Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 November tsamba 6-7
  • November 25–‏December 1

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • November 25–‏December 1
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 November tsamba 6-7

NOVEMBER 25–DECEMBER 1

MASALIMO 109-112

Nyimbo Na. 14 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muzithandiza Yesu, Mfumu Yathu

(10 min.)

Atapita kumwamba, Yesu anakhala kudzanja lamanja la Yehova (Sl 110:1; w06 9/1 13 ¶6)

Mu 1914, Yesu anayamba kugonjetsa adani ake (Sl 110:2; w00 4/1 18 ¶3)

Tingadzipereke mofunitsitsa pothandiza ulamuliro wa Yesu (Sl 110:3; be 76 ¶2)

Zithunzi zosonyeza m’bale wachinyamata akuthandiza ulamuliro wa Yesu: 1. Akuperekera maikolofoni pa misonkhano yampingo. 2. Akuthandiza mlongo wachikulire amene ali pa njinga ya olumala. 3. Akuphunzira Baibulo payekha. 4. M’bale wina akumuphunzitsa mmene angachitire utumiki watsopano mumpingo.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingakhale ndi zolinga zotani pofuna kusonyeza kuti ndimathandiza Ufumu wa Mulungu?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 110:4—Fotokozani pangano lomwe lili muvesili. (it-1 524 ¶2)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 109:1-26 (th phunziro 2)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Yambani kukambirana pogwiritsa ntchito kapepala. (lmd phunziro 4 mfundo 3)

5. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(5 min.) Chitsanzo. ijwfq 23—Mutu: N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Samenya Nawo Nkhondo? (lmd phunziro 4 mfundo 4)

6. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) lff phunziro 15 mfundo 6 komanso Zimene Ena Amanena (lmd phunziro 11 mfundo 3)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 72

7. Kodi Tingathandize Bwanji Ufumu wa Mulungu Mokhulupirika?

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza “Kalonga Wamtendere” Mokhulupirika.” Abale awiri akulalikira kwa munthu amene ali m’mbali mwa nyanja.

Ufumu wa Mulungu umasonyeza kuti Yehova ndi wolamulira wachilengedwe chonse. (Da 2:44, 45) Choncho nthawi zonse tikamachita zinthu zothandiza Ufumu wa Mulungu, timakhala tikusonyeza kuti Yehova ndi wolamulira wabwino.

Onerani VIDIYO yakuti Muzithandiza “Kalonga Wamtendere” Mokhulupirika. Kenako funsani funso ili:

  • Kodi timathandiza bwanji Ufumu wa Mulungu mokhulupirika?

Lembani lemba lomwe likugwirizana ndi njira zotsatirazi za mmene tingathandizire Ufumu wa Mulungu.

  • Kuona kuti Ufumuwu ndi wofunika kwambiri pa moyo wathu.

  • Kukhala ndi makhalidwe abwino omwe nzika za Ufumuwu zimayenera kukhala nawo.

  • Kuuza ena mwakhama zokhudza Ufumu.

  • Kulemekeza maboma a anthu, koma kumvera Mulungu ngati malamulo a Kaisara akutsutsana ndi malamulo a Mulungu.

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 18 ¶16-24

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena