Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr25 September tsamba 1-15
  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2025
  • Timitu
  • SEPTEMBER 1-7
  • SEPTEMBER 8-14
  • SEPTEMBER 15-21
  • SEPTEMBER 22-28
  • SEPTEMBER 29–OCTOBER 5
  • OCTOBER 6-12
  • OCTOBER 13-19
  • OCTOBER 20-26
  • OCTOBER 27–NOVEMBER 2
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2025
mwbr25 September tsamba 1-15

Malifalensi a ”Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”

© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

SEPTEMBER 1-7

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 29

Muzikana Miyambo Kapena Zikhulupiriro Zomwe Sizisangalatsa Mulungu

wp16.06 6, bokosi

Masomphenya Otithandiza Kumvetsa za Kumwamba

Anthu ambiri amaopa kwambiri mizimu yoipa. Iwo amatsirika zinthu zawo komanso kugwiritsa ntchito zithumwa pofuna kudziteteza ku ziwandazo. Komatu palibe chifukwa chochitira zimenezi. Zili choncho chifukwa Baibulo limatitsimikizira kuti: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Yehova, yemwe ndi Mulungu woona, ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana ndipo adzakutetezani mukamamudalira.

Kuti Yehova azikutetezani muyenera kuphunzira zimene amafuna n’kumatsatira zimene mwaphunzirazo. Mwachitsanzo, Akhristu akale amumzinda wa Efeso anasonkhanitsa mabuku awo azamatsenga n’kuwatentha. (Machitidwe 19:19, 20) Choncho kuti inunso Mulungu azikutetezani muyenera kutaya zithumwa, nsupa, mikuzi, mabuku azamatsenga kapena chilichonse chokhudzana ndi kukhulupirira mizimu.

w19.04 17 ¶13

Tizitsatira Mfundo za Choonadi Pakachitika Maliro

13 Ngati simukudziwa zoyenera kuchita pa miyambo inayake muyenera kupemphera kwa Yehova kuti akupatseni nzeru. (Werengani Yakobo 1:5.) Kenako mungafufuze m’mabuku athu. Mwinanso tingafunse akulu mumpingo wathu. Iwo sangakusankhireni zochita koma angakukumbutseni mfundo za m’Baibulo ngati zimene tikukambiranazi. Mukamachita zimenezi, mumaphunzitsa ‘mphamvu zanu za kuzindikira’ kuti muzitha “kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.”​—Aheb. 5:14.

w18.11 11 ¶12

“Ndidzayenda M’choonadi Chanu”

12 Miyambo ndi zikhalidwe zosemphana ndi Malemba. Achibale athu, anzathu akuntchito kapena akusukulu angafune kuti tichite nawo miyambo ina. Kodi tingapewe bwanji kuchita nawo miyambo ndi zikhalidwe zimene Mulungu amadana nazo? Chimene chingatithandize ndi kukumbukira mmene Yehova amaonera zinthuzo. Ndi bwino kuonanso nkhani za m’mabuku athu zofotokoza mmene maholide osiyanasiyana anayambira. Kukumbukira zifukwa za m’Malemba zimene zingatithandize kuti tizipewa maholidewa kumatithandiza kutsimikiza mumtima mwathu kuti tikuchita zinthu ‘zovomerezeka kwa Ambuye.’ (Aef. 5:10) Kukhulupirira Yehova ndiponso Mawu ake kumatithandiza kuti tisamaope anthu.​—Miy. 29:25.

Mfundo Zothandiza

it “Kuyamikira Mwachiphamaso” ¶1

Kuyamikira Mwachiphamaso

Ndi kuyamikira munthu mwaluso, kutamanda mwabodza, mosachokera pansi pa mtima kapena mokokomeza. Zimenezi zimachititsa kuti munthu amene akuyamikiridwayo azidziona kuti ndi wofunika kwambiri kapena azidzimva, zomwe zingamuwononge. Cholinga cha munthu amene amachita zimenezi ndi kufuna kuti azikondedwa kapena alandire zinazake kuchokera kwa amene akumutamandayo, kapena kuti azioneka kuti amadziwa kuyamikira anthu kapenanso kuti azilemekezedwa. Nthawi zambiri zimachititsa kuti amene akuyamikiridwayo akodwe mumsampha. (Miy 29:5) Kuyamikira munthu mwachiphamaso sikusonyeza nzeru yochokera kumwamba, koma nzeru ya dzikoli, ndipo munthu wotereyu amasonyeza kuti ndi wodzikonda, watsankho komanso wachinyengo. (Yak 3:17) Kulankhula zinthu mosachokera pansi pa mtima, kunama, kuyamikira mwachinyengo kapena kutamanda anthu, komanso kuchita zinthu zimene zingachititse kuti ena azidzimva, zonsezi sizisangalatsa Mulungu.​—2Ak 1:12; Aga 1:10; Aef 4:25; Akl 3:9; Chv 21:8.

