Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 3/8 tsamba 12-14
  • Maseŵero a Timu Kodi Ali Bwino kwa Ine?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maseŵero a Timu Kodi Ali Bwino kwa Ine?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maseŵero—Mapindu Ake
  • Kudziŵika, Chipambano, ndi Kutchuka
  • Olephera
  • Kodi Ndiyenera Kuloŵa Timu Yamaseŵero?
    Galamukani!—1996
  • Kodi Ndiloŵe m’Timu Yasukulu?
    Galamukani!—1991
  • Mavuto Okhala m’Maseŵera Lerolino
    Galamukani!—1991
  • Kuika Maseŵera m’Malo Ake Oyenera
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 3/8 tsamba 12-14

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Maseŵero a Timu Kodi Ali Bwino kwa Ine?

“Ndimakonda maseŵero. Ndimamvadi bwino kwambiri. Ndipo ndimasangalala kuyanjana ndi mabwenzi anga.”—Sandy wazaka 14.

“KUSANGALALA!” “Kutengeka maganizo!” “Kupambana!” Izi zinali zifukwa zina zimene achichepere a ku United States ndi a ku Canada anapereka pamene anafunsidwa chifukwa chimene amaseŵerera maseŵero olinganizidwa. Mwachionekere, achichepere ambiri alinso ndi chisangalalo chimodzimodzicho.

Titenge United States, mwachitsanzo. Malinga ndi buku lakuti Your Child in Sports, lolembedwa ndi Lawrence Galton, “chaka chilichonse, Aamereka achichepere okwanira 20 miliyoni azaka zisanu ndi chimodzi ndi kuposapo amaseŵera, kapena amayesa kuseŵera, m’matimu olinganizidwa.” Ndipo pamene kuli kwakuti zaka zingapo zokha zapitazo maseŵera a timu olinganizidwa anali a amuna chabe, ziŵerengero zazikulu za atsikana zikuseŵera baseball, basketball, ndipo ngakhale kupikisana wina ndi mnzake m’bwalo la mpira.

Mwinamwake mumakonda maseŵero ndipo mumalingalira kuti kuloŵa timu kungakhale chinthu chosangalatsa. Kapena zingakhale kuti mukupeza chilimbikitso chochuluka—mwinamwake ngakhale chikakamizo—kuchokera kwa makolo, aphunzitsi, kapena alangizi a maseŵero kuti muloŵe timu. Mulimonse mmene zingakhalire, kukhala ndi mbali m’maseŵero a timu kumafuna nthaŵi yochuluka ndi nyonga. Motero, kuli kwanzeru kudziŵa ubwino wake ndi kuipa kwake. Choyamba, tiyeni tione ena a maubwino ake.

Maseŵero—Mapindu Ake

“Chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono,” limatero Baibulo. (1 Timoteo 4:8) Ndipo achichepere mosakayikira angapindule ndi maseŵero olimbitsa thupi. Mu United States, achichepere ochuluka akudwala matenda a kunenepa, matenda a BP, ndi kukhala ndi cholestrol wambiri. Kuchita maseŵero olimbitsa thupi nthaŵi zonse kungathandize kwambiri kuletsa mavuto ameneŵa. Malinga ndi nkhani ya m’magazini a American Health, achichepere amene amalimbitsa thupi nthaŵi zonse “samafasa m’chifuŵa kuposa achichepere amene samaseŵera [osadzitanganitsa]. Amene amalimbitsa thupi nthaŵi zonse amachitanso bwino kwambiri m’maseŵero ndipo samanenepa kwambiri.” Ofufuza amanenanso kuti kulimbitsa thupi kumathetsa kupsinjika maganizo, kumachepetsa kutopa, ndipo kumakupatsani kukhala ndi tulo tabwino.

Modabwitsa, buku lakuti Your Child in Sports limanena kuti: “Zapezeka kuti matenda ambiri a achikulire amayambira kuubwana.” Motero madokotala ambiri amaona kuti mapindu a kulimbitsa thupi nthaŵi zonse amafika ngakhale kuuchikulire. Wolemba nkhani Mary C. Hickey akunena kuti: “Kufufuza kwapeza kuti ana amene amachita maseŵero kaŵirikaŵiri amakhala athanzi labwino atakula.”

