Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 July tsamba 10-11
  • August 5-11

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • August 5-11
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 July tsamba 10-11

AUGUST 5-11

MASALIMO 70-72

Nyimbo Na. 59 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. ‘Uzani M’badwo Wotsatira’ za Mphamvu za Mulungu

(10 min.)

Davide ali mnyamata anaona Yehova akumuteteza (Sl 71:5; w99 9/1 18 ¶17)

Davide anaona kuti Yehova ankamuthandiza pamene anakalamba (Sl 71:9; g04 10/8 17 ¶3)

Davide analimbikitsa achinyamata powafotokozera zimene zinamuchitikira (Sl 71:17, 18; w14 1/15 23 ¶4-5)

Banja lomwe linali m’chithunzi cha nkhani ya mlungu wapita yamutu wakuti “Mfundo Zofunika pa Nthawi ya Kulambira kwa Pabanja.” Aitana banja lachikulire kuti lidzakhale nawo pa kulambira kwa pabanja ndipo likumvetsera mosangalala pamene banjalo likuwafotokozera zimene zawachitikira pa moyo wawo komanso kuwaonetsa zithunzi.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Pa nthawi ya kulambira kwa pabanja, kodi ndingacheze ndi m’bale kapena mlongo uti mu mpingo wathu amene watumikira Yehova kwa nthawi yaitali?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 72:8—Kodi zimene Yehova analonjeza Abulahamu pa Genesis 15:18 zinakwaniritsidwa bwanji pa nthawi imene Mfumu Solomo inkalamulira? (it-1 768)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 71:1-24 (th phunziro 5)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Siyani mwamtendere kukambirana ndi munthu amene wayamba kukangana nanu. (lmd phunziro 4 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pitirizani kukambirana ndi wachibale amene amazengereza kuphunzira Baibulo. (lmd phunziro 8 mfundo 4)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(5 min.) Nkhani. ijwfq 49​—Mutu: N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Anasintha Zinthu Zina Zomwe Ankakhulupirira? (th phunziro 17)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 76

7. Zomwe Mungachite pa Kulambira kwa Pabanja

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Banja lomwe lija laimirira ndipo likuimba nyimbo za Ufumu.
Banja lomwe lija likuonera pulogalamu ya JW Broadcasting.
Mwana wamkazi wa m’banjali akulankhula ndi mayi ake pa kulambira kwa pabanja pamene akuyeserera zimene angayankhe anzake kusukulu.

Nthawi ya Kulambira kwa Pabanja ndi yofunika kwambiri kuti ana ‘apatsidwe malangizo komanso aphunzitsidwe mogwirizana ndi zimene Yehova amanena.’ (Aef 6:4) Kuphunzitsa ana ndi ntchito yaikulu, koma kukhoza kukhala kosangalatsa makamaka ngati ana akufuna kudziwa zambiri zokhudza choonadi cha m’Baibulo. (Yoh 6:27; 1Pe 2:2) Kambiranani bokosi lakuti “Zimene Mungakambirane pa Kulambira kwa Pabanja,” lomwe lili ndi mfundo zomwe zingathandize makolo kudziwa zimene angachite kuti Kulambira kwa Pabanja kuzikhala kothandiza komanso kosangalatsa, kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  • Kodi mungakonde kugwiritsa ntchito zinthu ziti?

  • Kodi pali zinanso zimene mwaona kuti ndi zothandiza?