SEPTEMBER 8-14

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 30

“Musandipatse Umphawi Kapena Chuma”

w18.01 24-25 ¶10-12

Kodi Tiyenera Kukonda Ndani Kuti Tikhale Osangalala?

10 N’zoona kuti tonsefe timafunikira ndalama. Zili choncho chifukwa zimatiteteza m’njira zina. (Mlal. 7:12) Koma funso n’lakuti, Kodi n’zotheka munthu amene amangopeza zofunika pa moyo zokha kukhaladi wosangalala? Inde. (Werengani Mlaliki 5:12.) Aguri mwana wa Yake anapempha Mulungu kuti: “Musandipatse umphawi kapena chuma. Ndidye chakudya chimene ndikufunika kudya.” M’pomveka kuti sankafuna kukhala mphawi wadzaoneni. Iye anafotokoza kuti sankafuna zimenezi chifukwa zikhoza kumuchititsa kuti abe n’kunyozetsa Mulungu. Koma n’chifukwa chiyani sankafuna kukhala ndi chuma? Iye anapitiriza kuti: “Kuti ndisakhute kwambiri n’kukukanani kuti: ‘Kodi Yehova ndani?’” (Miy. 30:8, 9) Mwina inuyo mwaonapo anthu amene amadalira kwambiri chuma chawo m’malo modalira Mulungu.

11 N’zosatheka kuti anthu amene amakonda ndalama asangalatse Mulungu. Paja Yesu ananena kuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” Ndipo asananene zimenezi ananena kuti: “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma unjikani chuma chanu kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge, ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba.”​—Mat. 6:19, 20, 24.

12 Anthu ambiri amaona kuti akamakhala moyo wosalira zambiri amasangalala komanso amakhala ndi nthawi yambiri yotumikira Yehova. M’bale wina dzina lake Jack, yemwe amakhala ku United States, anagulitsa nyumba ndiponso bizinezi yake n’cholinga choti azichita upainiya limodzi ndi mkazi wake. Iye anati: “Sizinali zophweka kuti tigulitse nyumba ndiponso malo athu okongola kwambiri. Koma kwa zaka zambiri ndinkaweruka kuntchito n’kubwera nditakhumudwa kwambiri chifukwa cha mavuto akuntchitoko. Mkazi wanga, yemwe anali mpainiya wokhazikika, nthawi zonse ankakhala wosangalala. Iye ankakonda kundiuza kuti, ‘Bwana wanga ndi wabwino kuposa mabwana onse.’ Popeza kuti panopa nanenso ndikuchita upainiya, tonse tikugwirira ntchito Yehova.”

w87 5/15 30 ¶8

Opani Yehova Ndipo Mudzakhala Achimwemwe

◆ 30:15, 16​—Kodi zitsanzo zimenezi mfundo yake ndi yotani?

Zitsanzo zimenezi zimasonyeza kuipa kwa dyera. Misundu imangokhalira kuyamwa magazi mwadyera mofanana ndi zimene munthu wadyera amachita pomangofunafuna ndalama kapena mphamvu. Mofananamo, Manda sakhuta, koma amakhalabe otseguka kuti anthu ambiri akufa aikidwemo. Mimba yosabereka imalirira ana. (Genesis 30:1) Nthaka youma imamwa madzi a mvula imene yangogwa, ndipo mwamsanga imawonekanso youma. Ndipo moto womwe wayatsa zinthu umafalikira n’kuyatsanso zinthu zina zimene zili pafupi. Ndi mmenenso zilili ndi munthu wadyera. Koma anthu amene amatsogoleredwa ndi nzeru yochokera kwa Mulungu, sachita zinthu modzikonda choncho.

w11 6/1 10 ¶4

Kodi Mungatani Kuti Muzigula Zinthu Mogwirizana Ndi Ndalama Zimene Mumapeza?

Muzisunga ndalama pang’onopang’ono musanagule kanthu. Ngakhale kuti zimaoneka ngati zachikale, ndi bwino kumasunga kaye ndalama musanagule chinthu. Imeneyi ndi njira ina yabwino kwambiri imene ingakuthandizeni kupewa kugwera m’mavuto azachuma. Kuchita zimenezi kumathandiza anthu ambiri kupewa kukhala ndi ngongole. Kumathandizanso kuti musamagule zinthu pa mtengo wokwera chifukwa nthawi zambiri mukagula chinthu pangongole, mumachigula modula. Baibulo limanena kuti nyerere “n’zanzeru” chifukwa “zimasonkhanitsa chakudya chawo m’chilimwe” kuti zidzachigwiritse ntchito m’tsogolo.​—Miyambo 6:6-8; 30:24, 25.

