Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu
© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
SEPTEMBER 2-8
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 79-81
Muzikonda Dzina la Yehova Laulemerero
Dipo Ndi ‘Mphatso Yangwiro’ Yochokera kwa Atate
5 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda dzina la Yehova? Zochita zathu ndi zimene zingasonyeze. Paja Yehova amafuna kuti tikhale oyera. (Werengani 1 Petulo 1:15, 16.) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kulambira Yehova yekha komanso kumumvera ndi mtima wonse. Ngakhale tikamazunzidwa, tiziyesetsa kutsatira mfundo zake ndi malamulo ake. Tikamachita zinthu zabwino, timaonetsa kuwala kwathu ndipo dzina la Yehova limalemekezedwa. (Mat. 5:14-16) Tikamakhala oyera, timasonyeza kuti malamulo a Yehova ndi abwino ndipo zonena za Satana ndi zabodza. Koma tikachimwa, tiyenera kulapa mochokera pansi pa mtima ndipo tisamachitenso makhalidwe alionse amene anganyozetse dzina la Yehova.—Sal. 79:9.
ijwbv 3 ¶4-5
Aroma 10:13—“Adzaitana pa Dzina la Ambuye”
M’Baibulo, mawu oti ‘kuitana pa dzina la Yehova’ amatanthauza zambiri osati kungodziwa chabe dzina la Mulunguli n’kumaligwiritsa ntchito pomulambira. (Salimo 116:12-14) Koma amatanthauzanso kumukhulupirira ndiponso kumudalira kuti azitithandiza.—Salimo 20:7; 99:6.
Dzina la Mulungu linali lofunika kwambiri kwa Yesu Khristu. Paja mawu oyambirira a m’pemphero lake lachitsanzo anali akuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Yesu anasonyezanso kuti tiyenera kumudziwa Yehova, kumumvera komanso kumukonda kuti tidzapeze moyo wosatha.—Yohane 17:3, 6, 26.
Mfundo Zothandiza
it-2 111
Yosefe
Dzina la Yosefe Linkatchulidwatchulidwa. Potengera udindo waukulu womwe Yosefe anali nawo pakati pa ana Yakobo, zinali zoyenera kuti nthawi zina dzina lake lizigwiritsidwa ntchito ponena za mafuko onse a Isiraeli (Sl 80:1) kapena ponena za mafuko amene anapanga ufumu wakumpoto. (Sl 78:67; Am 5:6, 15; 6:6) Dzina lake limatchulidwanso m’maulosi a m’Baibulo. M’masomphenya aulosi a Ezekieli, cholowa chimene Yosefe anapatsidwa chinali zigawo ziwiri (Eze 47:13), geti limodzi la mzinda wotchedwa “Yehova Ali Kumeneko,” linali ndi dzina lakuti Yosefe (Eze 48:32, 35), ponena za kugwirizanitsa anthu a Yehova, Yosefe amatchulidwa kuti ndi mtsogoleri wa gulu limodzi la mtunduwo, ndipo Yuda ndi mtsogoleri wa gulu linalo. (Eze 37:15-26) Ulosi wa Obadiya unasonyeza kuti anthu “a m’banja la Yosefe” adzawononga nawo anthu “a m’banja la Esau” (Ob 18), komanso Zekariya ananena kuti Yehova adzapulumutsa “nyumba ya Yosefe.” (Zek 10:6) Potchula za mafuko auzimu a Isiraeli, dzina la Yosefe ndi lomwe limatchulidwa m’malo mwa Efuraimu.—Chv 7:8.
Mfundo yakuti dzina la Yosefe likutchulidwa pa Chivumbulutso 7:8, ikusonyeza kuti ulosi umene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira unakwaniritsidwanso pa Isiraeli wauzimu. Choncho n’zochititsa chidwi kuti Wamphamvu wa Yakobo, yemwe ndi Yehova Mulungu, anatumiza Khristu Yesu monga M’busa wabwino yemwe anapereka moyo wake “chifukwa cha nkhosa.” (Yoh 10:11-16) Komanso Khristu Yesu ndi mwala wapakona wa maziko, pamene kachisi wa Mulungu yemwe akupangidwa ndi Isiraeli wauzimu anamangidwapo. (Aef 2:20-22; 1Pe 2:4-6) M’busayu yemwenso ndi Mwala ali ndi Mulungu Wamphamvuyonse.—Yoh 1:1-3; Mac 7:56; Ahe 10:12; yerekezerani ndi Ge 49:24, 25.
SEPTEMBER 9-15
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 82-84
Muziyamikira Mwayi wa Utumiki Umene Muli Nawo
Zimene Tingaphunzire kwa Mbalame
Anthu okhala ku Yerusalemu ankadziwa bwino za anamzeze omwe amakonda kumanga zisa zawo kudenga la nyumba. Anamzeze ena ankamanga zisa kudenga la kachisi wa Solomo. Anamzezewa ayenera kuti ankaona kuti ndi malo amene anapiye awo angakhale motetezeka.
Mmodzi mwa ana a Kora, yemwe analemba Salimo 84, ankatumikira kukachisi mlungu umodzi pa miyezi 6 iliyonse ndipo ankaona zisa zimene anamzeze ankamanga kukachisiko. Iye ankafunitsitsa kuti akhale kunyumba ya Yehova nthawi zonse ngati mmene anamzezewa ankachitira. Iye anati: “Inu Yehova wa makamu, ine ndimakondadi chihema chanu chachikulu! Ndimalakalaka mabwalo a Yehova ndipo ndafookeratu chifukwa cholakalaka mabwalowo. Mtima wanga ndi thupi langa zikufuula mosangalala kwa Mulungu wamoyo. Inu Yehova wa makamu, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, ngakhale mbalame zapeza malo okhala pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu. Namzeze wadzimangira chisa chake pamenepo, ndi kuikamo ana ake!” (Salimo 84:1-3) Kodi nafenso limodzi ndi ana athu timasonyeza kuti ndife ofunitsitsa kukhala mumpingo wa anthu a Mulungu nthawi zonse?—Salimo 26:8, 12.
Musadzipanikize, Ndipo Mudzakhala Achimwemwe
Tingakhale ndi malire pa zimene tingachite potumikira Yehova chifukwa cha ukalamba kapena matenda. Ngati ndinu kholo, mungaone ngati simukupindula ndi phunziro laumwini kapena misonkhano yachikhristu chifukwa mumathera nthawi ndi mphamvu zanu mukusamalira ana. Komabe kodi n’kutheka kuti nthawi zina mumalephera kuona zimene mungakwanitse chifukwa chongoganizira kuti ndinu wolephera?
Kale, zaka zikwi zambiri zapitazo, Mlevi wina anakhumba zinthu zomwe sizikanatheka. Iye anali ndi mwayi wotumikira pa kachisi milungu iwiri pachaka. Komabe, anafuna kuti azikhala pafupi ndi guwa la nsembe moyo wake wonse, ndipo zimenezo zinali zotamandika. (Sal. 84:1-3) Kodi n’chiyani chinathandiza munthu wokhulupirikayu kukhutira ndi mwayi umene anali nawo? Anazindikira kuti kukhala m’mabwalo a kachisi ngakhale tsiku limodzi ndi mwayi wapadera kwambiri. (Sal. 84:4, 5, 10) Ifenso, m’malo mongoganizira zimene sitingathe kuchita, tizizindikira ndiponso kuyamikira zinthu zimene tingathe kuchita.
Yehova Amaona Kuti Ndinu Amtengo Wapatali
12 Ngati mukuvutika ndi matenda enaake, dziwani kuti Yehova amamvetsa mavuto anu. Choncho muzimupempha kuti azikuthandizani kukhala ndi maganizo oyenera. Muziwerenganso mawu abwino amene Yehova wakusungirani m’Baibulo. Muziganizira kwambiri malemba amene amasonyeza kuti Yehova amakonda atumiki ake. Mukamachita zimenezi, mudzaona kuti Yehova amakomera mtima anthu onse amene amamutumikira mokhulupirika.—Sal. 84:11.
Mfundo Zothandiza
it-1 816
Mwana Wamasiye
Popeza zinali zosavuta kuiwala anthu omwe aferedwa kapena omwe analibe owateteza, Yehova anagwiritsa ntchito mawu akuti “mwana wamasiye” pofotokoza zimene zinkachitika aisiraeli akakhala okhulupirira kapena akasiya kukhala okhulupirira. Pa nthawi imene mtunduwu unali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, mwana wamasiye ankasamalidwa bwino. Koma anthuwo akasiya kuchita zinthu mwachilungamo, mwana wamasiye ankanyalanyazidwa ndipo zimenezi zinkasonyeza kuti mtunduwo suli pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Sl 82:3; 94:6; Yes 1:17, 23; Yer 7:5-7; 22:3; Eze 22:7; Zek 7:9-11; Mki 3:5) Anthu amene ankachitira nkhanza mwana wamasiye ankakhala otembereredwa. (De 27:19; Yes 10:1, 2) Yehova amanena yekha kuti iye ndi amene amawateteza (Miy 23:10, 11), amawathandiza (Sl 10:14; Sl 146:9), ndi Bambo wawo (Sl 68:5), amawachitira zinthu mwachilungamo (De 10:17, 18), amawachitira chifundo (Ho 14:3) komanso amawasiya amoyo.—Yer 49:11.
Chimodzi mwa zinthu zimene zimadziwikitsa Akhristu oona ndi kusamalira anthu amene mwamuna kapena makolo awo anamwalira. Yakobo analembera Akhristu anzake kuti: “Kulambira koyera komanso kosadetsedwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye amene akukumana ndi mavuto komanso kupewa kuti dzikoli likuchititseni kukhala ndi banga.”—Yak 1:27.
SEPTEMBER 16-22
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 85-87
Pemphero Limatithandiza Kupirira
Kodi Mukuonetsa Ulemerero wa Yehova?
10 ‘Kulimbikira kupemphera’ kungatithandizenso kuonetsa ulemerero wa Mulungu. (Aroma 12:12) Tifunika kupemphera kwa Yehova kuti atithandize kumutumikira m’njira yoyenera. Tiyenera kumupempha kuti atipatse mzimu woyera, atithandize kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu, kulimbana ndi mayesero ndiponso kukhala ndi luso lotha “kufotokoza bwino mawu a choonadi.” (2 Tim. 2:15; Mat. 6:13; Luka 11:13; 17:5) Mofanana ndi mwana amene amadalira bambo wake, ifenso tiyenera kudalira Yehova yemwe ndi Atate wathu wakumwamba. Ngati titamupempha kuti atithandize kumutumikira bwino, tingakhulupirire kuti adzatithandizadi. Tisamaganize kuti mapemphero athu amamuvutitsa. Tikamapemphera tiyenera kumutamanda, kumuthokoza ndiponso kumupempha kuti atithandize, makamaka tikakhala pa mayesero. Tiyeneranso kumupempha kuti atithandize kumutumikira m’njira imene imalemekeza dzina lake loyera.—Sal. 86:12; Yak. 1:5-7.
Mmene Yehova Amayankhira Mapemphero Athu
17 Werengani Salimo 86:6, 7. Wolemba masalimo Davide ankakhulupirira kuti Yehova amva komanso kuyankha mapemphero ake. Inunso mungamakhulupirire zimenezi. Zitsanzo zomwe takambirana munkhaniyi, zikutitsimikizira kuti Yehova angatipatse nzeru komanso mphamvu zimene timafunikira kuti tipirire. Iye angagwiritse ntchito abale ndi alongo kapenanso anthu omwe panopa sakumutumikira kuti atithandize mwanjira inayake..
18 Ngakhale kuti sinthawi zonse pamene Yehova angayankhe mapemphero athu m’njira imene timayembekezera, timadziwa kuti adzatiyankha. Iye adzatipatsa zenizeni zimene tikufunikira komanso pa nthawi yomwe zikufunikira. Choncho pitirizani kupemphera muli ndi chikhulupiriro choti Yehova azikusamalirani panopa komanso kuti ‘adzakhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse’ m’dziko latsopano lomwe likubwera.—Sal. 145:16.
Mfundo Zothandiza
it-1 1058 ¶5
Mtima
Kutumikira Ndi “Mtima Wonse.” Mtima weniweni umafunika kukhala wathunthu kuti uzigwira bwino ntchito, koma mtima wophiphiritsa ukhoza kukhala wogawanika. Davide anapemphera kuti: “Ndithandizeni kuti ndiziopa dzina lanu ndi mtima wonse,” kusonyeza kuti mtima wa munthu ukhoza kukhala wogawanika chifukwa cha zimene umakonda komanso kuopa. (Sl 86:11) Munthu wotereyu akhoza kukhala ndi ‘mitima iwiri’ kapenanso kukhala wofunda polambira Mulungu. (Sl 119:113; Chv 3:16) Akhoza kumatumikira ambuye awiri, kapena mwachinyengo kumanena zinthu zina pomwe akuganiza zinthu zina. (1Mb 12:33; Sl 12:2) Yesu anadzudzula mwamphamvu anthu achinyengo omwe amakhala ndi mitima iwiri.—Mt 15:7, 8.
SEPTEMBER 23-29
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 88-89
Ulamuliro wa Yehova Ndi Wabwino Kwambiri
Muzikhala Kumbali ya Ulamuliro wa Yehova
5 Chinthu china chimene chimachititsa kuti Yehova akhale woyenera kulamulira n’chakuti amalamulira mwachilungamo kwambiri. Iye anati: “Ine ndine Yehova, amene ndimasonyeza kukoma mtima kosatha, ndimapereka ziweruzo ndi kuchita chilungamo padziko lapansi. Pakuti zinthu zimenezi zimandisangalatsa.” (Yer. 9:24) Kuti achite zinthu mwachilungamo, Yehova sadalira malamulo amene anthu omwe si angwiro analemba. Iye ndi wachilungamo kale moti amadziwa yekha zoyenera kuchita ndipo ndi amene anapereka malamulo kwa anthu. Paja Baibulo limati: “Chilungamo ndi chiweruzo ndizo maziko a mpando [wake] wachifumu.” (Sal. 89:14; 119:128) Choncho sitiyenera kukayikira kuti malamulo ake, mfundo zake komanso zonse zimene amasankha ndi zachilungamo. Koma Satana, yemwe amanena kuti Yehova salamulira bwino, walephera kuthandiza kuti zinthu ziziyenda mwachilungamo m’dzikoli.
Muzikhala Kumbali ya Ulamuliro wa Yehova
10 Yehova salamulira mopondereza ndipo si womva zake zokha. Iye anapereka ufulu kwa anthu ndipo izi zimathandiza kuti anthu azisangalala. (2 Akor. 3:17) Pa nkhani imeneyi, Davide analemba kuti: “Ulemu ndi ulemerero zili pamaso pake [pa Mulungu], pokhala pake pali mphamvu ndi chimwemwe.” (1 Mbiri 16:7, 27) Nayenso Etani, amene analemba masalimo ena, anati: “Odala ndi anthu amene amafuula mosangalala. Iwo amayendabe m’kuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova. Iwo amakondwera ndi dzina lanu tsiku lonse. Chilungamo chanu chimawakweza.”—Sal. 89:15, 16.
11 Tikamaganizira zinthu zabwino zimene Yehova amachita timatsimikizira kuti ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Timakhala ndi maganizo a wamasalimo amene ananena kuti: “Kukhala tsiku limodzi m’mabwalo anu n’kwabwino kuposa kukhala masiku 1,000 kwina.” (Sal. 84:10) Maganizo amenewa ndi omveka chifukwa Yehova ndi amene anatilenga komanso amadziwa zimene zingatisangalatse ndipo amatipatsa zinthuzo mowolowa manja. Chilichonse chimene amatiuza kuti tichite chimakhala chotithandiza ndipo tikamvera timasangalala. Izi zimachitika ngakhale pamene tiyenera kudzimana zinthu zina kuti timumvere.—Werengani Yesaya 48:17.
Tizikhulupirira Kwambiri Ufumu wa Mulungu
14 Pangano lake ndi pangano la Davide. (Werengani 2 Samueli 7:12, 16.) Yehova anachita pangano ndi Davide pamene iye ankalamulira ku Yerusalemu ndipo anamulonjeza kuti Mesiya adzachokera m’banja lake. (Luka 1:30-33) Choncho Yehova anasonyeza kuti munthu wochokera m’banja la Davide adzakhala “woyenerera mwalamulo” kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. (Ezek. 21:25-27) Ufumu wa Davide “udzakhazikika mpaka kalekale” kudzera mwa Yesu. Pajanso Baibulo limanena kuti: “Mbewu yake [ya Davide] idzakhala mpaka kalekale, ndipo mpando wake wachifumu udzakhala ngati dzuwa.” (Sal. 89:34-37) Choncho pangano la Davide limatitsimikizira kuti Ufumu wa Mesiya sudzayamba kuchita zinthu mwachinyengo komanso zimene udzachite zidzathandiza anthu mpaka kalekale.
Mfundo Zothandiza
‘Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika’
4 M’Malemba a Chiheberi, mawu akuti “kukhulupirika,” amatanthauza kumamatira munthu amene umamukonda n’kumapitirizabe kumuthandiza. Munthu amachita zimenezi osati chifukwa chongoti n’zimene ayenera kuchita koma chifukwa cha chikondi. Choncho kukhala wokhulupirika n’kosiyana ndi kungokhala wodalirika. Mwachitsanzo, wolemba masalimo anati mwezi ndi “mboni yokhulupirika yamumlengalenga” chifukwa nthawi zonse umakhalapo. (Salimo 89:37) Choncho tinganene kuti mwezi ndi wokhulupirika, kapena kuti wodalirika. Koma sikuti mwezi umasonyeza kukhulupirika kofanana ndi kumene munthu amasonyeza. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa choti mwezi sungasonyeze chikondi.
5 Baibulo limasonyeza kuti munthu wokhulupirika amakhalanso wachikondi. Ndipotu munthu akakhala wokhulupirika kwa munthu wina, zimasonyeza kuti munthu winayo ndi mnzake. Munthu woteroyo amakhala wokhulupirika nthawi zonse ndipo sakhala ngati mafunde apanyanja amene amangokankhika ndi mphepo iliyonse. Munthu wokhulupirika, kapena kuti wachikondi chokhulupirika, samasintha zivute zitani.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
ijwbq 181
Kodi Baibulo N’chiyani?
Baibulo limayamba ndi kufotokoza mfundo zachidule zokhudza mmene Mulungu Wamphamvuyonse analengera kumwamba ndi dziko lapansi. Mulungu amatiuza dzina lake lakuti Yehova kudzera m’Baibulo ndipo amafuna kuti anthu onse amudziwe.—Salimo 83:18.
Baibulo limafotokoza kuti dzina la Mulungu linadetsedwa ndipo limafotokozanso zimene adzachite kuti aliyeretse.
Baibulo limatiuza cholinga chimene Mulungu analengera anthu komanso dzikoli. Limanena mmene Mulungu adzathetsere mavuto onse amene anthu akukumana nawo.
Baibulo lili ndi malangizo othandiza kuti tizikhala moyo wabwino. Mwachitsanzo, limatithandiza pa nkhani monga:
● Kukhala bwino ndi anzathu. “Choncho zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo. Zimenezi ndi zomwe Chilamulo chimafuna komanso zimene aneneri analemba.”—Mateyu 7:12.
Tanthauzo lake: Zimene timafuna kuti ena atichitire, ifenso tiziwachitira zomwezo.
● Kuthana ndi nkhawa. “Musamadere nkhawa za mawa, chifukwa mawalo lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”—Mateyu 6:34.
Tanthauzo lake: Tisamadandaule zokhudza mavuto omwe angadzachitike m’tsogolo, koma tizingothana ndi mavuto amene tikukumana nawo panopa basi.
● Kukhala ndi banja losangalala. “Aliyense wa inu azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.”—Aefeso 5:33.
Tanthauzo lake: Chikondi komanso ulemu ndi makhalidwe ofunika kwambiri kuti anthu okwatirana azikhala mosangalala.
SEPTEMBER 30–OCTOBER 6
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 90-91
Muzikhulupirira Yehova Kuti Mukhale ndi Moyo Wautali
Kufufuza Moyo Wautali
Sikuti asayansi onse amavomereza kuti njira zothandiza kuti munthu asakalambe zingachititse kuti munthu akhaledi ndi moyo wautali kuposa umene anthu amakhala nawo masiku ano. N’zoona kuti kuyambira m’zaka za m’ma 1800 anthu akumakhala ndi moyo wotalikirapo. Koma chifukwa chachikulu n’chakuti anthu akuyesetsa kukhala aukhondo, pali mankhwala ambiri othandiza komanso pali katemera woteteza kumatenda osiyanasiyana. Asayansi ena amaona kuti panopa anthu sakukhala ndi moyo waufupi kapena wautali kwambiri kuposa umene timayembekezera.
Zaka pafupifupi 3,500 zapitazo, Mose yemwe analemba nawo Baibulo, ananena kuti: “Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70, ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadera amakwana zaka 80. Koma ngakhale zili choncho, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka. Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timachoka mofulumira.” (Salimo 90:10) Ngakhale kuti anthu ayesetsa kwambiri kuti atalikitse zaka zimene timakhala ndi moyo, moyo wathu ndi waufupibe ngati mmene Mose ananenera.
Koma pali nyama zina zimene zimakhala ndi moyo zaka mahandiredi komanso mitengo ina imene imakhalako kwa zaka masauzande ambiri. Tikayerekeza zaka zimenezi ndi zaka zimene anthufe timakhala ndi moyo, mwina tingadzifunse kuti, ‘Kodi anthufe tinalengedwa kuti tizingokhala ndi moyo zaka 70 kapena 80 basi?
wp19.1 5, bokosi
Kodi Dzina la Mulungu Ndi Ndani?
Anthu ambiri akhala akudzifunsa funso limeneli. Mwina nanunso munadzifunsapo funsoli. Kapena tingafunse kuti: Ngati zinthu zonse zinachita kulengedwa, ndiye Mulungu amene anazilengayo anachokera kuti?
Asayansi ambiri amavomereza kuti chilengedwechi chili ndi chiyambi. Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, vesi lina la m’Baibulo limati: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1.
N’zosatheka kuti zinthu zimene timaonazi zinangokhalako zokha, popanda amene anazipanga. Pamalo oti palibepo chilichonse sipangayambike kanthu. Ndipo zikanakhala kuti poyambapo kunalibe aliyense, bwenzi panopa zinthu zonse za m’chilengedwechi kulibe. Ngakhale kuti ndi zovuta kumvetsa kwa anthufe, mfundo ndi yoti payenera kuti pali winawake yemwe wakhala alipo kuyambira kale, amene anachititsa kuti zinthu timaonazi zikhaleko. Ameneyu ndi Yehova Mulungu, yemwe ndi mzimu, ndi wamphamvuyonse komanso ndi wanzeru.—Yohane 4:24.
Ponena za Mulungu, Baibulo limati: “Mapiri asanabadwe, kapena musanakhazikitse dziko lapansi ndi malo okhalapo anthu, inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.” (Salimo 90:2) Choncho Mulungu wakhala alipo kuyambira kalekale. Ndipo kenako, “pa chiyambi,” analenga zinthu zonse zomwe zili m’chilengedwechi.—Chivumbulutso 4:11.
Kodi Chikondi Chingatithandize Bwanji Kuti Tisamachite Mantha?
16 Satana amadziwa kuti timaona kuti moyo wathu ndi wamtengo wapatali. Komabe iye amanena kuti tikhoza kulolera kutaya chilichonse ngakhale ubwenzi wathu ndi Yehova, n’cholinga choti titeteze moyo wathu. (Yobu 2:4, 5) Komatu iye amakhala akudzinamiza. Ngakhale zili choncho, popeza kuti iye “ali ndi njira yobweretsera imfa,” amayesa kugwiritsa ntchito mantha achibadwa omwe timakhala nawo pa nkhani ya imfa kuti atichititse kusamvera Yehova. (Aheb. 2:14, 15) Nthawi zina anthu amene amatsogoleredwa ndi Satana amatiopseza kuti atipha ngati sitisiya kukhulupirira Yehova. Pamene tikufunika thandizo lachipatala mwamsanga, nthawi zina Satana angapezerepo mwayi wotichititsa kusankha zinthu molakwika. Madokotala kapena achibale omwe si a Mboni angatikakamize kuti tivomere kuikidwa magazi zomwe zingachititse kuti tiphwanye malamulo a Mulungu. Kapenanso munthu wina angatilimbikitse kuti tipeze thandizo la mankhwala losemphana ndi mfundo za m’Malemba.
17 Ngakhale kuti sitifuna kufa, timadziwa kuti Yehova sadzasiya kutikonda ngakhale titamwalira. (Werengani Aroma 8:37-39.) Anzake a Yehova akamwalira, iye amawakumbukirabe ndipo zimangokhala ngati adakali ndi moyo. (Luka 20:37, 38) Amafunitsitsa kudzawaukitsa. (Yobu 14:15) Yehova anapereka malipiro okwera kwambiri n’cholinga choti ‘tidzapeze moyo wosatha.’ (Yoh. 3:16) Timadziwa kuti iye amatikonda kwambiri ndipo amatiganizira. Choncho m’malo mosiya Yehova tikakhala kuti tikudwala kapena tikhoza kufa, timamudalira kuti atilimbikitse, kutipatsa nzeru komanso kutipatsa mphamvu. Izi ndi zimene Valérie ndi mwamuna wake anachita.—Sal. 41:3.
Mfundo Zothandiza
Kodi Aliyense Ali Ndi Mngelo Amene Amamuyang’anira?
Baibulo silinena kuti munthu aliyense ali ndi mngelo wake amene amamuyang’anira. N’zoona kuti Yesu anati: “Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati, [ophunzira a Yesu] chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.” (Mateyu 18:10) Koma sikuti apa Yesu ankatanthauza kuti aliyense ali ndi mngelo amene amamuyang’anira. M’malomwake ankatanthauza kuti angelo amachita chidwi ndi wophunzira wa Yesu aliyense ndipo amafuna kuti zinthu zizimuyendera bwino. Choncho atumiki a Mulungu sachita dala zinthu zoika moyo pangozi poganiza kuti angelo a Mulungu awateteza.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti angelo sathandiza anthu? Ayi. (Salimo 91:11) Anthu ena amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu amawateteza komanso amawatsogolera pogwiritsa ntchito angelo. Mmodzi wa anthu amenewa ndi a Kenneth amene tawatchula m’nkhani yoyamba ija. N’kuthekadi kuti Mulungu ndi amene anathandiza a Kenneth. Nthawi zambiri a Mboni za Yehova amaona umboni wosonyeza kuti angelo amawathandiza pa ntchito yawo yolalikira. Komabe popeza angelo saoneka, sitingafotokoze mwatsatanetsatane zonse zimene amachita pothandiza anthu m’njira zosiyanasiyana. Koma sikulakwa ngati munthu akuthokoza Yehova chifukwa choti akuona kuti wamuthandiza pogwiritsa ntchito angelo.—Akolose 3:15; Yakobo 1:17, 18.
