CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 48-50
Achikulire Angatiphunzitse Zambiri
Achikulire amalimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova komanso zimene anatilonjeza, akamatiuza ‘ntchito zodabwitsa’ zimene aona Yehovayo akuchita m’masiku otsiriza ano. (Sal. 71:17, 18) Ngati muli ndi mwayi wokhala ndi achikulire mumpingo wanu, afunseni
mmene Yehova wawathandizira kuthana ndi mavuto omwe akhala akukumana nawo pomutumikira
mmene amamvera akaona kuwonjezereka kwa olalikira Ufumu
mmene amasangalalira akaona momwe gulu lathu likufotokozera choonadi cha m’Baibulo momveka bwino masiku ano
zokhudza kusintha kumene aona kukuchitika m’gulu la Yehova