MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zimene Tingaphunzire kwa Akhristu Omwe Atumikira kwa Nthawi Yaitali
M’mipingo yathu tili ndi abale ndi alongo omwe akhala akutumikira Yehova kwa zaka zambiri. Tingaphunzirepo kanthu tikaona mmene asonyezera kudalira Yehova. Tikhoza kuwafunsa zokhudza mbiri ya gulu la Yehova komanso mavuto amene akhala akukumana nawo, ndiponso mmene Yehova wawathandizira kupirira mavutowo. Tikhozanso kuwaitana kuti adzakhale nafe pa Kulambira kwa Pabanja n’cholinga choti adzatifotokozere zimene akhala akukumana nazo pamoyo wawo.
Ngati mwatumikira Yehova kwa nthawi yaitali, muzikhala womasuka kufotokozera achinyamata zomwe mwakumana nazo pa moyo wanu. Yakobo ndi Yosefe ankafotokozera ana awo zimene anakumana nazo pamoyo wawo. (Gen. 48:21, 22; 50:24, 25) Ndipo kenako Yehova anauza mitu ya mabanja kuti iziphunzitsa ana awo zokhudza ntchito zake zazikulu. (Deut. 4:9, 10; Sal. 78:4-7) Masiku anonso, makolo komanso anthu ena mumpingo akhoza kufotokozera achinyamata zinthu zosangalatsa zimene aona Yehova akuchita pogwiritsa ntchito gulu lake.
ONERANI VIDIYO YAKUTI KUKHALABE OGWIRIZANA PANTHAWI IMENE NTCHITO YATHU INALI YOLETSEDWA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi ofesi ya nthambi ya ku Austria inathandiza bwanji abale a m’mayiko amene ntchito yathu inali yoletsedwa?
Kodi abale a m’mayikowa anachita zotani kuti chikhulupiriro chawo chikhalebe cholimba?
N’chifukwa chiyani ofalitsa ambiri a ku Romania anachoka m’gulu la Yehova, nanga anabwerera bwanji?
Kodi zimene abalewa anakumana nazo zalimbitsa bwanji chikhulupiriro chanu?
Akhristu omwe atumikira kwa nthawi yaitali angakulimbikitseni mwauzimu