OCTOBER 7-13
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 92-95
Kutumikira Yehova Ndi Kwabwino Kwambiri
Achinyamata, Kodi Mukuyesetsa Kukwaniritsa Zolinga Zauzimu?
5 Chifukwa chachikulu chokhalira ndi zolinga zauzimu n’chakuti timafuna kusonyeza kuti timayamikira chikondi cha Yehova komanso zonse zimene watichitira. Pa nkhani imeneyi, wolemba masalimo ananena kuti: “Ndi bwino kuyamika inu Yehova . . . Pakuti mwandichititsa kusangalala, inu Yehova, chifukwa cha zochita zanu. Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito ya manja anu.” (Sal. 92:1, 4) Ngati ndinu wachinyamata, muyenera kuganizira zinthu zambirimbiri zimene Yehova wakupatsani. Mwachitsanzo, wakupatsani moyo, mfundo zimene mumakhulupirira, Baibulo, mpingo komanso chiyembekezo chabwino kwambiri. Munthu akamaika zinthu zauzimu pamalo oyamba amasonyeza kuti akuyamikira zinthu zonse zimene Mulungu watipatsa ndipo zimathandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba.
Kodi Mumayendera Maganizo a Ndani?
8 Yehova ali ngati kholo labwino chifukwa amafuna kuti ana akefe tikhale ndi moyo wabwino kwambiri. (Yes. 48:17, 18) Choncho amatiphunzitsa kuti tikhale ndi makhalidwe abwino komanso tiziganizira anzathu. Ndiye amafuna kuti tiziyendera maganizo ake pa nkhani imeneyi. Zimenezi sizitipanikiza ayi, koma zimangotithandiza kuti tikhale ndi maganizo abwino komanso apamwamba. (Sal. 92:5; Miy. 2:1-5; Yes. 55:9) Zimatithandiza kusankha zinthu zimene tingasangalale nazo koma pa nthawi imodzimodziyo tikugwiritsa ntchito ufulu wathu. (Sal. 1:2, 3) Kunena zoona, kuyendera maganizo a Yehova n’kwabwino komanso kothandiza.
Yehova Amaona Kuti Ndinu Amtengo Wapatali
18 Pamene tikukula, tisamakayikire kuti padakali zinthu zina zimene Yehova amafuna kuti tichite. (Sal. 92:12-15) Yesu anasonyeza kuti Yehova amayamikira zilizonse zimene tingachite pomutumikira ngakhale zitaoneka zochepa kwambiri. (Luka 21:2-4) Choncho muziganizira kwambiri zimene mungakwanitse kuchita. Mwachitsanzo, mukhoza kuuza anthu za Yehova, kupempherera abale anu komanso kulimbikitsa anthu ena kuti akhalebe okhulupirika. Yehova amaona kuti ndinu wantchito mnzake ngati muli ndi mtima womumvera osati chifukwa chochita zinthu zambiri pomutumikira.—1 Akor. 3:5-9.
Mfundo Zothandiza
‘Nzeru za Mulungu N’zozama’
18 Mtumwi Paulo anafotokoza kuti nzeru za Yehova ndi zapadera kwambiri. Iye anati: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zovuta kuzimvetsa, ndipo ndani angatulukire njira zake?” (Aroma 11:33) Poyamba ndi mawu akuti “ndithudi,” Paulo anasonyeza kuti anakhudzidwa kwambiri komanso anagoma ndi nzeru za Yehova. Mawu a Chigiriki amene anagwiritsa ntchito palembali omwe anawamasulira kuti “kuzama,” ndi ofanana kwambiri ndi mawu akuti “phompho.” Choncho zimene Paulo ananena zimatithandiza kuona m’maganizo zimene ankatanthauza. Tikamaganizira nzeru za Yehova, zimakhala ngati tikuyang’ana m’chidzenje chozama kwambiri chomwe pansi pake sitingathe kuonapo, chachikulu kwambiri moti sitingathe kudziwa bwino kukula kwake, ndiponso chokanika kuchifotokoza ngakhalenso kuchijambula bwinobwino. (Salimo 92:5) Kudziwa zimenezi kuyeneratu kutichititsa kuti tikhale odzichepetsa.
OCTOBER 14-20
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 96-99
“Muzilengeza Uthenga Wabwino”
Kodi Uthenga Wabwino N’chiyani?
AKHRISTU ayenera kumalalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ Ayeneranso kufotokozera ena kuti Ufumuwo ndi boma la m’tsogolo limene lidzalamulira dziko lonse lapansi mwachilungamo. Komabe m’Baibulo mawu akuti “uthenga wabwino” amagwiritsidwanso ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, m’Baibulo muli mawu ngati, “uthenga wabwino wa chipulumutso” (Salimo 96:2); “uthenga wabwino wa Mulungu” (Aroma 15:16); ndi “uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu.”—Maliko 1:1.
Mwachidule, uthenga wabwino ndi mfundo zonse za choonadi zimene Yesu ananena ndiponso zimene ophunzira ake analemba. Yesu asanapite kumwamba anauza otsatira ake kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.” (Mateyu 28:19, 20) Choncho ntchito ya Akhristu oona sikungouza anthu za Ufumu, koma ayeneranso kuyesetsa kuphunzitsa anthuwo kuti akhale ophunzira a Yesu.
Kodi pa Tsiku la Chiweruzo Padzachitika Zotani?
Monga tikuonera pachithunzi chili kumanjachi, anthu ambiri amaganiza kuti pa Tsiku la Chiweruzo anthu onse adzaonekera pampando wachifumu wa Mulungu ndipo adzaweruzidwa malinga ndi ntchito zimene anachita. Anthuwa amaganiza kuti ena adzalandira moyo kumwamba ndipo ena adzapita kukazunzidwa kumoto. Koma Baibulo limasonyeza kuti cholinga cha Tsiku la Chiweruzo ndi kupulumutsa anthu ku zinthu zopanda chilungamo zimene zimachitika padzikoli. (Salimo 96:13) Mulungu wasankha Yesu kukhala Woweruza wake amene adzabweretsa chilungamo kwa anthu.—Werengani Yesaya 11:1-5; Machitidwe 17:31.