w24.06 13 ¶18

Pitirizani Kukhala Alendo a Yehova Mpaka Kalekale

18 Dzifunseni kuti: ‘Kodi nthawi zonse ndimangoganizira za ndalama komanso zimene ndingagule? Kodi ndikabwereka ndalama, ndimachedwa kubweza poganiza kuti amene wandibwereka ndalamayo sakuzifuna? Kodi kukhala ndi ndalama kumandichititsa kuti ndizidziona ngati wofunika koma n’kumalephera kuthandiza ena? Kodi ndimaona kuti abale ndi alongo ena ndi okonda ndalama chabe chifukwa choti ali ndi ndalamazo? Kodi ndimakonda kucheza ndi anthu olemera n’kumapewa anthu osauka?’ Tili ndi mwayi waukulu wokhala alendo a Yehova, choncho kuti tipitirize kukhala anzake tiyenera kupewa kukonda ndalama. Tikamachita zimenezi Yehova sadzatisiya.​—Werengani Aheberi 13:5.

Mfundo Zothandiza

w09 4/15 17 ¶11-13

Chilengedwe Chimasonyeza Nzeru za Yehova

11 Mbira ndi mtundu wina wa zolengedwa zazing’ono zimene zingatiphunzitse mfundo zofunika kwambiri. (Werengani Miyambo 30:26.) Nyamayi imaoneka ngati kalulu ndipo ili ndi makutu aafupi koma ozungulira, komanso miyendo yake ndi yaifupi. Nyama yaing’ono imeneyi imakhala m’matanthwe. Iyo ili ndi maso akuthwa kwambiri ndipo amaithandiza kuona msanga adani. Komanso m’matanthwe amene imakhala muli maenje ndi mphako zimene zimaiteteza kwa adani. Mwachibadwa, mbira zimakula bwino chifukwa chokhala pagulu, ndipo zimenezi zimapereka chitetezo komanso zimathandiza nyamazi kukhala zofunda m’nyengo yozizira.

12 Kodi tikuphunzira chiyani kwa mbira? Choyamba, onani kuti nyamayi imasamala kuti isagwidwe. Imagwiritsa ntchito maso ake akuthwa kuonera msanga adani ngakhale ali kutali, ndipo imakhala pafupi ndi dzenje kapena mphako, zimene zingathandize kupulumutsa moyo wake. Ifenso tiyenera kukhala ndi maso auzimu akuthwa kuti tizitha kuona zinthu zobisika zangozi zimene zili m’dziko la Satanali. Mtumwi Petulo analangiza Akhristu kuti: “Sungani maganizo anu, khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.” (1 Pet. 5:8) Yesu ali padziko lapansi, anakhalabe maso, inde watcheru, pamene Satana ankayesetsa kufuna kuswa umphumphu Wake. (Mat. 4:1-11) Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino kwa otsatira ake.

13 Njira imodzi imene tingakhalire maso ndiyo kuyesetsa kugwiritsa ntchito chitetezo chauzimu chimene Yehova wapereka kwa ife. Sitiyenera kunyalanyaza kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kupezeka pamisonkhano yachikhristu. (Luka 4:4; Aheb. 10:24, 25) Ndiponso mofanana ndi mbira zimene zimakula bwino chifukwa chokhala pagulu, tifunikira kukhala pafupi kwambiri ndi Akhristu anzathu kuti ‘tizilimbikitsana.’ (Aroma 1:12) Tikamagwiritsa ntchito chitetezo chimene Yehova wapereka, timasonyeza kuti tikugwirizana ndi zimene wamasalmo Davide analemba kuti: “Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye.”​—Sal. 18:2.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwbq nkhani na. 102

Kodi Kutchova Juga Ndi Tchimo?

Yankho la m’Baibulo

Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza mwatsatanetsatane zokhudza juga, mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuzindikira kuti Mulungu amaona kuti khalidweli ndi tchimo.​—Aefeso 5:17.a

● Anthu amatchova juga chifukwa cha dyera ndipo Mulungu amadana ndi khalidwe limeneli. (1 Akorinto 6:9, 10; Aefeso 5:3, 5) Kuti munthu wotchova juga awine, pamafunika kuti anzake aluze, koma Baibulo limaletsa kusirira zinthu za anthu ena mwansanje.​—Ekisodo 20:17; Aroma 7:7; 13:9, 10.

● Kutchova juga, ngakhale pang’ono pokha, kungachititse munthu kuti ayambe kukonda kwambiri ndalama.​—1 Timoteyo 6:9, 10.

Nthawi zambiri anthu otchova juga amadalira matsenga kapena mwayi. Komabe, Mulungu amaona kuti kukhulupirira zimenezi ndi kulambira mafano, komwe sikugwirizana ndi kulambira kumene iye amavomereza.​—Yesaya 65:11.

● M’malo molimbikitsa khalidwe lomapeza zinthu zomwe sitinazigwirire ntchito, Baibulo limatilimbikitsa kugwira ntchito mwakhama. (Mlaliki 2:24; Aefeso 4:28) Anthu omwe amatsatira malangizowa ‘amadya chakudya chimene achigwirira ntchito.’​—2 Atesalonika 3:10, 12.

● Kutchova juga kumalimbikitsa khalidwe la mpikisano, lomwe limaletsedwa m’Baibulo.​—Agalatiya 5:26.

SEPTEMBER 15-21

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 31

Kodi Tingaphunzire Chiyani Kuchokera pa Malangizo Achikondi a Mayi?

w11 2/1 19 ¶7-8

Muziphunzitsa Ana Anu Makhalidwe Abwino

Aphunzitseni zinthu zonse zokhudza kugonana. Ndi bwinodi kuti makolo azichenjeza ana awo nkhani zokhudza kugonana. (1 Akorinto 6:18; Yakobo 1:14, 15) Komabe Baibulo limanena kuti kugonana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, osati msampha wa Satana. (Miyambo 5:18, 19; Nyimbo ya Solomo 1:2) Choncho kuuza ana anu achinyamata zoipa zokhazokha zokhudza kugonana kungachititse kuti aziganiza molakwa za nkhaniyi komanso mosagwirizana ndi Malemba. Mtsikana wina wa ku France dzina lake Corrina ananena kuti: “Makolo anga akafuna kunena nkhani zokhudza kugonana, ankangonena za kuipa kwa chiwerewere ndipo zimenezi zinandichititsa kuganiza kuti kugonana ndi koipa nthawi zonse.”

Onetsetsani kuti mwauza ana anu mbali zonse zokhudza kugonana. Mayi wina wa ku Mexico, dzina lake Nadia, ananena kuti: “Pokambirana ndi ana anga nkhani zokhudza kugonana, nthawi zonse ndimawauza kuti kugonana ndi kwabwino chifukwa ndi mmene tinalengedwera. Yehova Mulungu anakonza zoti anthu azigonana ndiponso azisangalala. Koma ndimawauzanso kuti anthu okwatirana okha ndi amene ayenera kugonana. Ndimawauza kuti munthu angasangalale ngati akutsatira dongosolo la Yehova pa nkhaniyi kapena akhoza kupeza mavuto ngati sanatsatire dongosolo limeneli.”

ijwhf nkhani na. 4 ¶11-13

Mmene Mungathandizire Ana Anu pa Nkhani ya Mowa

Muziyamba ndi inuyo kukambirana ndi mwana wanu zokhudza mowa. Bambo wina wa ku Britain dzina lake Mark ananena kuti: “Mowa umasokoneza kwambiri ana. Tsiku lina ndinafunsa mwana wanga wamwamuna wa zaka 8 kuti afotokozepo maganizo ake ngati kumwa mowa n’kwabwino kapena ayi. Ndinkalankhula naye momasuka ngati kuti tikungocheza ndipo zimenezi zinathandiza kuti nayenso amasuke kunena maganizo ake pa nkhani ya mowa.”

Ngati nthawi zambiri mumakonda kunena za mavuto amene amakhalapo chifukwa cha mowa, zingathandize ana anu kudziwa kuopsa kwa mowa. Choncho potengera msinkhu wa mwana wanu, mukamakambirana nkhani zofunika pa moyo monga kupewa ngozi pamsewu komanso nkhani zokhudza kugonana, mungakambirane nayenso zokhudza kuopsa kwa mowa.

Muzikhala chitsanzo chabwino. Ana ali ngati thonje. Thonje likaviikidwa m’madzi, kaya akuda kapena oyera, limayamwa komanso kutengera mtundu wa madziwo. Ochita kafukufuku anapeza kuti nawonso ana amatengera kwambiri zimene makolo awo amakonda kuchita. Izi zikutanthauza kuti ngati inuyo mumaona kuti kumwa mowa ndi njira yokhayo yabwino yochepetsera nkhawa kapena mavuto anu, mwana wanunso amatengera zomwezo. Choncho muzikhala chitsanzo chabwino. Ndipo ngati mumamwa, muziyesetsa kumwa moyenera.

g17.6 9 ¶5

Mungaphunzitse Bwanji Ana Anu Kukhala Odzichepetsa?

Muziwalimbikitsa kukhala opatsa. Muzithandiza mwana wanu kudziwa kuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Mungachite zimenezi polemba mayina a anthu amene mungawathandize komanso mmene mungawathandizire monga kuwagulira zinthu, kuwapatsa ndalama ya thiransipoti kapena kuwakonzera zinthu zomwe zawonongeka. Kenako muzipita ndi mwana wanuyo pokathandiza anthuwo. Mwana wanu adzachita chidwi akamaona kuti mukusangalala chifukwa chothandiza ena. Adzaphunziranso kukhala wodzichepetsa poona zimene mumachita.​—Lemba lothandiza: Luka 6:38.

