Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 September tsamba 14-15
  • October 28–November 3

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • October 28–November 3
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 September tsamba 14-15

OCTOBER 28–NOVEMBER 3

MASALIMO 103-104

Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Amakumbukira Kuti Ndife Fumbi”

(10 min.)

Chifundo chachikulu cha Yehova chimamuchititsa kukhala wololera (Sl 103:8; w23.07 21 ¶5)

Iye satitaya tikalakwitsa zinazake (Sl 103:​9, 10; w23.09 6-7 ¶16-18)

Sayembekezera kuti tizichita zimene sitingathe (Sl 103:14; w23.05 26 ¶2)

Mwamuna akumvetsera mwatcheru pamene mkazi wake akumufotokozera mmene akumvera.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi zimene ndimachitira anthu ena zimasonyeza kuti ndine wololera mofanana ndi Yehova?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 104:24—Kodi vesili likutiphunzitsa chiyani zokhudza luso la Yehova lolenga zinthu? (cl 55 ¶18)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 104:​1-24 (th phunziro 11)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. (lmd phunziro 3 mfundo 4)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani vidiyo yakuti Sangalalani Pophunzira Baibulo ndi munthu amene anavomera kuphunzira Baibulo. (th phunziro 9)

6. Nkhani

(5 min.) lmd zakumapeto A mfundo 6—Mutu: Mwamuna Ayenera ‘Kukonda Mkazi Wake Ngati Mmene Amadzikondera Yekha.’ (th phunziro 1)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 44

7. Kodi Mumadziwa Zimene Simungakwanitse Kuchita?

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Yehova amasangalala tikamachita zonse zomwe tingathe pomutumikira, komanso ifeyo timasangalala. (Sl 73:28) Komabe ndi bwino kuti tikamachita zonse zomwe tingathe, tiziganiziranso zomwe sitingakwanitse kuchita. Zimenezi zingatithandize kuti tisamakhale ndi nkhawa komanso tisamakhumudwe.

Mlongo wa muvidiyo yakuti “Tingachite Zambiri Potumikira Yehova Tikamachita Zomwe Tingakwanitse.”

Onerani VIDIYO yakuti Tingachite Zambiri Potumikira Yehova Tikamachita Zomwe Tingakwanitse. Kenako funsani mafunso awa:

  • Kodi Yehova amayembekezera kuti tizichita chiyani? (Mik 6:8)

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Tingachite Zambiri Potumikira Yehova Tikamachita Zomwe Tingakwanitse.” Mlongo wachitsikana ali limodzi ndi mnzake pa lesitilanti ndipo akulimbikitsa munthu amene amaphunzira naye Baibulo.
  • N’chiyani chinathandiza mlongoyu kuti asamadere nkhawa kwambiri za mmene angakwaniritsire cholinga chake?

KODI TINGADZIWE BWANJI ZIMENE SITINGAKWANITSE KUCHITA?

  • Musamadziyerekezere ndi ena. (Aga 6:4) Musamachite kapena kuganiza kuti mukhoza kukwanitsa kuchita zinazake potengera zimene ena akuchita. Mukhoza kuchita zambiri kapena zochepa kuposa munthu amene mumafanana naye zaka kapena amene mumafanana naye maudindo a banja

  • Musamangochita zinthu zimene munazolowera. (Aro 12:1; 1Ak 7:31) Musamaope kuchita utumiki umene poyamba mungauone ngati ndi wovuta kapena simungasangalale nawo.—Mki 3:10

  • Muzidziikira zolinga zosatenga nthawi pofuna kuona zimene mungakwanitse kuchita. Mwachitsanzo, kodi mungakwanitse kuchita upainiya wokhazikika? Kwa miyezi ingapo mwina mungawonjezere nthawi imene mumalalikira kapena kuchita upainiya wothandiza. Mukhozanso kuyesa kuchita upainiya wokhazikika kwa chaka chimodzi. Ngakhale mutaona kuti simungakwanitse kuchita upainiya wokhazikika, kapenanso patatha chaka mukuona kuti simungapitirize, nthawi zonse mudzakhala osangalala kudziwa kuti munakwaniritsa zolinga zing’onozing’ono zimene munadziikira.—Mla 6:9

  • Muzikhala okonzeka kusintha. Zinthu pa moyo wathu zimasintha, ndipo zomwe tingakwanitse kuchita zimasinthanso. Choncho nthawi ndi nthawi muzionanso zolinga zanu

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 17 ¶8-12, bokosi patsamba 137

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 55 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena