June 22-28
EKISODO 1–3
Nyimbo Na. 7 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala”: (10 min.)
[Onerani vidiyo ya Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Ekisodo.]
Eks. 3:13—Mose ankafuna kudziwa tanthauzo la dzina la Yehova komanso kuti iye ndi ndani kwenikweni (w13 3/15 25 ¶4)
Eks. 3:14—Yehova amakhala chilichonse chomwe chingafunikire kuti akwaniritse cholinga chake (kr 43, bokosi)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Eks. 2:10—N’chifukwa chiyani tinganene kuti mwana wamkazi wa Farao ndi amene anatenga Mose n’kumamulera? (g04 4/8 22 ¶2)
Eks. 3:1—Kodi Yetero anali wansembe wotani? (w04 3/15 24 ¶4)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Eks. 2:11-25 (th phunziro 11)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 16)
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. Kenako gawirani magazini ya posachedwapa imene ili ndi nkhani yomwe mwininyumba anayambitsa. (th phunziro 12)
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w02 6/15 11 ¶1-4—Mutu: Chinthu Choposa Chuma cha Aigupto. (th phunziro 13)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Khalani Bwenzi La Yehova—Dzina la Yehova: (6 min.)
Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako itanani ana amene munawasankhiratu kuti abwere kutsogolo ndipo muwafunse mafunso otsatirawa: Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauza chiyani? Kodi Yehova analenga chiyani? Kodi Yehova angakuthandizeni bwanji?
Dzina la Mulungu Linakwezedwa ku Scandinavia: (9 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: N’chifukwa chiyani anthu ochepa okha ndi amene ankadziwa dzina la Mulungu zisanafike zaka za m’ma 1500? Kodi dzina la Yehova linayamba bwanji kugwiritsidwa ntchito ku Scandinavia? N’chifukwa chiyani mumaona kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika ndi lamtengo wapatali?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 88 ndime 12-19
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
• Nyimbo Na. 49 ndi Pemphero