Mtendere Udzayamba mu Ulamuliro wa Zaka 1,000
18 Ubwenzi umenewu unasokonekera pamene Satana anachititsa anthu kupandukira ulamuliro wa Yehova. Koma kuyambira mu 1914, Ufumu wa Mesiya wakhala ukubwezeretsa mtendere ndi mgwirizano. (Aef. 1:9, 10) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, zinthu zosangalatsa zimene tikuyembekezera zidzachitika. Ndiyeno n’chiyani chidzachitika “pa mapeto pake,” kapena kuti pa mapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000? Ngakhale kuti Yesu anapatsidwa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi,” iye alibe mtima wofuna kulanda udindo wa Yehova. Yesu ndi wodzichepetsa ndipo “adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake.” Iye adzagwiritsa ntchito udindo wake kuti ‘alemekeze Mulungu.’—Mat. 28:18; Afil. 2:9-11.
19 Pa nthawi imeneyo, anthu olamulidwa ndi Ufumu padziko lapansi adzakhala angwiro. Iwo adzatsatira chitsanzo cha Yesu. Adzagonjera ulamuliro wa Yehova modzichepetsa ndiponso mofunitsitsa. Iwo akadzapambana mayesero omaliza adzasonyeza kuti alidi ndi mtima wofuna kugonjera Yehova. (Chiv. 20:7-10) Pambuyo pake, adani onse a Mulungu, kungoyambira anthu, ziwanda komanso Satana weniweniyo, adzawonongedwa. Nthawi imeneyi idzakhala yosangalatsa kwambiri. Onse a m’banja la Yehova adzamutamanda mosangalala ndipo iye adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”—Werengani Salimo 99:1-3.
Mfundo Zothandiza
it-2 994
Nyimbo
Mawu onena za “nyimbo yatsopano” samangopezeka m’buku la Masalimo lokha koma amapezekanso m’mabuku olembedwa ndi Yesaya komanso mtumwi Yohane. (Sl 33:3; 40:3; 96:1; 98:1; 144:9; 149:1; Yes 42:10; Chv 5:9; 14:3) Tikaona bwinobwino nkhani zambiri zimene mukupezeka mawu akuti “nyimbo yatsopano,” zimasonyeza kuti nyimboyo inkaimbidwa chifukwa chakuti Yehova anasonyeza m’njira yatsopano ulamuliro wake monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 96:10 limanena mawu osangalatsa akuti: “Yehova wakhala Mfumu.” Zikuoneka kuti nkhani yaikulu imene ili mu “nyimbo yatsopano” imeneyi ndi zochitika zatsopano zokhudza mmene Yehova wasonyezera kuti ndi mfumu komanso kuti zimenezi zikutanthauza chiyani kumwamba ndi dziko lapansi.—Sl 96:11-13; 98:9; Yes 42:10, 13.
OCTOBER 21-27
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 100-102
Muziyamikira Chikondi Chokhulupirika cha Yehova
Mmene Mungakonzekerere Kubatizidwa
18 Kukonda Yehova ndi khalidwe lofunika kwambiri lomwe muyenera kukhala nalo. (Werengani Miyambo 3:3-6.) Kukonda kwambiri Mulungu kungatithandize kuti tizipirira mavuto amene timakumana nawo. Nthawi zambiri Baibulo limafotokoza mmene Yehova amasonyezera chikondi chokhulupirika kwa atumiki ake. Chikondichi ndi champhamvu kwambiri moti sichitha zivute zitani. (Sal. 100:5) Inuyo munalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Gen. 1:26) Ndiye kodi mungasonyeze bwanji chikondi ngati chimenechi?
19 Muziyamikira. (1 Ates. 5:18) Tsiku lililonse muzidzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amandikonda?’ Kenako muzionetsetsa kuti mukumuthokoza m’mapemphero anu ndipo muzitchula zenizeni zimene wakuchitirani. Muziona kuti chikondicho akusonyeza inuyo panokha, mofanana ndi mmenenso mtumwi Paulo ankaonera. (Werengani Agalatiya 2:20.) Dzifunseni kuti, ‘Kodi inenso ndikufuna kumusonyeza chikondi?’ Kukonda Yehova kudzakuthandizani kuti mupitirize kulimbana ndi mayesero komanso mavuto omwe mukukumana nawo. Chikondichi chidzakulimbikitsaninso kuti mupitirize kumachita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse, n’kumasonyeza kuti mumakonda Atate wanu tsiku ndi tsiku.
“Khalanibe Oganiza Bwino Ndipo Khalani Maso”
10 Zinthu zina zimene tiyenera kupewa ndi monga kukopana, kuledzera, kudya kwambiri, kulankhula mawu omwe angakhumudwitse ena komanso kuonera zosangalatsa zachiwawa, zolaula ndi zinthu zina zotere. (Sal. 101:3) Mdani wathu Mdyerekezi nthawi zonse amafunafuna mipata yoti awononge ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Pet. 5:8) Ngati sitingakhale maso, Satana angadzale m’mitima mwathu mbewu za nsanje, chinyengo, dyera, chidani, kudzikuza komanso mkwiyo. (Agal. 5:19-21) Poyamba zinthu zimenezi zingaoneke ngati zosaopsa. Koma ngati sitingachitepo kanthu mwamsanga kuzizula mumtima mwathu, zingapitirize kukula ngati chomera chakupha ndipo zingayambitse mavuto.—Yak. 1:14, 15.
Kodi Mukutsatira Machenjezo a Yehova Omveka Bwino?
7 Kodi tingapewe bwanji aphunzitsi onyenga? Sitiwalandira m’nyumba zathu kapena kuwapatsa moni. Timakananso kuwerenga mabuku awo, kuwaonera pa TV ndiponso kuwerenga kapena kuyankha zimene alemba pa Intaneti. N’chifukwa chiyani timawakana kwamtuwagalu? Chifukwa chakuti timakonda “Mulungu wachoonadi” ndipo timadana ndi ziphunzitso zopotoka zimene zimasemphana ndi Mawu ake a choonadi. (Sal. 31:5; Yoh. 17:17) Timakondanso gulu la Yehova limene latiphunzitsa mfundo zosangalatsa za choonadi. Mwachitsanzo, taphunzira za dzina lakuti Yehova ndi tanthauzo lake, cholinga chimene Mulungu analengera dziko lapansi, zimene zimachitika munthu akamwalira ndiponso chiyembekezo chakuti akufa adzauka. Kodi mukukumbukira mmene munamvera mutangophunzira mfundo zamtengo wapatali ngati zimenezi? Musalole kuti mabodza amene aphunzitsi onyenga amanena akuchititseni kupandukira gulu la Mulungu limene lakuphunzitsani mfundo za choonadi zimenezi.—Yoh. 6:66-69.
8 Kaya aphunzitsi onyenga anene zotani, ife sitingawatsatire. Titati tiwatsatire tikhoza kukhumudwa kwambiri chifukwa ali ngati zitsime zouma. M’malomwake, tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake. Gulu limeneli silinatikhumudwitsepo ndipo kwa nthawi yaitali lakhala likutipatsa madzi oyera a choonadi ochokera m’Mawu a Mulungu.—Yes. 55:1-3; Mat. 24:45-47.
Mfundo Zothandiza
it-2 596
Vuwo
Mbalame yotchedwa vuwo ikakhuta kwambiri, nthawi zambiri imaulukira kumalo akutali komwe sikukhala anthu, kumene imakakhala mokhumata itapindira khosi lake m’mapewa ndipo sisunthasuntha moti kuchokera patali munthu akhoza kumangoona ngati pali mwala woyera. Mbalameyi imatha kukhala choncho kwa maola ambiri isanachokepo, zomwe zikugwirizana ndi mmene munthu wina amene analemba masalimo ankamvera panthawi imene sankatha kuchita zinthu zina chifukwa cha mavuto ake. Anapereka fanizo pofotokoza chisoni chake kuti: “Ndikufanana ndi mbalame yamʼchipululu yotchedwa vuwo.” (Sl 102:6) Palembali mawu akuti ‘chipululu’ sakutanthauza malo ouma komwe sikupezeka zomera kapena zamoyo koma akungonena za kumalo komwe sikukhala anthu, mwina m’madambo. M’nyengo zinazake pachaka mbalame zotchedwa vuwo zimapezekabe m’madambo akumpoto kwa chigwa cha Yorodano.
Mbalamezi zimakonda kukhala kumalo azokha kumene sizingasokonezedwe ndi anthu. Kumeneko zimamanga zisa komanso kukhala ndi ana ndipo n’kumene zimagona zikachoka kodya nsomba. Chifukwa choti imakonda kukhala kumalo kwayokha komanso kopanda anthu, mbalameyi imagwiritsidwa ntchito m’Baibulo pofotokoza za chiwonongeko. Kuti apereke chithunzi cha kuwonongedwa kwa Edomu, Yesaya analosera kuti vuwo azidzakhala m’dzikolo. (Yes 34:11) Nayenso Zefaniya analosera kuti mbalame ya vuwo idzagona pamitu ya zipilala za mzinda wa Nineve kusonyeza kuti mzindawo udzawonongedwa ndipo simudzakhalanso anthu.—Zef 2:13, 14.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
ijwbq 129
Kodi Baibulo Linasinthidwa Kapena Kusokonezedwa?
Ayi. Tikaona zimene zili m’mipukutu ya kale zikusonyeza kuti Baibulo silinasinthidwe. Zili choncho ngakhale kuti kwa zaka masauzande ambiri lakhala likukoperedwa pa zinthu zimene n’kupita kwa nthawi zimawonongeka.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti panalibe zolakwika pamene ankalikopera?
Pali mipukutu ya Baibulo yambiri yomwe ndi ya kale imene yapezeka. Zimene zili m’mipukutu ina ndi zosiyana ndi zimene zili m’mipukutu ina, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti panali zolakwika zina pamene ankakopera mipukutuyi. Zinthu zambiri zomwe ndi zosiyana m’mipukutuyi ndi zing’onozing’ono ndipo sizisintha tanthauzo la malembawo. Komabe, zikuoneka kuti malemba ena anasinthidwa kwambiri ndipo zikuoneka kuti anachita zimenezi mwadala n’cholinga chofuna kusokoneza uthenga wa m’Baibulo. Taonani zitsanzo ziwiri izi:
1. M’mipukutu ina ya kale ya Baibulo, lemba la 1 Yohane 5:7 analimasulira kuti: “kumwamba kuli Atate, Mawu, komanso Mzukwa Woyera: onsewa ndi mmodzi.” Komabe, mipukutu yodalirika imasonyeza kuti mawu amenewa munalibe m’mipukutu yoyambirira. Mawuwa anachita kuwonjezeredwa. N’chifukwa chake mawuwa sanaphatikizidwe m’Mabaibulo odalirika a masiku ano.
2. Dzina la Mulungu limapeza maulendo masauzande ambiri m’mipukutu ya kale ya Baibulo. Koma m’Mabaibulo ambiri anachotsa dzinali n’kuika mayina aulemu monga “Ambuye” kapena “Mulungu.”
Kodi tingatsimikize bwanji kuti m’Baibulo mulibenso zolakwika zina zambiri?
Panopa pali mipukutu yambiri imene yapezeka ndipo zimenezi zathandiza kuti zikhale zosavuta kuzindikira zinthu zomwe n’zolakwika. Kodi kufananitsa zomwe zili m’mipukutuyi kwasonyeza zotani pa nkhani ya kulondola kwa Baibulo?
● Pothirira ndemanga pa Malemba Achiheberi (omwe amadziwika kwambiri kuti “Chipangano Chakale”), katswiri wamaphunziro dzina lake William H. Green ananena kuti: “Tikhoza kunena molimba mtima kuti palibenso zinthu zina zakale zimene zinakoperedwa molondola kwambiri chonchi.”
● Ponena za Malemba Achigiriki, kapena kuti “Chipangano Chatsopano,” katswiri wina wa Baibulo dzina lake F. F. Bruce analemba kuti: “Umboni wotsimikizira kuti nkhani zomwe zili mu Chipangano Chatsopano n’zoona ndi waukulu kwambiri kuposa umboni wa zolemba zina zili zonse zakale. Koma n’zodabwitsa kuti palibe amene amakayikira zolemba zakalezi zomwe zilibe umboni wokwanira.”
● Sir Frederic Kenyon, omwe ndi katswiri wodziwika bwino wa mipukutu ya Baibulo, ananena kuti munthu “akhoza kunyamula Baibulo m’manja mwake n’kunena mosaopa kapena kukayikira kuti amene wanyamulawo ndi mawu enieni a Mulungu omwe akhalapo kwa zaka zambiri popanda mfundo zofunika kwambiri kusokonekera.”
Kodi pali zifukwa zinanso ziti zotipangitsa kutsimikiza kuti Baibulo linakoperedwa molondola?
● Okopera Baibulo a Chiyuda komanso a Chikhristu, analemba nkhani zimene zimasonyeza machimo akuluakulu omwe atumiki a Mulungu anachita. (Numeri 20:12; 2 Samueli 11:2-4; Agalatiya 2:11-14) Komanso iwo analemba nkhani zodzudzula mtundu wa Ayuda chifukwa chosamvera. Nkhanizi zinathandizanso anthu kuzindikira ziphunzitso zina zomwe zinali maganizo a anthu. (Hoseya 4:2; Malaki 2:8, 9; Mateyu 23:8, 9; 1 Yohane 5:21) Anthu amene anakopera nkhanizi anasonyeza kuti anali okhulupirika komanso ankalemekeza kwambiri Mawu a Mulungu chifukwa anakopera nkhanizo molondola kwambiri.
● Kodi si zomveka kunena kuti Mulungu amene anauzira Baibulo, angathe kuchita chilichonse kuti lipitirizebe kukhala lolondola? (Yesaya 40:8; 1 Petulo 1:24, 25) Komanso sikuti iye ankafuna kuti Baibulo lingothandiza anthu akale, koma ankafuna kuti litithandizenso masiku ano. (1 Akorinto 10:11) Ndipotu, “zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.”—Aroma 15:4.
● Yesu komanso otsatira ake ankagwiritsa ntchito nkhani zochokera m’Malemba Achiheberi ndipo sanakayikire kuti nkhanizo zinali zolondola.—Luka 4:16-21; Machitidwe 17:1-3.
OCTOBER 28–NOVEMBER 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 103-104
“Amakumbukira Kuti Ndife Fumbi”
Muzitsanzira Yehova pa Nkhani Yololera
5 Kudzichepetsa komanso kukoma mtima kumachititsa Yehova kuti akhale wololera. Mwachitsanzo Yehova anasonyeza kuti ndi wodzichepetsa pamene ankafuna kuwononga anthu oipa ku Sodomu. Pogwiritsa ntchito angelo ake, Yehova anauza Loti kuti athawire kudera lamapiri. Koma Loti ankachita mantha kupita kumeneko. Choncho anachonderera Yehova kuti iye ndi banja lake athawire ku Zowari, tauni yaing’ono imene inkafunikanso kuwonongedwa. Yehova akanatha kuuza Loti kuti atsatirebe malangizo amene anamupatsa. M’malomwake anavomereza zimene Loti anapempha ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti asawononge mzinda wa Zowari. (Gen. 19:18-22) Patapita zaka zambiri, Yehova anasonyezanso chifundo kwa anthu a mumzinda wa Nineve. Iye anatumiza Yona kuti akalengeze kuti mzinda woipa wa Nineve uwonongedwa. Koma ataona kuti anthu a mumzindawo alapa, anawamvera chisoni ndipo sanawawononge.—Yona 3:1, 10; 4:10, 11.
Tizidalira Yehova Ngati Mmene Samisoni Ankachitira
16 Ngakhale kuti Samisoni anakumana ndi mavuto aakulu chifukwa cholakwitsa zinthu, iye sanasiye kuchita chifuniro cha Yehova. Choncho kaya talakwitsa zinthu ndipo tikufunika kudzudzulidwa, kusiyitsidwa udindo kapena utumiki winawake, sitiyenera kufooka. Tizikumbukira kuti Yehova amakhala wokonzeka kutikhululukira. (Sal. 103:8-10) Ngakhale kuti timalakwitsa zinthu, Yehova angatigwiritsebe ntchito ngati mmene anachitira ndi Samisoni.
17 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira m’bale wina wachinyamata dzina lake Michael. Iye ankatumikira Yehova mwakhama ndipo anali mtumiki wothandiza komanso mpainiya wokhazikika. N’zomvetsa chisoni kuti iye analakwitsa zinthu, zomwe zinachititsa kuti asiyitsidwe utumiki wake. Michael anati: “M’mbuyo monsemu zinthu zinkandiyendera bwino potumikira Yehova. Koma mwadzidzidzi zinangokhala ngati ndaomba khoma. Sindinkaganiza kuti Yehova angandisiye, komabe ndinkakayikira ngati ndingadzakhalenso naye pa ubwenzi wabwino ngati poyamba kapenanso kumachita zambiri pomutumikira mumpingo.”
18 N’zosangalatsa kuti Michael sanataye mtima. Iye anati: “Ndinayesetsa kuti ndikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova popemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima, kuphunzira Mawu ake komanso kuwaganizira mozama.” Patapita nthawi, iye anayambiranso kutumikira mumpingo ngati poyamba. Panopa iye ndi mkulu komanso mpainiya wokhazikika. Michael ananenanso kuti: “Zimene mpingo unachita makamaka akulu pondilimbikitsa, zinandithandiza kuzindikira kuti Yehova amandikondabe. Panopa ndikutumikiranso mumpingo ndili ndi chikumbumtima choyera. Zomwe zinandichitikirazi zinandiphunzitsa kuti Yehova amakhululukira aliyense yemwe walapa kuchokera pansi pa mtima.” Ifenso tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa komanso kutigwiritsa ntchito ngakhale kuti tinalakwitsapo zinazake. Chongofunika ndi kuchita zonse zomwe tingathe kuti tikonze zomwe tinalakwitsazo, n’kupitiriza kumudalira.—Sal. 86:5; Miy. 28:13.
Mungathe Kukwaniritsa Zolinga Zanu Zauzimu
2 Ngati panopa muli ndi cholinga china chomwe simunachikwaniritse, dziwani kuti si inu olephera. Kuti munthu akwaniritse ngakhale cholinga chaching’ono amafunika nthawi komanso khama. Mukamafunitsitsa kukwaniritsa cholinga chinachake mumasonyeza kuti mumaona kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ndi wamtengo wapatali komanso mukufunitsitsa kumupatsa zinthu zabwino kwambiri. Yehova amayamikira khama lanu. N’zoona kuti sayembekezera zambiri kuposa zimene mungakwanitse. (Sal. 103:14; Mika 6:8) Choncho muzikhala ndi zolinga zimene mungazikwaniritse malinga ndi mmene zilili pa moyo wanu. Ndiye mukadziikira cholinga, kodi mungatani kuti muchikwaniritse? Tiyeni tione mfundo zina zomwe zingakuthandizeni.
Mfundo Zothandiza
Mphamvu za Kulenga—‘Anapanga Kumwamba Komanso Dziko Lapansi’
18 Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake zotha kulenga zinthu? Timasowa chonena tikaona kuchuluka kwa zinthu zosiyanasiyana zimene analenga. Wolemba masalimo wina anati: “Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova! . . . Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.” (Salimo 104:24) Zimenezitu ndi zoona. Asayansi apeza kuti padzikoli pali mitundu ya zamoyo yopitirira 1 miliyoni. Koma ena amati n’kutheka kuti pali zamoyo zambiri kuposa pamenepa. Nthawi zina munthu waluso angaone kuti akusowa zinthu zatsopano zoti achite. Koma luso la Yehova komanso mphamvu zake zotha kulenga zinthu zatsopano ndiponso zosiyanasiyana, sizidzatha.