APRIL 8-14
MASALIMO 26-28
Nyimbo Na. 34 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Zomwe Davide Anachita Kuti Akhalebe Wokhulupirika kwa Yehova
(10 min.)
Davide anapempha Yehova kuti amuyenge (Sl 26:1, 2; w04 12/1 14 ¶8-9)
Davide sankacheza ndi anthu oipa (Sl 26:4, 5; w04 12/1 15 ¶12-13)
Davide ankakonda kulambira Yehova (Sl 26:8; w04 12/1 16 ¶17-18)
Ngakhale kuti Davide ankalakwitsa zinthu zina, iye “anali ndi mtima wokhulupirika.” (1Mf 9:4) Anthu onse ankaona kuti Davide anali wokhulupirika chifukwa ankakonda komanso kutumikira Yehova ndi mtima wonse.
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Sl 27:10—Kodi lembali lingatilimbikitse bwanji pamene tikumva kuti anzathu atisiya tokha? (w06 7/15 28 ¶15)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 27:1-14 (th phunziro 2)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwiritsani ntchito kapepala kopezeka pa Zinthu Zophunzitsira. (th phunziro 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani funso lomwe lili kuseri kwa kapepala komwe munamusiyira pa ulendo woyamba. Muuzeni za webusaiti ya jw.org ndipo musonyezeni zina mwa zinthu zomwe zimapezekapo. (lmd phunziro 9 mfundo 3)
6. Nkhani
(5 min.) lmd zakumapeto A mfundo 3—Mutu: Chilengedwe Chidzabwereranso Mwakale. (th phunziro 13)
Nyimbo Na. 128
7. Achinyamata Amene Akuyesetsa Kukhalabe Okhulupirika
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Achinyamata a Chikhristu amafunika kuyesetsa kuti akhalebe okhulupirika. Chifukwa choti ndi opanda ungwiro, iwo amafunika kuyesetsa kuti akhalebe oyera pamene ali pachimake pa unyamata, nthawi imene chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu ndipo akhoza kuvutika kusankha bwino zinthu. (Aro 7:21; 1Ak 7:36) Nthawi zonse amafunikanso kukhala olimba kuti anzawo asawakakamize kuchita zachiwerewere, komanso kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo. (Aef 2:2) Achinyamata amene amayesetsa kukhalabe okhulupirika, timawanyadira kwambiri.
Onerani VIDIYO yakuti Moyo Wanga Wachinyamata—Ndingatani Ngati Anzanga Akundikakamiza Kuti Ndichite Zachiwerewere? Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa:
Kodi Cory ndi Kamryn ankakakamizidwa kuchita chiyani ndi anzawo?
Kodi n’chiyani chinawathandiza kukhalabe okhulupirika?
Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingakuthandizeni ngati mwakumana ndi zinthu zofanana ndi zimenezi?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 8 ¶5-12