ZIMENE MUNGAKAMBIRANE PA KULAMBIRA KWA PABANJA

BAIBULO:

  • Pogwiritsa ntchito Baibulo lojambulidwa, tsatirani kuwerenga Baibulo kwa mlungu umenewo kapena werengani mosinthanasinthana. Aliyense akhoza kumawerenga pa malo a munthu winawake wotchulidwa m’Baibulo

  • Konzani mafunso kuchokera pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu umenewo. Aliyense wa m’banjamo akhoza kusankha funso, kukafufuza, kenako n’kufotokoza zimene akuphunzirapo

  • Funsani funso kapena yerekezerani zochitika zinazake kenako fufuzani mfundo za m’Baibulo zimene mungagwiritse ntchito kuchokera m’buku lakuti Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu

  • Chitani sewero la kachigawo kenakake ka nkhani ya m’Baibulo

  • Mlungu uliwonse lembani vesi la m’Baibulo pakakhadi, monga lopezeka mu Zakumapeto A m’kabuku ka Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa, kenako lowezani vesilo. Muzikambirana makadi amene munalemba mlungu wapita

  • Muzikambirana mbali ina ya m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale

  • Muziuza aliyense m’banja lanu kuti apereke lipoti kuchokera pa zimene anawerenga munkhani za mutu wakuti “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” kapena “Kufotokoza Mavesi a M’Baibulo” zomwe zimapezeka pansi pa mutu wakuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA pa jw.org

MISONKHANO:

  • Muzikonzekera mbali inayake ya msonkhano wa mpingo

  • Muzikonzekera komanso kuyeserera ndemanga. Muzionanso ngati ndemangazo sizikudya nthawi

  • Muziimba nyimbo za Ufumu

  • Muzikambirana komanso kuyeserera zimene munganene kuti mulimbikitse munthu wina misonkhano isanayambe kapena itatha

  • Muziyeserera nkhani ya ophunzira imene wina m’banja lanu wapatsidwa

UTUMIKI:

  • Muzikonzekera utumiki wa kunyumba ndi nyumba

  • Muzikonzekera mmene mungapangire maulendo obwereza

  • Yerekezerani kuti mwapeza mpata wochita ulaliki wa mwamwayi, kenako yesererani mmene mungayambire kulankhulana mwachibadwa

  • Muzikambirana zolinga zimene mungakhale nazo kuti muwonjezere utumiki wanu pa nyengo ya Chikumbutso kapena pamene muli pa holide kuntchito kapena ku sukulu

ZIMENE BANJA LANU LIKUFUNIKIRA:

  • Yesererani zimene mungachite ngati pachitika zinazake, kapena ngati mukuona kuti zinazake zikhoza kuchitika, mwachitsanzo nkhani yokhudza kusatenga mbali pa ndale, kuvutitsidwa ndi ena kusukulu, zibwenzi kapena kuchita maholide enaake

  • Yesererani kukambirana nkhani inayake ndipo makolo ndi ana azisinthana maudindo. Anawo afufuze nkhaniyo kenako akambirane ndi makolo omwe ayerekezera kukhala ana

MFUNDO ZOWONJEZERA

  • Onerani ndi kukambirana pulogalamu ya JW Broadcasting®

  • Werengani nkhani kapena onerani vidiyo ya pa jw.org kenako kambiranani

  • Werengani nkhani kapena onerani vidiyo yopezeka pa gawo lakuti “Achinyamata” kapena “Ana” zomwe zimapezeka pansi pa mutu wakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa pa jw.org

  • Kambiranani notsi zimene munalemba pa msonkhano wachigawo kapena wadera

  • Onani kapena fufuzani chinachake cha m’chilengedwe kenako kambiranani zimene tikuphunzirapo zokhudza Yehova

  • Nthawi ndi nthawi muziitana munthu wina kuti adzakhale nanu pa Kulambira kwa Pabanja kuti mucheze naye

  • Muzikambirana zolinga zauzimu zimene mungakhale nazo komanso zimene mungachite kuti muzikwaniritse

  • Muzichitira limodzi zinthu zinazake, mwachitsanzo kupanga chinthu chinachake chotchulidwa m’Baibulo, kujambula mapu kapena kulemba tchati

Onerani VIDIYO yakuti Muzipeza Njira Zatsopano Zochitira Kulambira kwa Pabanja. Kenako funsani funso ili:

  • Kodi mwamuna angatani kuti mkazi wake azisangalala ndi kulambira kwa pabanja ngati pakhomopo palibe ana?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 13 ¶17-24

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 123 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena