CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 17-19
Nkhondo ya Mulungu Idzathetsa Nkhondo Zonse
N’chifukwa chiyani Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachikondi ndi wamtendere” anauza Mwana wake yemwe ndi “Kalonga Wamtendere” kuti adzamenye nkhondo?—2 Akor. 13:11; Yes. 9:6.
Yehova ndi Yesu amakonda chilungamo ndipo amadana ndi zoipa
Mtendere weniweni ndi chilungamo zidzakhalapo anthu oipa akadzawonongedwa
Gulu lankhondo la Mulungu ‘lidzamenya nkhondo mwachilungamo,’ ndipo zimenezi zikuonekera chifukwa omenya nkhondowo akwera mahatchi oyera komanso avala zovala zoyera
Kodi tingatani kuti tidzapulumuke pa nkhondo yofunikayi?—Zef. 2:3