Ambiri amalingalira kuti maseŵero a timu ali ndi mapindu ena apadera. Atate wina anati ponena za kuseŵera mpira kwa mwana wake: ‘Kumamchititsa kusangokhala m’makwalala. Kumamphunzitsa nzeru.’ Ena amalingalira kuti kuseŵera m’timu kumaphunzitsa wachichepere kugwira ntchito ndi ena—luso limene lingakhale ndi mapindu a moyo wonse. Maseŵero a timu amaphunzitsanso achichepere kulondola malamulo, kukhala odziletsa, kuchita utsogoleri, ndi kukhala odekha ponse paŵiri pamene apambana ndi pamene alephera. “Maseŵero amaphunzitsa achichepere zinthu zambiri,” akutero Dr. George Sheehan. “Amachititsa ophunzira kuona zinthu zimene amamva kwa aphunzitsi: kulimba mtima, luso, kudzipereka.”—Current Health, September 1985.

Mulimonse mmene zingakhalire, kukhala m’timu imene yapambana kungakulitse kudzidalira kwa munthu. “Ngati ndagolitsa kapena ndayesa kuti ndigolitse,” akutero Eddie wachichepere, “ndimanyada.”

Kudziŵika, Chipambano, ndi Kutchuka

Komabe, kwa achichepere ena chinthu chimene chimawakopa kwenikweni m’maseŵero a timu ndicho kukhala ndi chiyanjo cha mabwenzi awo ndi kudziŵika. “Nthaŵi zonse ukachita chabwino,” akufotokoza motero Gordon wazaka 13, “onse amangokusisita pamsana.”

Buku lakuti Teenage Stress, lolembedwa ndi Susan ndi Daniel Cohen, limati: ‘Ngati pali njira iliyonse yomuka nayo ku kutchuka, makamaka kwa anyamata, ndiyo maseŵero. . . . Nthaŵi zambiri simungapeze ngwazi yamaseŵero m’timu ya mpira kapena ya basketball akumalakalaka kudziŵika.’ Kufufuza kwina kunasonyeza kwenikweni mmene amaseŵero alili olemekezeka kwambiri. Ophunzira anafunsidwa kaya anafuna kukumbukiridwa monga ngwazi yamaseŵero kapena monga wophunzira wanzeru kwambiri, kapena monga munthu wotchuka kwambiri. Pakati pa anyamata, ambiri anasankha kukhala “ngwazi yamaseŵero.”

Kunena kuti woseŵera mpira kapena basketball amalandira ulemu wambiri kuposa munthu wophunzira sikodabwitsa kwambiri pamene mulingalira za chisamaliro chonga kulambira chimene chimaperekedwa ndi aulutsi a nkhani pa akatswiri. Nkhani zambiri zimene zimakambidwa zimasumikidwa pa kuchuluka kwa ndalama zimene amalandira ndi moyo wawo wa tayetaye. Nchifukwa chake achichepere ambiri, makamaka amene amakhala m’matauni, amaona maseŵero akusukulu monga mlatho womka nawo ku chipambano—njira yothaŵira umphaŵi!

Mwatsoka lanji, zinthu sizimakhala monga momwe ziyembekezo zimenezo zilili. Nkhani ina ya mutu wakuti “Kodi ndi Amaseŵero Angati Amene Amakhala Akatswiri?” ya m’magazini a Current Health inapereka ziŵerengero zopangitsa munthu kuganiza. Iyo inati: ‘Anyamata oposa 1 miliyoni [ku United States] amaseŵera mpira m’sukulu za sekondale; pafupifupi 500,000 amaseŵera basketball; ndipo pafupifupi 400,000 amaseŵera baseball. Kuchokera kusukulu ya sekondale kufika kukoleji, chiŵerengero cha oseŵerawo chimatsika kwambiri. Amaseŵero onse amene amaseŵera mpira, basketball, ndi baseball pamakoleji ali pafupifupi 11,000 basi.’ Kuchoka pamenepo chiŵerengero chimatsikanso kowopsa. “Pafupifupi 8 peresenti [ya amaseŵero apakoleji] ndiwo okha amene amalembedwa m’matimu a akatswiri, ndipo pafupifupi 2 peresenti okha amasaina pangano laukatswiri.” Ndiyeno nkhaniyo ikupereka chikumbutso ichi: “Ngakhale kusainirana pangano sikumatanthauza kuti wamaseŵero adzakhala ndi malo m’timuyo.”

Motero, onse pamodzi, “pa amaseŵero 12,000 a sukulu za sekondale mmodzi chabe ndiye amakhala katswiri.” Zimenezo zangokhala ngati mwaŵi wa kupambana mphotho yoyamba ya lotale! Komabe, mungadzifunse kuti, kodi wamaseŵero sangalandire maphunziro apakoleji aulere kaamba ka kuyesayesa kwake konse? Kachiŵirinso, mwaŵi si waukulu kwambiri. Malinga ndi buku lakuti On the Mark, lolembedwa ndi Richard E. Lapchik ndi Robert Malekoff, “pakati pa mamiliyoni a amaseŵero akusukulu za sekondale . . . , mmodzi yekha mwa anthu 50 ndi amene amapatsidwa ndalama za maphunziro kuti aziseŵerera pakoleji.” Chiŵerengero china chomvetsa chisoni ndi ichi: “Pa amaseŵero a luso kwambiri amene amapatsidwa ndalama za maphunziro m’maseŵero a ndalama zambiri onga mpira ndi basketball, osakwanira 30 peresenti amamaliza maphuziro awo apakoleji patapita zaka zinayi.”

Kwa amaseŵero ambiri, lingaliro la kukhala wamaseŵero wotchuka ndi wachuma ndi loto chabe—zongocheza.

Olephera

Pamene muganizira za chiyembekezo cha kukhala ndi thanzi labwino, kuwongolera khalidwe, ndi kutchuka kwambiri, kuloŵa timu yamaseŵero yolinganizidwa kungaonekebe kukhala chinthu chanzeru kuchichita. Koma musanathamangire kumayeso ake, taganizirani zimene zinanenedwa mu Ladies’ Home Journal kuti: “Achichepere ambiri akudzilembetsa m’maseŵero olinganizidwa lerolino kuposa ndi mmene anachitira mumbadwo uliwonse wapita. Nkhani yoipa njakuti: Ziŵerengero zambiri koposa zikulephera m’maseŵero ameneŵa.” Dr. Vern Seefeldt, katswiri pankhani imeneyi, anati: ‘Pamene amafika zaka 15, 75 peresenti ya achichepere amene anaseŵerapo maseŵero alephera.’

Talingalirani za Canada, kumene maseŵero a ice hockey ali otchuka kwambiri. Mumpikisano umodzi wa ophunzira hockey, 53 peresenti ya oseŵera ake oposa 600,000 anali osafika pamsinkhu wazaka 12. Komabe, 11 peresenti okha anali oposa pamsinkhu wazaka 15. Chifukwa chake? Achichepere ambiri amasiya pamsinkhu umenewo. Kodi nchifukwa ninji ambiri amasiya?

Ofufuza amanena kuti olephera otero kaŵirikaŵiri amapereka chifukwa chosavuta kumva cha kusiya kwawo: Maseŵerowo samakhalanso osangalatsa. Zoonadi, kuseŵera m’timu kungakhale ntchito yotopetsa ndi yodya nthaŵi. Magazini a Seventeen anauza oŵerenga ake kuti kungochita mayeso oloŵa timu kungafune kugwira ntchito “maola atatu patsiku, masiku asanu pamlungu . . . pafupifupi kwa mlungu umodzi kapena milungu iŵiri.” Mutapambana mayeso amenewo ndi kuloŵa timu, maola enanso ambiri a kuyeseza ndi kulimbitsa thupi amakhala kutsogolo kwanu. Chitsanzo chabwino kwambiri ndi cha mtsikana wa m’timu ya basketball ya atsikana amene amathera maola oposa atatu patsiku kukonzekera maseŵero ake. Nthaŵi imeneyo ingatheredwe pakuchita zinthu zina zopindulitsa kwambiri.

Komabe, achichepere ambiri samadera nkhaŵa za programu yotopetsa imeneyo. Amasangalala ndi maseŵerowo ndi chitokoso cha kuwongolera maluso awo a maseŵero. Koma pali zifukwa zina zimene achichepere ambiri amalepherera maseŵero olinganizidwa. Muyenera kuzidziŵa zimenezo kuti musankhe kuloŵa timu kapena ayi. Monga mmene Miyambo 13:16 imanenera, “yense wochenjera amachita mwanzeru.” Motero nkhani yamtsogolo idzapitiriza nkhani imeneyi.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

‘Amaseŵero aluso kwambiri apayunivesite amene amalandira ndalama zamaphunziro chifukwa cha maseŵero amalephera kumaliza maphunziro awo’

[Chithunzi patsamba 13]

Kutchuka kwa amaseŵero kumakoka achichepere ambiri kuti aloŵe maseŵero olinganizidwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena