APRIL 1-7
MASALIMO 23-25
Nyimbo Na. 4 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. “Yehova Ndi Mʼbusa Wanga”
(10 min.)
Yehova amatitsogolera (Sl 23:1-3; w11 5/1 31 ¶3)
Yehova amatiteteza (Sl 23:4; w11 5/1 31 ¶4)
Yehova amatidyetsa (Sl 23:5; w11 5/1 31 ¶5)
Yehova amasamalira atumiki ake mofanana ndi mmene m’busa watcheru amasamalira nkhosa zake.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi Yehova amandisamalira bwanji ineyo?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Sl 23:3—Kodi ‘njira zachilungamo’ ndi chiyani, nanga n’chiyani chingatithandize kuti tisasiye kuyendamo? (w11 2/15 24 ¶1-3)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 23:1–24:10 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Fotokozani lemba lolimbikitsa la m’Baibulo kwa munthu amene wakuuzani kuti akuda nkhawa ndi kuwonongeka kwa chilengedwe. (lmd phunziro 2 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Sonyezani mmene phunziro la Baibulo limachitikira kwa munthu amene analandira kabuku ka Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. (lmd phunziro 9 mfundo 3)
6. Kuphunzitsa Anthu
(5 min.) lff phunziro 14 mfundo 4 (lmd phunziro 11 mfundo 3)
Nyimbo Na. 54
7. Timakana Mawu a Alendo
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Nkhosa zimadziwa mawu a m’busa wawo ndipo zimamutsatira. Koma zikamva mawu a mlendo yemwe sizimudziwa, zimathawa. (Yoh 10:5) Mofanana ndi zimenezi, ifenso timamvera mawu a Abusa athu auzimu Yehova ndi Yesu, omwe ndi achikondi komanso odalirika. (Sl 23:1; Yoh 10:11) Koma timakana mawu a alendo amene amafuna kufooketsa chikhulupiriro chathu pogwiritsa ntchito “mawu achinyengo.”—2Pe 2:1, 3.
Chaputala 3 cha buku la Genesis, chimafotokoza nthawi yoyamba imene mawu a mlendo anamveka padziko lapansi. Satana anaonekera kwa Hava ndipo anadzisintha kuti asadziwike kuti ndi iyeyo amene akulankhula. Iye ananamizira kukhala mnzake, ndipo ananena zabodza zokhudza mawu komanso zolinga za Yehova. N’zomvetsa chisoni kuti Hava anamvetsera ndipo zimenezi zinabweretsa mavuto aakulu kwa iyeyo ndi anthu onse a m’banja lake.
Masiku ano, Satana amatichititsa kuti tizikayikira Yehova ndi gulu lake pofalitsa nkhani zabodza komanso zoipa. Tikamva mawu a alendo, tizithawa. Kumvetsera, ngakhale kwa kanthawi kochepa chifukwa choti tili ndi chidwi, n’koopsa kwambiri. Kodi Satana analankhula mawu angati kuti apusitse Hava pamene ankalankhula naye? (Ge 3:1, 4, 5) Nanga bwanji ngati munthu amene timamudziwa, yemwe amatikonda komanso ali ndi zolinga zabwino, akufuna kutiuza zinthu zoipa zokhudza gulu la Yehova?
Onerani VIDIYO yakuti Muzikana “Mawu a Alendo.” Kenako funsani omvera funso lotsatirali:
Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa mmene Jane anachitira zinthu ndi mayi ake omwe si a Mboni?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 8 ¶1-4, bokosi patsamba 61-62