene mothekera kwenikweni mudzaloŵamo m’chipinda chosungira zinthu cha timu? Wachichepere wina akuvomereza motere: “Munali kutukwana kochuluka ndi kugwiritsira ntchito chinenero choipa. Anyamatawo nthaŵi zonse ankalankhula za asungwana ndipo ankabweretsa mabuku osonyeza umaliseche kuti tidzipenya.” Kuwonjezerapo, kukulitsa ndi kusunga mzimu wa timu kaŵirikaŵiri kumafuna kuti mudzikumana mwamayanjano ndi anzanu a m’timu kuchiyambi ndi kumapeto a maseŵera ndi magawo okonzekera.

Zowonadi, kungakhale kotheka kuloŵa m’timu ndikukhalabe osaloŵetsedwamo mwamayanjano. Koma monga momwe msungwana wazaka 14 zakubadwa akuvomerezera kuti: “Chitsenderezo cha ausinkhu wanu nchamphamvu koposa kwakuti simungathe kungoseŵera nkubwerera kunyumba.” Chotero Baibulo limafunsa kuti: ‘Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake?’ (Miyambo 6:27) Pokakamizidwa ndi anzawo a m’timu, achichepere ena adzipeza ali pamapwando kumene zakumwa zoledzeretsa ndi mankhwala ogodomalitsa zinagwiritsiridwa ntchito, kuphatikizapo nyimbo zoluluza ndi mikhalidwe yololerana ndi osiyana nawo ziŵalo.

Talingalirani chokumana nacho cha wachichepere wotchedwa Robert. Iye akuti: “Pambuyo poloŵa m’timu, mavuto anali aakulu. Padali chitsenderezo champhamvu chakugonana ukwati usanakhale, kugwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa, kumwa, ndi kupita kumapwando oipa. Sindinakhulupirire konse kuti zinthu zoterozo zingagwirizane ndi maseŵera akusukulu yasekondale. M’bwalo ngakhale kunja, umayembekezeredwa kuyenda, kulankhula, ndikuchita mofanana ndi anyamata ena onsewo.”

Chosafunikiranso kunyalanyazidwa ndicho chiyambukiro chimene kukhala kwanu ndiphande m’maseŵera chingakhale nacho pa dongosolo la zochita zanu zauzimu. (Ahebri 10:23-25) “Kaŵirikaŵiri, maseŵera ndi kukonzekera zimawombana ndi misonkhano Yachikristu,” akutero Gerald wachichepere.

Zoloŵa M’malo Zabwino

Ndithudi, kuphunzira maseŵera olira nyonga kungaperekedwe mkati mwa maola akuphunzira apasukulu monga mbali ya ndandanda ya maphunziro yokhazikika, ndipo kaŵirikaŵiri sipamakhala chiletso chirichonse kwa wachichepere Wachikristu kupezekapo pamakalasi oterowo. Ndiponso, mikhalidwe imasiyana m’maiko osiyanasiyana. Komabe, achichepere pakati pa Mboni za Yehova mwachisawawa amapeŵa kuloŵetsedwa m’maseŵera ochitika m’maola osakhala asukulu. Tsopano, zimenezi sizikutanthauza kuti inuyo monga wachichepere Wachikristu simungasangalale ndi maseŵera. Komabe, zimatanthauza kuti mudzafunikira kuchitapo kanthu kenakake.

Mwachitsanzo, mungalankhule ndi makolo anu ponena za kukonzekera kupita nawo kumalo kwina, monga ngati kukaseŵera. Ichi chingapereke nthaŵi kwa banja lanu ndi mabwenzi kukasangalala ndi maseŵera ena abwino. Kapena mungaitane achichepere Achikristu angapo kubwera pamodzi ndi kutchova njinga, kuseŵera mpira, kapena kuchita mpikisano umene mungafune.

Komabe, chofunika koposa nchakuti mupeŵe mzimu wakupikisana wopambanitsa. Kukhala ndi matimu alamulo, oikidwiratu kumayambitsa mzimu wakufuna kupambana pamtengo uliwonse ngakhale ngati oseŵera onse ali Akristu. Chotero kaŵirikaŵiri chimakhala chabwino koposa kuzilola zinthu kukhala zamwadzidzidzi. Kwenikwenidi, kukhala ndi chiyang’aniro chakutichakuti cha wachikulire nthaŵi zonse kumakhala lingaliro labwino.

Kunena zowona, maseŵera amwadzidzidzi sangakhale ndi zisangalatso za maseŵera olinganizidwa akusukulu. Koma mungasangalalebe. Robert anasankha kuleka kuseŵera m’timu yake yakusukulu. Koma iye akuti: “Ndimasangalalabe kwambiri kuseŵera maseŵera. Ndimasangalala koposa tsopano kuposa kale. Pamene ndimaseŵera tsopano, sindimatero kuti ndipambane pamtengo uliwonse, ndiponso sindimakhala ndi mzimu wampikisano.”

Kumbukirani kuti pamene mtumwi Paulo anauza Timoteo wachichepere kuti: ‘Chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono,’ iye anawonjezera kuti, ‘koma [kudzipereka kwaumulungu, NW] kupindula zonse.’ Mowonekeratu, kukhala katswiri wa maseŵera olira nyonga sindicho chifuno cha Mkristu m’moyo. Chotero aikeni maseŵera m’malo ake. Kodi nkumawonongeranji nthaŵi imene ingagwiritsiridwe ntchito mopindulitsa kumangirira uzimu wanu? Kumbukirani kuti: Kudzipereka kwaumulungu ‘kukhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’—1 Timoteo 4:8.

[Chithunzi patsamba 18]

Mzimu wakupambana pamtengo uliwonse ngwaukulu m’maseŵera ambiri apasukulu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena