Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu
© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
JANUARY 6-12
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 127-134
Makolo, Pitirizani Kusamalira Cholowa Chanu Chamtengo Wapatali
Muziyamikira Mwayi Wanu Wokhala M’banja la Yehova
9 Yehova analenga anthu kuti azikhala ndi ana, ndipo anawapatsa udindo wophunzitsa anawo kuti azimukonda komanso kumutumikira. Ngati ndinu makolo, kodi mumayamikira mwayi umene Yehova anakupatsaniwu? Angelo sanapatsidwe mwayiwu ngakhale kuti anapatsidwa luso lochita zinthu zambiri. Poganizira mfundo imeneyi, makolo amene akulera ana ayenera kuona kuti umenewu ndi udindo wofunika kwambiri. Makolo apatsidwa udindo wolera ana awo “m’malangizo a Yehova ndikuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4; Deut. 6:5-7; Sal. 127:3) Pofuna kuthandiza makolo, gulu la Yehova limapereka zinthu zothandiza pophunzira Baibulo monga mabuku, mavidiyo, nyimbo komanso zinthu zina kudzera pa webusaiti. N’zoonekeratu kuti Atate wathu wakumwamba komanso Mwana wake amakonda kwambiri ana. (Luka 18:15-17) Makolo akamadalira Yehova n’kumachita zonse zomwe angathe posamalira ana awo, omwe ndi amtengo wapatali, Yehova amasangalala. Ndipo makolo oterewa, amathandiza ana awo kukhala ndi chiyembekezo chodzakhala m’banja la Yehova mpaka kalekale.
Makolo Ayenera Kuphunzitsa Ana Awo Kukonda Yehova
20 Muzidziwa bwino ana anu. Lemba la Salimo 127 limayerekezera ana ndi mivi. (Werengani Salimo 127:4.) Mofanana ndi mivi imene imapangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana komanso imasiyana kukula kwake, ananso amakhala osiyana. Choncho makolo ayenera kudziwa mmene angaphunzitsire mwana aliyense. Banja lina la ku Israel lomwe linalera bwino ana awo awiri kuti azitumikira Yehova linafotokoza zimene zinawathandiza. Iwo anati: “Tinkaphunzira ndi mwana aliyense payekha.” Munthu aliyense amene ndi mutu wa banja angasankhe ngati zimenezi zingathandize.
Mfundo Zothandiza
it-1 543
Zomera Zotchulidwa M’Baibulo
Amene analemba masalimo anatchula zina zimene zimachitika ndi mtengo wa maolivi pomwe ankalonjeza anthu amene amaopa Yehova kuti: “Ana ako adzakhala ngati mphukira za mtengo wa maolivi kuzungulira tebulo lako.” (Sl 128:1-3) Mtengo wa maolivi umene wakula bwino, amadula mphukira zake pofuna kudzala mitengo ina. Kuwonjezera pamenepo, mizu ya mtengo wa maolivi umene wakhala nthawi yaitali imayambanso kuphukira zomwe zimathandiza kuti mtengowo upitirize kukula. Mofanana ndi mphukira, ana amakhala pafupi ndi bambo awo, zomwe zimathandiza kuti banja lizisangalala.
JANUARY 13-19
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 135-137
“Ambuye Wathu Ndi Wamkulu Kuposa Milungu Ina Yonse”
it-2 661 ¶4-5
Mphamvu, Ntchito Zamphamvu
Mulungu amasonyeza kuti amatsogolera mphamvu zam’chilengedwe. Anthu ena amayembekezera kuti, kuti Yehova asonyeze kuti iye ndi Mulungu woona amayenera kutsogolera mphamvu zam’chilengedwechi pofuna kuyeretsa dzina lake. (Sl 135:5, 6) Zinthu zam’chilengedwe monga dzuwa, mwezi, mapulaneti komanso nyenyezi zimayenda motsatira dongosolo lake nthawi zonse. Zimene zimapanga zinthu monga mphepo, mvula ndi zinthu zina zimatsatira malamulo amene amazitsogolera. Dzombe limauluka m’magulu komanso mbalame zimasamuka. zinthu zimenezi ndi zinthu zinanso zambiri, pazokha sizingayeretse dzina la Mulungu kwa anthu otsutsa kapena olambira milungu yabodza.
Komabe, Yehova Mulungu akhoza kuchititsa kuti zinthu zam’chilengwechi zikwaniritse cholinga chinachake ndipo zichite zinthu mwamphamvu kuposa mmene zimachitira nthawi zonse pofuna kusonyeza Umulungu wake. Ngakhale zinthu zina monga chilala, mvula yamphamvu komanso nyengo, pazokha si zachilendo koma pa nthawi imene zinachitika pofuna kukwaniritsa ulosi wa Yehova, zinasonyeza kuti ndi zapadera. (Yerekezerani ndi 1Mf 17:1; 18:1, 2, 41-45.) M’zochitika zambiri, zinthu zimenezi zinali zodabwitsa mwina chifukwa chakuti zinachitika mwamphamvu kwambiri (Eks 9:24) kapena chifukwa chakuti zinachitika m’njira imene zinali zisanachitikepo, modzidzimutsa kapenanso mosayembekezereka.—Eks 34:10; 1Sa 12:16-18.
Kodi Timapindula Bwanji ndi Chikondi Chokhulupirika cha Yehova?
16 Yehova akakhala malo athu othawirako, timamva kuti ndife otetezeka. Komabe nthawi zina tikhoza kufooka n’kumalephera kusiya kumva choncho. Ndiye kodi Yehova angatichitire zotani pa nthawi ngati imeneyo? (Werengani Salimo 136:23.) Pang’onopang’ono, iye adzatinyamula m’manja ake n’kutithandiza kuti tikhalenso olimba. (Sal. 28:9; 94:18) Mmene timapindulira: Kudziwa kuti tingadalire Mulungu kuti azitithandiza, kumatikumbutsa kuti anthufe tinadalitsidwa m’njira ziwiri. Choyamba, tili ndi malo achitetezo othawirako posatengera kumene timakhala. Ndipo chachiwiri, Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambiri.
Mfundo Zothandiza
it-1 1248
Ya
Mawu akuti Ya nthawi zambiri amagwiritsidwa ntchito m’Baibulo anthu akamafotokoza mmene akumvera mumtima potamanda Yehova komanso poimba nyimbo, kapena popemphera komanso pochonderera Yehova, ndipo kawirikawiri amakonda kugwiritsidwa ntchito pamene anthu akusangalala chifukwa choti apambana kapena apulumutsidwa, kapenanso pamene akufotokoza umboni wa mphamvu za Mulungu. Zitsanzo za zimenezi ndi zambiri. Mawu akuti “Tamandani Ya!” (Aleluya) omwe amatanthauza kutamanda Mulungu, amapezeka m’buku la Masalimo, ndipo amapezeka koyamba pa Salimo 104:35. Mu masalimo ena amapezeka kumayambiriro kokha (Sl 111, 112), nthawi zina cham’katikati (135:3), ndipo nthawi zinanso kumapeto kokha (Sl 104, 105, 115-117), koma nthawi zambiri kumayambiriro ndi kumapeto komwe (Sl 106, 113, 135, 146-150). M’buku la Chivumbulutso, zolengedwa za kumwamba zimatchulidwa zikutamanda Mulungu mobwerezabwereza pogwiritsa ntchito mawu amenewa.—Chv 19:1-6.
Malo ena onse amene mawu akuti Ya amapezeka, amasonyeza kutamanda Yehova kudzera mu nyimbo komanso m’pemphero. Pali nyimbo ya chipulumutso ya Mose. (Eks 15:2) M’buku la Yesaya, tanthauzo la mawuwa limamveketsedwa bwino pophatikiza mayina onse “Ya, Yehova.” (Yes 12:2; 26:4) Hezekiya atachiritsidwa modabwitsa pamene anatsala pang’ono kumwalira, analemba ndakatulo yofotokoza mmene ankamvera ndipo anagwiritsa ntchito mobwerezabwereza mawu akuti Ya. (Yes 38:9, 11) Pali kusiyana pakati pa anthu akufa, amene sangatamande Ya, ndi anthu amoyo amene adzatamanda Ya mpaka kalekale. (Sl 115:17, 18; 118:17-19) Komabe m’masalimo ena mawuwa amagwiritsidwa ntchito m’pemphero losonyeza kuyamikira pamene anthuwo apulumutsidwa, atetezedwa kapena athandizidwa.—Sl 94:12; 118:5, 14.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
ijwfq 7
Kodi Ndinu Akhristu?
Inde. Ndife Akhristu pa zifukwa zotsatirazi:
• Timayesetsa kutsatira mosamala zimene Yesu Khristu ankaphunzitsa komanso khalidwe lake.—1 Petulo 2:21.
• Timakhulupirira kuti munthu angadzapulumuke pokhapokha ngati atakhulupirira Yesu chifukwa “palibe dzina lina pansi pa thambo, limene laperekedwa kwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”—Machitidwe 4:12.
• Kuti munthu akhale wa Mboni za Yehova, amabatizidwa m’dzina la Yesu.—Mateyu 28:18, 19.
• Timapemphera m’dzina la Yesu.—Yohane 15:16.
• Timakhulupirira kuti Yesu ndi Mutu, kapena kuti munthu amene wapatsidwa udindo, pa munthu wina aliyense.—1 Akorinto 11:3.
Komabe, ndife osiyana m’njira zambiri ndi zipembedzo zina zimene zimati n’zachikhristu. Mwachitsanzo, timakhulupirira kuti Baibulo limaphunzitsa zoti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, osati Mulungu mwana. (Maliko 12:29) Sitikhulupirira kuti munthu ali ndi mzimu umene umapitirizabe kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira, komanso palibe pamene Malemba amasonyeza zoti Mulungu amazunza anthu powawotcha kumoto wosazima. Sitikhulupiriranso zakuti anthu amene amatsogolera mu mpingo ayenera kukhala ndi mayina audindo amene amawachititsa kukhala apamwamba mosiyana ndi anthu ena onse.—Mlaliki 9:5; Ezekieli 18:4; Mateyu 23:8-10.
JANUARY 20-26
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 138-139
Musalole Kuti Mantha Akubwezeni M’mbuyo
Tizitamanda Yehova Mumpingo
10 Kodi inuyo mumachita mantha mukangoganiza zokweza dzanja lanu kuti muyankhe? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha. Ambirife timakhala ndi mantha tikafuna kuyankha. Koma kuti muthetse vutoli, choyamba muyenera kudziwa zimene zimakuchititsani mantha. Kodi mumaopa kuti muiwala zoti munene kapena munena zolakwika? Kapena kodi mumaganiza kuti ndemanga yanu singakhale yabwino ngati ya anthu ena? Ngati mumaopa zimenezi, musadandaule chifukwa zingasonyeze kuti ndinu wodzichepetsa komanso mumaona kuti anthu ena ndi okuposani. Yehova amakonda anthu odzichepetsa chonchi. (Sal. 138:6; Afil. 2:3) Koma iye amafunabe kuti muzimutamanda ndiponso kulimbikitsa abale ndi alongo anu kumisonkhano. (1 Ates. 5:11) Iye amakukondani ndipo angakuthandizeni kuti muzilimba mtima n’kumayankha.
Tizilimbikitsana Pamisonkhano ya Mpingo
7 Mungapeze mfundo zina zimene zingakuthandizeni mu Nsanja za Olonda za m’mbuyomu. Mwachitsanzo, muzikonzekera bwino. (Miy. 21:5) Mukamaidziwa bwino nkhaniyo, sizingakhale zovuta kuti muyankhepo. Komanso ndemanga zanu zizikhala zachidule. (Miy. 15:23; 17:27) Simungamachite mantha kwambiri kupereka ndemanga yachidule. Ndemanga yachidule, mwinanso yokhala ndi chiganizo chimodzi kapena ziwiri, ingakhale yosavuta kumvetsa kwa abale ndi alongo anu kusiyana ndi ndemanga yaitali yokhala ndi mfundo zambiri. Mukamayankha mwachidule komanso m’mawu anuanu, mumasonyeza kuti mwakonzekera bwino komanso mwamvetsa zimene mukuphunzirazo.
Mfundo Zothandiza
it-1 862 ¶4
Kukhululuka
Kuwonjezera pamenepa, Akhristu amafunika kukhululukira anthu amene awalakwira posatengera kuti awalakwira kangati. (Lu 17:3, 4; Aef 4:32; Akl 3:13) Mulungu sangakhululukire anthu amene amakana kukhululukira anzawo. (Mt 6:14, 15) Komabe, ngakhale munthu atachita tchimo lalikulu mpaka kufika pochotsedwa mumpingo wa Chikhristu, akhoza kukhululukidwa ngati atasonyeza kuti walapa kuchokera pansi pa mtima. Pa nthawiyi anthu onse mumpingo angafunike kumusonyeza kuti amamukonda. (1Ak 5:13; 2Ak 2:6-11) Komabe, Akhristu sayenera kukhululukira anthu oipa amene amadana ndi anzawo komanso amene amachita machimo mwadala osalapa. Anthu amenewa amakhala adani a Mulungu.—Ahe 10:26-31; Sl 139:21, 22.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
ijwyp 105
Mungatani Kuti Musamachite Manyazi Kwambiri?
Vuto lake: Manyazi angakumanitseni zinthu zina ndipo simungapeze anzanu abwino.
Ubwino wake: Manyazi si oipa nthawi zonse. Amathandiza kuti munthu uziganiza usanalankhule, uziona zinthu moyenerera komanso uzimvetsera ena akamalankhula.
Mfundo yolimbikitsa: Pali zomwe mungachite kuti musakhale amanyazi kwambiri ndipo tikambirana zinthu zimenezi munkhaniyi.
Kodi ndi zinthu ziti zimene mumaopa?
Munthu wamanyazi amaopa kulankhula ndi anthu pamasom’pamaso. Izi zingachititse kuti musapeze anzanu ambiri n’kumangokhala ngati muli m’chipinda chanokha chamdima. Zimenezi n’zoopsa kwambiri. Koma mukaganizira zimene mumaopa mutha kupeza kuti palibe chifukwa choopera. Taonani zinthu zitatu zimene ena amaopa.
• Choyamba: “Ndimasowa nkhani zoti ndizikamba.”
Zoona zake: Anthu sakumbukira kwambiri zimene mumalankhula koma mmene amamvera akakhala ndi inuyo. Mungachepetse mantha anu ngati mutakulitsa luso lanu lomvetsera, muzichita chidwi ndi zimene anthu ena amalankhula.
Ganizirani izi: Kodi mumakonda munthu wotani, wolongolola amene sasowa chonena pa nkhani iliyonse kapena amene amamvetsera bwino wina akamalankhula?
• Chachiwiri: “Anthu akhoza kuona kuti ndine wobowa.”
Zoona Zake: Anthu amanenabe za munthu kaya ndi wamanyazi kapena ayi. Mukhoza kusiya kuopa zimenezi ndipo n’zotheka kuchititsa anthu kuti azinena zabwino za inuyo. Chongofunika ndi kuwapatsa mpata woti akudziweni bwino.
Ganizirani izi: Mukamakhala ndi maganizo akuti anthu sakunena zabwino za inuyo, nthawi zina zimakhala kuti inuyo ndi amene mukuwaganizira zolakwika.
• Chachitatu: “Ndikhoza kuchita manyazi kwambiri ngati nditanena zolakwika.”
Zoona zake: Zimenezi zikhoza kuchitikira aliyense. Mukhoza kusiya kuopa zimenezi. Chongofunika ndi kuphunzira kudziseka nokha ngati mwalakwitsa zinazake.
Ganizirani izi: Ngakhale inuyo, kodi simusangalala kukhala ndi anthu amene amavomereza kuti amalakwitsa zinthu zina?
Kodi mukudziwa? Anthu ena amaganiza kuti si amanyazi chifukwa choti amalemba kwambiri mameseji. Koma kuti munthu akhale mnzako weniweni pamafunika kukumana naye pamasom’pamaso. Wasayansi wina dzina lake Sherry Turkle analemba kuti: “Umunthu weniweni umaonekera tikakumana n’kumalankhulana uku tikuonana.”
Zimene Mungachite
• Musamadziyerekezere ndi anthu ena. Musamafune kufanana ndi anthu ochangamuka kwambiri. Muzingoonetsetsa kuti simukuchita manyazi kwambiri n’cholinga choti zinazake zisakupiteni komanso muyambe kugwirizana ndi anthu.
“Sikuti mufunika kukamba nkhani zambirimbiri kapena kukhala ngati muli kupate nthawi zonse. Umangofunika kuuza munthu wachilendo dzina lako, kenako n’kumufunsa mafunso angapo osavuta basi.”—Alicia.
Mfundo ya m’Baibulo: “Koma aliyense payekha ayese ntchito yake kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake osati modziyerekezera ndi munthu wina.”—Agalatiya 6:4.
• Muzikhala tcheru. Muziona zimene anthu ochezeka amachita akamalankhula ndi anthu. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimawathandiza? Nanga ndi zinthu ziti zimene zimawavuta nthawi zina? Nanga ndi maluso ati amene ali nawo omwe mungafune kutengera?
“Muziona zimene anthu amene savutika kupeza anzawo amachita. Muziona zimene amachita komanso zimene amalankhula akakumana ndi munthu koyamba.”—Aaron.
Mfundo ya m’Baibulo: “Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.”—Miyambo 27:17.
• Muzifunsa mafunso. Anthu amakonda kufotokoza maganizo awo pa nkhani zosiyanasiyana choncho kufunsa mafunso kumathandiza kuti muyambe kucheza. Kumathandizanso kuti anthu asiye kuganizira kwambiri za inuyo.
“Kukonzekereratu kungakuthandizeni kuti musamaope kwambiri. Mukhoza kuganizira nkhani zingapo zimene mungakambirane ndi anthu musanapite kokacheza, n’cholinga choti musakapanikizike mukakakumana ndi anthu achilendo.”—Alana.
Mfundo ya m’Baibulo: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena”—Afilipi 2:4.
JANUARY 27–FEBRUARY 2
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 140-143
Muzichita Zinthu Mogwirizana ndi Mapemphero Anu Opempha Thandizo
‘Imva Mawu a Anthu Anzeru’
13 Tiziona kuti kupatsidwa malangizo ndi umboni wakuti Yehova amatikonda. Yehova amatifunira zabwino. (Miy. 4:20-22) Iye akatipatsa malangizo kudzera m’Mawu ake, m’mabuku ofotokoza Baibulo kapena kudzera mwa Mkhristu mnzathu, amakhala akutisonyeza chikondi chake. Lemba la Aheberi 12:9, 10 limati, ‘amatilangiza kuti tipindule.’
14 Tiziganizira kwambiri malangizowo osati mmene aperekedwera. Nthawi zina tingaone ngati munthu sanatipatse malangizo m’njira yoyenera. N’zoona kuti aliyense amene akufuna kupereka malangizo ayenera kuyesetsa kuchita zimenezo m’njira yabwino. (Agal. 6:1) Ngati ndife amene tikulangizidwa, tingachite bwino kuganizira malangizo amene tapatsidwa, ngakhale titaona kuti munthu amene watipatsa malangizowo akanatha kuchita zimenezo m’njira yabwino. Mwina tingadzifunse kuti: ‘Ngakhale kuti sindinakonde njira imene wandipatsira malangizowo kodi pali zimene ndingaphunzirepo? Kodi ndinganyalanyaze zimene amene wandipatsa malangizoyo amalakwitsa, n’kugwiritsa ntchito malangizo amene waperekawo?’ Tingakhale anzeru ngati nthawi zonse timayesetsa kuti tizipindula ndi malangizo amene tapatsidwa.—Miy. 15:31.
Khalanibe ‘Oyera Mtima’ Masiku Ovuta Ano
Atumiki a Mulungu ena amavutika chifukwa cha kutsutsidwa, mavuto a zachuma ndiponso matenda akulu. Nthawi zina, zimenezi zimachititsa kuti azivutika mu mtima mwawo. Izi n’zimene zinachitikiranso Mfumu Davide. Iye anati: “Mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhawa m’kati mwanga.” (Sal. 143:4) Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupirira pa nthawi yovuta imeneyi? Davide anakumbukira zimene Mulungu anachitira atumiki Ake ndiponso mmene anamupulumutsira iyeyo. Anaganizira zimene Yehova anali atachita chifukwa cha dzina Lake lalikulu. Davide ankaganizira kwambiri ntchito za Mulungu. (Sal. 143:5) Ifenso, tikamaganizira za Mlengi wathu, zimene anatichitira ndiponso zimene akutichitira, tidzatha kupirira tikamayesedwa.
Kodi N’zothekadi Kukwatira Kapena Kukwatiwa “Mwa Ambuye”?
Nthawi zina mungakhale ndi maganizo amene Davide anali nawo. Iye anapemphera kuti: “Fulumirani, ndiyankheni inu Yehova. Mphamvu zanga zatha. Musandibisire nkhope yanu.” (Sal. 143:5-7, 10) Mukamamva chonchi, muyenera kuyembekezerabe kuti muone zimene Yehova akufuna kuti muchite. Poyembekezerapo muziwerenga Mawu ake n’kumaganizira kwambiri zimene mukuwerengazo. Mukatero mudzadziwa bwino malamulo a Yehova komanso mudzaona mmene ankathandizira anthu ake m’mbuyomu. Mukamamumvera mudzazindikira ubwino wotsatira malangizo ake.
Mfundo Zothandiza
it-2 1151
Poizoni
Mawu Ophiphiritsa. Mawu abodza komanso onyoza ochokera kwa munthu woipa, amene amawononga mbiri ya munthu amayerekezeredwa ndi poizoni wakupha wa njoka. (Sl 58:3, 4) Baibulo limanena za anthu oipawa kuti, “M’milomo yawo (kapena kuti, “kukhosi kwawo”) muli poizoni wa mphiri”, ndipotu malovu a poizoni a njoka ya mphiri amakhala pakati pa mlomo ndi mano a m’mwamba. (Sl 140:3; Aro 3:13) Lilime la munthu amene amalankhula zinthu zoipa, miseche, kuphunzitsa zinthu zabodza kapena kulankhula zinthu zina zoipa, “ndi lodzaza ndi poizoni wakupha.”—Yak 3:8.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
ijwfq 21
N’chifukwa Chiyani Mumakana Kuikidwa Magazi?
Iyi ndi nkhani yokhudzana ndi kulambira Mulungu, osangoti yokhudzana ndi chithandizo cha mankhwala basi. M’Baibulo, ku Chipangano Chakale ndi Chatsopano chomwe, muli malamulo omveka bwino akuti tipewe magazi. (Genesis 9:4; Levitiko 17:10; Deuteronomo 12:23; Machitidwe 15:28, 29) Komanso Mulungu amaona kuti magazi amaimira moyo. (Levitiko 17:14) Choncho timapewa magazi osati posonyeza kumvera Mulungu basi koma posonyeza kumulemekeza popeza ndi Mulunguyo amene amapereka moyo.
Anthu ena akusintha maganizo
M’mbuyomo, madokotala ankaona kuti njira zothandizira odwala popanda kuwaika magazi zinali zoopsa kwambiri. Koma masiku ano, madokotala ambiri asintha maganizo amenewo. Mwachitsanzo, mu 2004 m’magazini inayake ya nkhani zachipatala munali nkhani imene inanena kuti “njira zambiri zimene zakonzedwa kuti tizithandizira anthu a Mboni za Yehova akadwala, m’tsogolo muno zidzalowa m’malo mwa njira zinazi ndipo tidzayamba kuzigwiritsa ntchito pothandizira anthu onse.” M’chaka cha 2010, magazini inanso inati: “Njira yochitira opaleshoni popanda kuika wodwalayo magazi izigwiritsidwanso ntchito pothandiza odwala ena masiku ano, osati a Mboni za Yehova okha.”—Heart, Lung and Circulation.
Madokotala ambirimbiri masiku ano akuthandiza odwala powachita maopaleshoni akuluakulu komanso ovuta koma popanda kuwaika magazi. Zimenezi zikuchitika ngakhale m’mayiko osauka ndipo odwala ambiri, omwe si a Mboni, akumapempha kuti awachite opaleshoni popanda kuwaika magazi.
FEBRUARY 3-9
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 144-146
“Osangalala Ndi Anthu Amene Mulungu Wawo Ndi Yehova”
Mafunso Ochokera Kwa Owerenga
2. Kamasuliridwe katsopanoka n’kogwirizana ndi mawu ena onse musalimoli. Kugwiritsa ntchito mawu oti “zikatero” muvesi 12 kukuthandiza anthu kuona kuti madalitso otchulidwa muvesi 12 mpaka 14 ndi a anthu olungama amene amapempha kuti apulumutsidwe kwa anthu oipa achilendo amene atchulidwa muvesi 11. Mfundo imeneyi ikuonekeranso muvesi 15 chifukwa chakuti mawu oti “odala” akutchulidwa mosonyeza kuti akunena za anthu abwinowo osati za anthu ena. Chifukwa cha zimenezi, malo awiri amene pali mawu oti “odala” amaonekeratu kuti akunena za anthu amene “Mulungu wawo ndi Yehova.” Mfundo ina yofunika kuikumbukira ndi yakuti m’Chiheberi, anthu sankalemba zizindikiro za m’kalembedwe monga zosonyeza kuti mawu enaake ananenedwa ndi winawake. Choncho omasulira amafunika kuzindikira tanthauzo la mawu amene akumasulira lomwe likugwirizana ndi kalembedwe ka Chiheberi, nkhani imene akumasulira komanso nkhani zina za m’Baibulo zimene n’zogwirizana ndi nkhaniyo.
3. Kamasuliridwe katsopanoka kakugwirizana ndi nkhani zina za m’Baibulo zofotokoza madalitso amene Mulungu adzapatse anthu okhulupirika. Kamasuliridwe katsopanoka kakusonyeza kuti Davide sankakayikira mfundo yakuti Mulungu akadzapulumutsa mtundu wa Isiraeli kwa adani awo, Aisiraeliwo adzakhala osangalala ndiponso zinthu zizidzawayendera bwino. (Lev. 26:9, 10; Deut. 7:13; Sal. 128:1-6) Paja lemba la Deuteronomo 28:4 limanena kuti: “Chidzadalitsika chipatso cha mimba yako, chipatso cha m’dziko lanu, chipatso cha ziweto zako, ana a ng’ombe zako ndi ana a nkhosa zako.” Ndipo izi n’zimene zinachitika mu ulamuliro wa mwana wa Davide dzina lake Solomo. Aisiraeli anali pa mtendere ndipo zinthu zinkawayendera bwino. Tisaiwalenso kuti zinthu zina mu ulamuliro wa Solomo zinkasonyeza mmene zidzakhalire mu ulamuliro wa Mesiya.—1 Maf. 4:20, 21; Sal. 72:1-20.
Pitirizani Kulimbitsa Chiyembekezo Chanu
16 Chiyembekezo chathu cha moyo wosatha ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo ndipo sitimakayikira kuti zidzachitika. Chiyembekezo chili ngati nangula wathu ndipo chimatithandiza kukhala odekha kuti tizipirira mayesero, kuzunzidwa komanso sitiopa kufa. Chilinso ngati chisoti ndipo chimateteza maganizo athu kuti tizipewa kuchita zoipa n’kumayesetsa kuchita zabwino. Chiyembekezo chathu cha m’Baibulo chimatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo chimasonyeza kuti iye amatikonda kwambiri. Zinthu zimatiyendera bwino kwambiri tikapitiriza kukhala ndi chiyembekezo cholimba.
17 M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma, Paulo anawalimbikitsa kuti: “Kondwerani ndi chiyembekezocho.” (Aroma 12:12) Paulo ankasangalala chifukwa sankakayikira kuti akapitirizabe kukhala wokhulupirika, adzalandira moyo wosatha kumwamba. Ifenso tingamasangalale ndi chiyembekezo chathu chifukwa sitimakayikira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake. Wolemba masalimo anati: “Wodala ndi munthu amene . . . chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake, . . . Wosunga choonadi mpaka kalekale.”—Sal. 146:5, 6.
Kodi Tiyenera Kukonda Ndani Kuti Tikhale Osangalala?
19 Anthu akhala akuvutika m’dziko la Satanali kwa zaka zoposa 6,000. Koma posachedwapa, dzikoli liwonongedwa. Monga tanenera, anthu ambiri m’dzikoli ndi odzikonda, okonda ndalama komanso zosangalatsa. Iwo amangoganizira ndiponso kufunafuna zinthu zokomera iwowo basi. Anthu oterewa sangakhale osangalala. Paja wolemba masalimo ananena kuti: “Wodala ndi munthu amene thandizo lake limachokera kwa Mulungu wa Yakobo, amene chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake.”—Sal. 146:5.
20 Ifeyo timakonda kwambiri Mulungu ndipo chaka chilichonse, anthu ambirimbiri amalowa m’gulu lathu. Uwutu ndi umboni woti Ufumu wa Mulungu ukulamulira ndipo posachedwapa ubweretsa madalitso osaneneka padzikoli. Anthu amene amachita zofuna za Mulungu ndi amene amakhala osangalala chifukwa amadziwa kuti akusangalatsa Wolamulira wa chilengedwe chonse. Ndipotu amene amakonda Yehova adzakhala osangalala mpaka kalekale. Munkhani yotsatira, tidzakambirana makhalidwe ena amene anthu odzikonda amasonyeza, komanso tidzaona makhalidwe abwino amene atumiki a Yehova amasonyeza.
Mfundo Zothandiza
it-1 111 ¶9
Nyama
Baibulo limalimbikitsa kuti tizichitira chilungamo komanso chifundo zolengedwa zotsika. Zimenezi ndi zomveka, chifukwa Yehova amanena yekha kuti iye ndi amene amazisamalira mwachikondi. (Miy 12:10; Sl 145:15, 16) M’Chilamulo cha Mose munali lamulo lonena kuti anthu azisamalira ziweto. Chilamulochi chinkanena kuti anthu akapeza chiweto chomwe chasochera, azichibweza kwa mwiniwake; komanso akapeza chiweto chomwe chagona pansi chifukwa cholemedwa ndi katundu, azithandiza kumasula katunduyo. (Eks 23:4, 5) Akamazigwiritsa ntchito, ankafunika kumachita zinthu moziganizira. (De 22:10; 25:4) Mofanana ndi anthu, nyamazi zinkafunika kumapumanso pa Tsiku la Sabata. (Eks 20:10; 23:12; De 5:14) Nyama zoopsa ankafunika kumaziyang’anira kapena kuzipha kuti zisavulaze anthu. (Ge 9:5; Eks 21:28, 29) Sankafunika kuchititsa kuti nyama zamitundu yosiyana zikwerane.—Le 19:19.
FEBRUARY 10-16
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 147-150
Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zotamandira Ya
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutamanda Yehova?
5 Sikuti Yehova ankangolimbikitsa Aisiraeli monga gulu koma ankalimbikitsanso aliyense payekha. Ndi mmene amachitiranso masiku ano. Wolemba Salimo 147 uja ananena kuti Mulungu “amachiritsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.” (Sal. 147:3) Izi zikusonyeza kuti Yehova amasamalira anthu amene akudwala komanso amene ali ndi nkhawa. Masiku anonso, Yehova amafunitsitsa kutitonthoza komanso kutilimbikitsa tikakhala ndi nkhawa. (Sal. 34:18; Yes. 57:15) Iye amatipatsa nzeru komanso mphamvu kuti tithe kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo.—Yak. 1:5.
6 Kenako, wolemba salimoyo anayamba kufotokoza zakumwamba. Iye ananena kuti Yehova “amawerenga nyenyezi zonse, ndipo zonsezo amazitchula mayina ake.” (Sal. 147:4) Mwina mukudabwa kuti n’chifukwa chiyani anangosintha nkhaniyi n’kuyamba kufotokoza zakumwamba? Taganizirani izi: Munthu amene analemba salimoli ankatha kuona nyenyezi koma sankadziwa kuti zilipo zingati. Panopa chiwerengero cha nyenyezi zimene anthu angathe kuziona chawonjezereka kwambiri. Ena amanena kuti mlalang’amba wathu wotchedwa Milky Way uli ndi nyenyezi mabiliyoni ambiri. Komatu milalang’ambayo ilipo yambirimbiri m’chilengedwechi. Choncho m’pomveka kunena kuti nyenyezi zilipo zosawerengeka. Koma Mlengi wathu amatha kupereka dzina kwa nyenyezi iliyonse. Izi zikusonyeza kuti Yehova amaona kuti nyenyezi iliyonse ndi yosiyana ndi inzake. (1 Akor. 15:41) Nanga bwanji za anthufe? Ngati Yehova amadziwa pamene pali nyenyezi iliyonse pa nthawi ina iliyonse ndiye kuti amadziwanso za munthu aliyense payekha. Izi zikutanthauza kuti amadziwa kumene muli, mmene mukumvera mumtima mwanu komanso chimene mukufunikira pa nthawi ina iliyonse.
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutamanda Yehova?
7 Sikuti Yehova amangodziwa bwino za inuyo panokha. Iye ndi wamphamvu komanso wachifundo moti angathe kukuthandizani pa vuto lanu lililonse. (Werengani Salimo 147:5.) Mwina nthawi zina mumaganiza kuti mavuto anu ndi aakulu kwambiri moti simungathe kuwapirira. Koma Yehova ndi wanzeru ndipo amadziwa zimene simungakwanitse komanso ‘amakumbukira kuti ndinu fumbi.’ (Sal. 103:14) Popeza si ife angwiro, timalakwitsa zinthu nthawi ndi nthawi. Timadandaula pamene talankhula mawu olakwika, kuchita zinthu zolakwika kapena kusirira zimene anthu ena ali nazo. Yehova alibe mavuto ngati amenewa koma amatimvetsa bwino kwambiri.—Yes. 40:28.
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutamanda Yehova?
18 Wolemba salimo uja ankadziwa kuti Aisiraeli anali ndi mwayi waukulu kwambiri. Zili choncho chifukwa ndi iwo okha amene anapatsidwa “mawu” a Mulungu komanso “malangizo ake ndi zigamulo zake.” (Werengani Salimo 147:19, 20.) Masiku ano, nafenso tili ndi mwayi waukulu chifukwa ndi ife tokha amene timadziwika ndi dzina la Mulungu. Timakhalanso pa ubwenzi wolimba ndi Yehova chifukwa chomudziwa ndiponso kutsogoleredwa ndi Mawu ake. Mofanana ndi wolemba Salimo 147, nanunso muyenera kuti muli ndi zifukwa zambiri zonenera kuti “Tamandani Ya” komanso zolimbikitsira anthu ena kuti azichita zimenezi.
Mfundo Zothandiza
it-1 316
Mbalame
Wolemba masalimo anaitana “mbalame zamapiko” kuti zitamande Yehova (Sl 148:1, 10), ndipo mbalame zimakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa choti zinalengedwa modabwitsa. Mbalame imodzi ikhoza kukhala ndi nthenga kuyambira 1,000 mpaka 20,000 kapena kuposa. Nthenga iliyonse imakhala ndi thunthu, ndipo pathunthupo pamakhala tinthambi mahandiredi ambirimbiri. Nthenga imodzi ya nkhunda ya masentimita atatu, ikhoza kukhala ndi tinthambi mamiliyoni ambiri. Nthenga za mbalame ndi zogometsa kwambiri kuposa ndege zimene anthu akupanga masiku ano. Mbalame zimakhala ndi mafupa opepuka okhala ndi mphako mkati moti mafupa a mbalame ina ya m’gulu la vuwo yokhala ndi mapiko aatali mamita awiri, akhoza kulemera magalamu 110. Mafupa a m’mapiko a mbalame zina zikuluzikulu amakhala olukanalukana ngati matabwa okhomera denga, mofanana ndi tizitsulo tomwe timakhala mkati mwa mapiko a ndege.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Tizimvetsera Mawu a Yehova
7 Werengani Mateyu 17:1-5. Ulendo wachiwiri pamene Yehova analankhula kuchokera kumwamba ndi pa nthawi imene Yesu “anasandulika.” Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane n’kupita nawo kuphiri lalitali. Ali kuphiriko, ophunzirawo anaona zinthu zodabwitsa kwambiri. Nkhope ya Yesu inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinawalanso kwambiri. Kenako panaoneka Mose ndi Eliya akulankhula naye zokhudza imfa yake. Ngakhale kuti ophunzira akewa anali “atatopa ndi tulo,” iwo anaona bwinobwino masomphenya odabwitsawa. (Luka 9:29-32) Kenako mtambo waukulu unawaphimba ndipo panamveka mawu a Mulungu kuchokera mumtambowo. Pa nthawi ya ubatizo ija, Yehova anasonyeza kuti amakonda Mwana wake komanso amakondwera naye ponena kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.” Koma pa nthawiyi anawonjezerapo mawu akuti: “Muzimumvera.”
8 Masomphenya amenewa ankasonyeza zimene zidzachitike Yesu akadzalandira mphamvu ndi ulemerero monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. N’zosachita kufunsa kuti Yesu analimbikitsidwa kwambiri moti anali wokonzeka kupirira mavuto ndi imfa zimene anali atatsala pang’ono kukumana nazo. Zimene ophunzirawa anaona zinalimbitsanso chikhulupiriro chawo n’kuwapatsa mphamvu kuti adzapirire komanso kugwira ntchito mwakhama m’tsogolo. Patapita zaka 30, mtumwi Petulo anafotokoza za masomphenya amenewa ndipo izi zikusonyeza kuti ankawakumbukirabe.—2 Pet. 1:16-18.
8 “Muzimumvera.” Yehova anasonyeza kuti amafuna kuti tizimvera mawu a Mwana wake. Ndiye kodi ndi zinthu ziti zimene Yesu ananena ali padzikoli? Iye ananena zinthu zambiri zofunika kuzitsatira. Mwachitsanzo, iye anaphunzitsa bwino ophunzira ake ntchito yolalikira uthenga wabwino ndipo anawauza mobwerezabwereza kuti ayenera kukhala maso. (Mat. 24:42; 28:19, 20) Iye anawauzanso kuti azichita zinthu mwamphamvu komanso kuti asafooke. (Luka 13:24) Yesu anauzanso ophunzira ake kuti ayenera kukondana, kukhala ogwirizana komanso kutsatira malamulo ake. (Yoh. 15:10, 12, 13) Apatu tingati Yesu anapereka malangizo abwino kwa ophunzira ake. Malangizo amenewa ndi othandizanso masiku ano.
10 Yesu ananena kuti: “Aliyense amene ali kumbali ya choonadi amamvera mawu anga.” (Yoh. 18:37) Ndiye timasonyeza kuti tikumvera mawu ake tikamapitiriza “kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.” (Akol. 3:13; Luka 17:3, 4) Timasonyezanso kumvera mawu ake tikamalalikira uthenga wabwino mwakhama “m’nthawi yabwino ndi m’nthawi yovuta.”—2 Tim. 4:2.
11 Yesu ananena kuti: “Nkhosa zanga zimamva mawu anga.” (Yoh. 10:27) Otsatira ake amasonyeza kuti amamva mawu ake osati pongomvetsera koma potsatira zimene watiuzazo. Iwo salola kusokonezeka ndi “nkhawa za moyo.” (Luka 21:34) Ngakhale zinthu zitavuta kwambiri, iwo amaona kuti chofunika kwambiri ndi kutsatira mawu a Yesu. Abale athu ambiri akukumana ndi mavuto akuluakulu monga kuzunzidwa, kusauka komanso ngozi zogwa mwadzidzidzi. Koma iwo amakhalabe okhulupirika kwa Yehova zivute zitani. Kwa anthu amene akukumana ndi mavutowa, Yesu akuwatsimikizira kuti: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda. Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso.”—Yoh. 14:21.
FEBRUARY 17-23
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 1
Achinyamata, Kodi Mudzamvera Ndani?
Musalole Kuti Chilichonse Chikulepheretseni Kulandira Mphoto
16 Ngati ndinu wachinyamata ndipo mumaona kuti makolo anu sakumvetsani komanso amakupanikizani, kodi mungatani? Maganizo amenewa akhoza kukuchititsani kuganiza kuti si nzeru kutumikira Yehova ndipo ngati maganizo amenewa atakula mukhoza kusiyadi kumutumikira. Koma dziwani kuti mukasiya, mudzaona nokha kuti palibenso anthu ena amene amakukondani ndi mtima wonse ngati mmene amachitira makolo anu komanso abale ndi alongo.
17 Ndipo ngati makolo anu sakulangizani, zingakhale zokayikitsa kuti amakukondani ndi mtima wonse. (Aheb. 12:8) Mwina njira imene makolowo amakulangizirani ndi imene sikusangalatsani. Koma m’malo mongoipidwa ndi mmene amaperekera malangizo, muyenera kuganizira chimene chimawapangitsa kuchita zimenezo. Choncho muyenera kukhala odekha ndipo muziyesetsa kuti musamakwiye msanga akamakudzudzulani. Paja Mawu a Mulungu amanena kuti: “Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziwa zinthu, ndipo munthu wozindikira amakhala wofatsa.” (Miy. 17:27) Yesetsani kuchita zinthu ngati wozindikira ndipo mukamalangizidwa muzimvetsera mofatsa. Muziyesetsa kuona mmene mungagwiritsire ntchito malangizowo popanda kuganizira kwambiri mmene akuwaperekera. (Miy. 1:8) Dziwani kuti ndi dalitso lalikulu kukhala ndi makolo amene amakonda Yehova ndi mtima wonse. Iwo amafunitsitsa kukuthandizani kuti mudzapeze mphoto ya moyo wosatha.
Kuteteza Dzina Lathu Monga Akhristu
11 Kondweretsani Mulungu, osati anthu. N’zachibadwa kufuna kudziwika kuti tili m’gulu linalake. Aliyense amafuna kukhala ndi anzake, ndipo timamva bwino kukhala pagulu la anzathu. Ana akamafika pamsinkhu wachinyamata ndiponso akakula ndithu, angatengeke kwambiri ndi zochita za anzawo. Izi zingakulitse mtima wofunitsitsa kutsanzira ena kapena kuwasangalatsa. Komatu dziwani kuti anzathu ndiponso anthu amsinkhu wathu sikuti nthawi zonse amatifunira zabwino ayi. Nthawi zina amangofuna wina woti azichita naye limodzi zoipazo. (Miyambo 1:11-19) Mkhristu akagonjera anzake amene akum’kakamiza kuchita zoipa, nthawi zambiri amayesetsa kudzibisa kuti ndi Mkhristu. (Salmo 26:4) Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Musatengere khalidwe la dzikoli.” (Aroma 12:2, The Jerusalem Bible) Yehova amatithandiza kukhala olimba kuti tisatengeke ndi zochita za ena.—Ahebri 13:6.
12 Ngati tikutengeka ndi zochita za anthu, zomwe zingaipitse dzina lathu monga Akhristu, ndi bwino kukumbukira kuti kukhala wokhulupirika kwa Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa maganizo a anthu kapena zochita za anthu ochuluka. Mfundo yabwino kwambiri pankhaniyi ikupezeka pa lemba la Eksodo 23:2 lomwe limati: “Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa.” Aisiraeli ochuluka atakayikira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo Ake, molimba mtima Kalebi anakana kuyendera maganizo a anzakewo. Iye anali wotsimikiza kuti malonjezo a Mulungu ndi odalirika, ndipo anapindula kwambiri chifukwa cha kulimba mtima kwakeko. (Numeri 13:30; Yoswa 14:6-11) Kodi nanunso ndinu wotsimikiza mofananamo kukanitsitsa kuyendera maganizo amene anthu ambiri akutsatira, pofuna kuti muteteze ubwenzi wanu ndi Mulungu?
Mfundo Zothandiza
it-1 846
Wopusa
Mawu akuti “wopusa” akagwiritsidwa ntchito m’Baibulo, amatanthauza munthu amene sachita zinthu mozindikira koma amachita zinthu zoipa zosagwirizana ndi mfundo zolungama za Mulungu, osati munthu amene ali ndi matenda amaganizo. Mawu a Chiheberi osiyanasiyana amene amanena za munthu wotereyu ndi kesilʹ (Miy 1:22), ʼewilʹ (Miy 12:15), na·valʹ (Miy 17:7), kutanthauza ‘munthu wopusa,’ komanso lets kutanthauza ‘munthu wonyoza’ (Miy 13:1). Mawu a Chigiriki akuti aʹphron amatanthauza “wopanda nzeru” (Lu 12:20), pomwe a·noʹe·tos (Aga 3:1) ndi mo·rosʹ (Mt 23:17; 25:2) amatanthauza “opusa.”
FEBRUARY 24–MARCH 2
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 2
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuikirapo Mtima Tikamaphunzira Baibulo Patokha?
‘Pitirizani Kuyenda M’choonadi’
16 Si tonse amene timakonda kuwerenga ndi kuphunzira. Koma Yehova amatilimbikitsa kuti ‘tizifunafuna’ komanso “kufufuza” kuti timvetse bwino mfundo zozama za choonadi. (Werengani Miyambo 2:4-6.) Tikamachita zimenezi, nthawi zonse timapindula. Pofotokoza zimene amachita akamawerenga Baibulo, Corey ananena kuti amaganizira zimene zili pavesi lililonse palokha. Iye anafotokoza kuti: “Ndimawerenga mawu a m’munsi aliwonse komanso kufufuza mavesi ena ofotokoza mfundo yofanana ndi ya vesilo ndiponso zinthu zina zowonjezereka. . . . Kugwiritsa ntchito njira imeneyi kumandithandiza kuti ndiphunzire zambiri.” Kaya timagwiritsa ntchito njira imeneyi kapena ina, timasonyeza kuti timakonda choonadi tikamapatula nthawi yathu komanso kuchita khama kuti tichiphunzire.—Sal. 1:1-3.
Nzeru Yeniyeni Ikufuula
3 Nzeru ingatanthauze luso lotha kugwiritsa ntchito zimene munthu akudziwa kuti asankhe bwino zochita. Komabe nzeru yeniyeni imaphatikizapo zambiri. Baibulo limati: “Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru. Kudziwa Woyera Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.” (Miy. 9:10) Choncho tikafuna kusankha zochita pa nkhani yofunika kwambiri tiyenera kudziwa mmene Yehova amaganizira pa nkhaniyo, komwe ndi “kudziwa Woyera Koposa.” Tingachite zimenezo pofufuza m’Baibulo komanso m’mabuku athu. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tili ndi nzeru yeniyeni.—Miy. 2:5-7.
4 Yehova yekha ndi amene angatipatse nzeru yeniyeni. (Aroma 16:27) N’chifukwa chiyani tikutero? Choyamba, iye pokhala Mlengi amadziwa chilichonse chokhudza zinthu zimene analenga. (Sal. 104:24) Chachiwiri, chilichonse chimene iye amachita chimasonyeza kuti iye ndi wanzeru. (Aroma 11:33) Chachitatu, onse amene amagwiritsa ntchito malangizo anzeru a Yehova zinthu zimawayendera bwino. (Miy. 2:10-12) Choncho kuti tipeze nzeru yeniyeni tiyenera kulola kuti mfundo za choonadi zimenezi zizititsogolera tikamasankha zochita komanso tikamachita zimene tasankhazo.
Achinyamata, Yesetsani Kulimbitsa Chikhulupiriro Chanu
2 Masiku ano anthu ambiri sakhulupirira kuti kuli Mulungu. Ngati ndinu wachinyamata wa Mboni kapena mukuphunzira Baibulo, mwina mumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndingamutsimikizire bwanji munthu kuti kuli Mlengi?’ Akhristufe timalimbikitsidwa kuti tiziganizira kwambiri zimene tamva kapena kuwerenga, kuti tidziwe ngati zili zoona kapena ayi. Paja Baibulo limati: “Kuganiza bwino kudzakuyang’anira.” Kuganiza bwino kungakuthandizeni kuti muzikana mfundo zabodza komanso kuti muzikhulupirira kwambiri Yehova.—Werengani Miyambo 2:10-12.
3 Kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chenicheni amafunika kudziwa zolondola zokhuza Mulungu. (1 Tim. 2:4) Choncho mukamaphunzira Baibulo kapena mabuku athu, musamathamange. Muzigwiritsa ntchito luso lanu lakuganiza n’cholinga choti muzindikire “tanthauzo” la zimene mukuwerengazo. (Mat. 13:23) M’nkhaniyi tiona kuti kuchita zimenezi kungakuthandizeni kutsimikizira kuti Yehova ndi amene analenga zinthu zonse komanso kuti Baibulo ndi Mawu ake.
Mfundo Zothandiza
it-1 1211 ¶4
Kukhulupirika
N’zotheka kukhala okhulupirika kwa Yehova, osati ndi mphamvu zathu, koma pokhapokha ngati timakhulupirira ndi kudalira mphamvu zake zopulumutsira. (Sl 25:21) Mulungu amalonjeza kuti adzakhala “chishango” komanso “malo achitetezo” kwa anthu okhulupirika. (Miy 2:6-8; 10:29; Sl 41:12) Chifukwa choti anthu okhulupirikawa nthawi zonse amayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Yehova, amakhala ndi moyo wosangalala zomwe zimawathandiza kuti azitha kukwaniritsa zolinga zawo. (Sl 26:1-3; Miy 11:5; 28:18) Komabe, Yobu anazindikira kuti, ngakhale kuti munthu wokhulupirika akhoza kuvutika chifukwa cha ulamuliro wa anthu oipa, n’kufa limodzi ndi oipawo, Yehova amakhala akudziwa kuti munthuyo anali wokhulupirika ndipo amamutsimikizira kuti adzamupatsa cholowa chake, adzakhala ndi mtendere m’tsogolo komanso adzalandira zinthu zabwino. (Yob 9:20-22; Sl 37:18, 19, 37; 84:11; Miy 28:10) Monga mmene zinalili ndi Yobu, munthu amaonedwa kuti ndi wofunika kwa Mulungu ngati ali wokhulupirika, osati ngati ali ndi chuma. (Miy 19:1; 28:6) Ana amene bambo awo ndi okhulupirika chonchi, amakhala ndi mwayi waukulu ndipo amakhala osangalala (Miy 20:7), komanso amalemekezedwa chifukwa cha chitsanzo chabwino ndi mbiri yabwino ya bambo awo.