Mfundo Zothandiza

w92 11/1 11 ¶7-8

Maphunziro M’nthawi za m’Baibulo

7 Ku Isiraeli, ana ankaphunzitsidwa kuyambira ali aang’ono ndi makolo awo onse awiri. (Deuteronomo 11:18, 19; Miyambo 1:8; 31:26) Katswiri wina wa Baibulo dzina lake E. Mangenot analemba kuti: “Akangoyamba kumene kulankhula, mwana ankaphunzira mawu angapo a m’Chilamulo. Amayi ake ankamuwerengera vesi mobwerezabwereza, ndipo akaliloweza ankamuwerengera lina. Pambuyo pake, ankamupatsa mavesi olembedwa omwe anali atawaloweza. Pamapeto pake, ankamuphunzitsa kuwerenga ndipo akakula ankapitiriza kuphunzira malangizo achipembedzo mwa kuwerenga komanso kuganizira mozama lamulo la Ambuye.”

8 Zimenezi zikusonyeza kuti njira yaikulu yophunzitsira inali yoti aziloweza zinthu pamtima. Zinthu zomwe ankaphunzira zokhudza malamulo a Yehova komanso zomwe ankachita ndi anthu ake zinkafunika kukhazikika mumtima mwawo. (Deuteronomo 6:6, 7) Ankafunika kumaganizira mozama zimenezi. (Salimo 77:11, 12) Pofuna kuthandiza kuti achinyamata ndi akuluakulu aziloweza, ankagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Zimenezi zinkaphatikizapo mavesi olembedwa mwandakatulo potsatira afabeti ya Chiheberi (monga mmene zilili pa Miyambo 31:10-31); pogwiritsa ntchito mawu oyamba ndi chilembo chofanana kapena akamvekedwe kofanana; komanso pogwiritsa ntchito manambala ngati amene anagwiritsidwa ntchito m’mavesi omaliza a Miyambo chaputala 30. N’zochititsa chidwi kuti akatswiri ena amaona kuti Kalendala ya Gezer, yomwe ndi imodzi ya zolembedwa zakale kwambiri za Chiheberi, inalembedwa ndi mwana wa sukulu.

SEPTEMBER 22-28

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MLALIKI 1-2

Pitirizani Kuphunzitsa M’badwo Wotsatira

w17.01 27-28 ¶3-4

‘Zinthu Zimenezo Uziziphunzitsa kwa Anthu Okhulupirika’

3 Ambirife timakonda kutumikira Yehova komanso timakonda udindo umene tili nawo m’gululi. Koma vuto ndi lakuti munthu akamakalamba sakwanitsa kuchita zambiri ngati poyamba. (Mlal. 1:4) Masiku ano, zimenezi zimabweretsa mavuto ena kwa Akhristu. Panopa, ntchito m’gulu la Yehova yakula kwambiri ndipo ikufuna zambiri. Ntchito zatsopano zachititsa kuti papezeke njira zatsopano zogwirira ntchitozo ndipo njira zambiri ndi zamakono. Ndiyeno achikulire ena amavutika kuzolowera njira zatsopanozo. (Luka 5:39) Ngakhale zitakhala kuti achikulirewo sakuvutika, achinyamata amakhala ndi mphamvu zambiri kuposa achikulire. (Miy. 20:29) Choncho ndi bwino kuti achikulire aziphunzitsa achinyamata kuti akhale ndi maudindo akuluakulu.​—Werengani Salimo 71:18.

4 Akhristu ena amene ali ndi maudindo zimawavuta kuphunzitsa achinyamata. Ena amaopa kuti alandidwa udindo umene amaukonda. Pomwe ena amakayikira achinyamatawo ndipo amaganiza kuti sangachite bwino zinthu. Ndiye pali enanso amene amaganiza kuti alibe nthawi yophunzitsa munthu wina. Koma nawonso abale achinyamata ayenera kukhala odekha akaona kuti sakupatsidwa udindo winawake.

Mfundo Zothandiza

it “Mlaliki” ¶1

Mlaliki

Mawu a Chiheberi akuti Qo·heʹleth (omwe amatanthauza “wosonkhanitsa kapena wobweretsa pamodzi”) amafotokoza bwino udindo wa mfumu ya Aisiraeli mu ulamuliro wotsogoleredwa ndi Mulungu. (Mla 1:1, 12) Unali udindo wa wolamulira kuti azibweretsa anthu a Mulungu pamodzi kuti azilambira Mfumu yawo yeniyeni yomwe ndi Mulungu. (1Mf 8:1-5, 41-43, 66) Pa chifukwa chimenechi, anthuwo ankatha kudziwa kuti mfumuyo ndi yabwino kapena yoipa ngati ikuwatsogolera polambira Yehova kapena ayi. (2Mf 16:1-4; 18:1-6) Wosonkhanitsa, yemwe pa nthawiyo anali Solomo anali atagwira kale ntchito yaikulu yosonkhanitsa ku kachisi Aisiraeli komanso anzawo, ndiponso anthu osakhalitsa m’dzikolo. M’bukuli, ankafuna kuthandiza anthu a Mulungu kuti asamachite zinthu zoipa komanso zosathandiza zam’dzikoli , m’malomwake azichita zinthu zomwe zingasangalatse Mulungu amene anadzipereka kwa iye.

SEPTEMBER 29–OCTOBER 5

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MLALIKI 3-4

Muzilimbitsa Chingwe Chanu Chopotedwa ndi Zingwe Zitatu

ijwhf nkhani na. 10 ¶2-8

Mungatani Kuti Zipangizo Zamakono Zisamakusokonezeni?

● Kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono mwanzeru kukhoza kulimbitsa banja lanu. Mwachitsanzo, amuna ena ndi akazi awo, amagwiritsira ntchito zipangizozi polumikizana pa nthawi imene sali limodzi.

“Meseji yachidule yongonena kuti ‘ndimakukonda’ kapena ‘ndakusowa’ ingatanthauze zambiri ndipo imakupangitsa kumva bwino.”​—Jonathan.

● Kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono mopanda nzeru kukhoza kusokoneza banja lanu. Mwachitsanzo, anthu ena amangokhalira kucheza pa foni ndipo zimenezi zimachititsa kuti asamakhale ndi nthawi yokwanira yocheza ndi mwamuna kapena mkazi wawo.

“Sindikukayikira kuti pali nthawi zina pamene mwamuna wanga ankafuna atacheza nane, koma ankalephera chifukwa choti ndinkatanganidwa ndi foni.”​—Julissa.

● Anthu ena amaona kuti akhoza kumakambirana zinthu zofunika ndi mwamuna kapena mkazi wawo kwinakunso akugwiritsa ntchito chipangizo chawo chamakono. Koma Sherry Turkle, yemwe ndi katswiri wa zachikhalidwe anatsutsa mfundo imeneyi. Iye ananena kuti “n’zosatheka kumachita zinthu ziwiri pa nthawi imodzi, ndipo tikamachita zinthu zingapo pa nthawi imodzi m’pamene zambiri zimawonongeka.”

“Ndimasangalala kwambiri kucheza ndi mwamuna wanga akakhala kuti sakuchita zinthu zina. Koma ndikamacheza naye, iyeyo n’kumatanganidwa ndi foni, zimakhala ngati foniyo ndi yofunika kwambiri kuposa ineyo.”​—Sarah.

Mfundo yofunika kwambiri: Mmene mumagwiritsira ntchito zipangizo zamakono zingachititse kuti banja lanu likhale lolimba kapena lisokonezeke.

w23.05 23-24 ¶12-14

Musazimitse “Lawi la Ya”

12 Kodi anthu okwatirana angatsanzire bwanji Akula ndi Purisika? Taganizirani zinthu zambiri zimene inuyo monga mwamuna kapena mkazi, mumafunika kuchita. Kodi n’zotheka kuti muzichitira limodzi zina mwa zinthu zimenezi monga banja, osati aliyense payekha? Mwachitsanzo, Akula ndi Purisika ankalalikira limodzi. Kodi inunso nthawi zambiri mumakonza zoti muzilalikira limodzi? Akula ndi Purisika ankagwiranso ntchito limodzi. Mwina inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu simugwira ntchito yofanana, koma kodi mungamagwire limodzi ntchito zapakhomo? (Mlal. 4:9) Mukamathandizana ntchito inayake, mumagwirizana kwambiri ndiponso mumapeza mpata wocheza. A Robert ndi a Linda akhala m’banja kwa zaka zoposa 50. A Robert anati: “Kunena zoona, sitipeza nthawi yambiri yochitira limodzi zinthu zosangalatsa. Koma ndikamatsuka mbale, mkazi wanga n’kumapukuta kapena ndikamalima panja, iye n’kubwera kudzandithandiza, ndimasangalala kwambiri. Kuchitira zinthu limodzi kumatithandiza kuti tizikhala ogwirizana ndipo chikondi chathu chimapitiriza kukula.”

13 Komabe, muzikumbukira kuti kungokhala limodzi, sikutanthauza kuti nthawi zonse muzichita zinthu mogwirizana. Mayi wina wa pabanja ku Brazil ananena kuti: “Masiku ano, pali zinthu zambiri zosokoneza, moti ndaona kuti tikhoza kugwera mumsampha womaganiza kuti timachitira zinthu limodzi chabe chifukwa choti timakhala nyumba imodzi. Ndaphunzira kuti kuwonjezera pa kukhala limodzi, timafunikiranso kumachita chidwi ndi mnzathuyo.” Taonani zimene Bruno ndi mkazi wake Tays amachita kuti aliyense azichita chidwi ndi mnzake. Iye anati: “Pa nthawi yathu yocheza, timaika patali mafoni athu n’kumangocheza basi.”

14 Koma bwanji ngati inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu simusangalala kuchitira zinthu limodzi? Mwina mumakonda zinthu zosiyana kapenanso mumangokhalira kuyambana, ndiye kodi mungatani? Taganizirani za moto, womwe tinautchula kumayambiriro kuja. Motowu sumangofikira kuyaka mwamphamvu. Umafunika kusonkhezera pang’onopang’ono, kenako n’kumaika nkhuni zazikulu. Mofanana ndi zimenezi, bwanji osayamba ndi kumapeza nthawi yochepa tsiku lililonse yochitira zinthu limodzi? Muzionetsetsa kuti muzichita zinthu zomwe nonse mumasangalala nazo, osati zimene zingachititse kuti muyambe kukangana. (Yak. 3:18) Kuyamba mwapang’onopang’ono kungathandize kuti mukulitse chikondi chanu.

w23.05 21 ¶3

Musazimitse “Lawi la Ya”

3 Kuti asazimitse “lawi la Ya,” onse, mwamuna ndi mkazi ayenera kuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. Kodi zimenezi zimathandiza bwanji banja lawo? Anthu okwatirana akamaona kuti ubwenzi wawo ndi Atate wawo wakumwamba ndi wofunika kwambiri, amakhala okonzeka kutsatira malangizo ake, zimene zimawathandiza kupewa komanso kulimbana ndi mavuto omwe angachititse kuti chikondi chawo chichepe. (Werengani Mlaliki 4:12.) Anthu omwe ali pa ubwenzi ndi Yehova amayesetsa kumutsanzira ndipo amakhala ndi makhalidwe monga kukoma mtima, kuleza mtima komanso kukhululuka. (Aef. 4:32–5:1) Anthu okwatirana omwe amasonyeza makhalidwewa siziwavuta kuti azikondana kwambiri. Mlongo wina dzina lake Lena, yemwe wakhala pabanja kwa zaka zoposa 25, anati: “Zimakhala zosavuta kukonda komanso kulemekeza munthu yemwe amakonda Yehova.”

Mfundo Zothandiza

it “Chikondi” ¶39

Chikondi

“Nthawi Yachikondi.” Yehova amakonda anthu onse kupatulapo amene amachita zoipa komanso amene amasonyeza kuti amadana naye. Mulungu amasiya kusonyeza chikondi chake kwa anthu amenewa. Yehova Mulungu ndi Yesu amakonda chilungamo ndipo amadana ndi kusamvera malamulo. (Sl 45:7; Ahe 1:9) Anthu amene amadana kwambiri ndi Mulungu ndi anthu okhawo omwe safunika kusonyezedwa chikondi ngakhale pang’ono. Kunena zoona sizingaphule kanthu kupitiriza kukonda anthu ngati amenewa chifukwa sangayamikire chikondi cha Mulungu. (Sl 139:21, 22; Yes 26:10) Choncho pakakhala zifukwa zomveka, Mulungu sawakonda ndipo nthawi idzafika yoti adzawawononge.​—Sl 21:8, 9; Mla 3:1, 8.

OCTOBER 6-12

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MLALIKI 5-6

Kodi Timasonyeza Bwanji Kuti Timalemekeza Mulungu Wathu Wamkulu?

w08 8/15 15-16 ¶17-18

Lemekezani Yehova mwa Kusonyeza Ulemu

17 Tifunikira kusonyeza ulemu wapadera polambira Yehova. Lemba la Mlaliki 5:1 limati: “Samalira phazi lako popita ku nyumba ya Mulungu.” Mose ndi Yoswa analamulidwa kuvula nsapato zawo pamalo opatulika. (Eks. 3:5; Yos. 5:15) Iwo amafunika kuchita zimenezi posonyeza ulemu. Ansembe a Chiisiraeli analamulidwa kuvala zovala za miyendo kuti ‘abise maliseche.’ (Eks. 28:42, 43) Zimenezi zinathandiza kuti azivala modzilemekeza akamatumikira pa guwa la nsembe. Aliyense m’banja la wansembe amafunikira kutsatira malamulo a Mulungu okhudza kudzilemekeza.

18 Motero, monga olambira a Yehova tifunikira kusonyeza ulemu m’mbali zonse za moyo wathu. Kuti ena azitipatsa ulemu ifenso tiyenera kuwapatsa ulemu. Tisasonyeze ulemu mwachiphamaso kapena mongodzionetsera chabe. Koma uzikhala ulemu wochokera mu mtima chifukwa Mulungu amaona mumtima. (1 Sam. 16:7; Miy. 21:2) Tiyenera kukhala aulemu nthawi zonse, m’zochita zathu ndi pochita zinthu ndi ena. Ndipo tiyeneranso kumadzilemekeza. Ndithudi, tizisonyeza ulemu polankhula ndi pochita zinthu zina. Pankhani ya khalidwe lathu, kavalidwe ndi kudzikongoletsa, tifunikira kutsatira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu.” (2 Akor. 6:3, 4) Mwa njira imeneyi ‘timakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu, Mulungu, m’zinthu zonse.’​—Tito 2:10.

w09 11/15 11 ¶21

Kuphunzira Baibulo Kungathandize Kuti Mapemphero Anu Azikhala Atanthauzo

21 Yesu anapemphera mwaulemu ndiponso ndi chikhulupiriro chonse. Mwachitsanzo asanaukitse Lazaro, “Yesu anakweza maso ake kumwamba ndi kunena kuti: ‘Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse.’” (Yoh. 11:41, 42) Kodi mapemphero anu amasonyeza ulemu ndi chikhulupiriro chotero? Mukawerenga bwinobwino pemphero la Yesu lachitsanzo, mudzaona kuti mbali zazikulu zimene anatchula ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova, kubwera kwa Ufumu wake ndi kuchitika kwa chifuniro chake. (Mat. 6:9, 10) Ndiyeno ganizirani za mapemphero anu. Kodi amasonyeza kuti inuyo mumafunadi Ufumu wa Yehova, kuchita chifuniro chake ndiponso mumafuna kuona dzina lake loyera litayeretsedwa? Mapemphero anu ayenera kusonyeza zimenezi.

w17.04 6 ¶12

“Uzikwaniritsa Zinthu Zimene Walonjeza”

12 Koma kubatizidwa ndi chiyambi chabe. Munthu akabatizidwa ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene analonjeza kwa Mulungu. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zinthu zakhala zikuyenda bwanji kuyambira pamene ndinabatizidwa? Kodi ndikutumikirabe Yehova ndi mtima wonse? (Akol. 3:23) Kodi ndimapemphera, kuwerenga Mawu a Mulungu, kusonkhana komanso kulalikira nthawi zonse? Kapena kodi ndafooka pang’ono pa zinthu zimenezi? Paja mtumwi Petulo anati tiyenera “kuwonjezera pa chikhulupiriro chathu kudziwa zinthu, kudziletsa, kupirira ndiponso kudzipereka kwa Mulungu.” (Werengani 2 Petulo 1:5-8.) Makhalidwe amenewa angatithandize kuti tizitumikirabe Mulungu mwakhama.

Mfundo Zothandiza

w20.09 31 ¶3-5

Mafunso Ochokera Kwa Owerenga

Lemba la Mlaliki 5:8 limanena za olamulira amene amapondereza osauka komanso kuwachitira zopanda chilungamo. Wolamulira ayenera kukumbukira kuti pali munthu winanso amene amamuyang’anira, yemwe ndi waudindo waukulu kuposa iyeyo. Ndiponso pamwamba pa munthu waudindo waukuluyu, pangakhale enanso a maudindo aakulu kwambiri. Chomvetsa chisoni n’chakuti m’maboma a anthu, olamulira onsewa amakhala achinyengo ndipo anthu amavutika ndi katangale komanso zinthu zopanda chilungamo.

Ngakhale zili choncho, sitiyenera kutaya mtima chifukwa tikudziwa kuti Yehova, amaona zimene anthu a maudindo aakulu m’maboma a anthu amachita. Choncho tingapemphe Yehova kuti atithandize komanso tingathe kumutulira nkhawa zathu. (Sal. 55:22; Afil. 4:6, 7) Timadziwa kuti “maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.”​—2 Mbiri 16:9.

Choncho lemba la Mlaliki 5:8 limatikumbutsa zomwe zimachitikadi m’maboma a anthu, kuti nthawi zonse munthu waudindo waukulu, amakhalanso ndi wina waudindo waukulu kuposa iyeyo. Chofunika kwambiri n’chakuti vesili lingatithandize kuganizira mfundo yakuti Yehova ndi amene ali wamkulu kwambiri, iye ndi Wolamulira Wamkulu. Panopa Yehova akulamulira kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Yehova yemwe ndi Wamphamvuyonse amaona zinthu zonse komanso munthu aliyense ndipo iye komanso Mwana wake ndi achilungamo.

OCTOBER 13-19

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MLALIKI 7-8

‘Muzipita Kunyumba Yamaliro’

it “Kulira” ¶9

Kulira

Nthawi Yolira. Lemba la Mlaliki 3:1, 4 limanena kuti pali “nthawi yolira ndi nthawi yoseka. Nthawi yolira mofuula ndi nthawi yovina.” Poganizira mfundo yakuti anthu onse amafa, munthu wanzeru amapita “kunyumba yamaliro” m’malo mopita kunyumba yamadyerero. (Mla 7:2, 4; yerekezerani ndi Miy 14:13.) Choncho munthu wanzeru amagwiritsa ntchito mwayi umenewu posonyeza ena chifundo komanso kuwalimbikitsa m’malo mopita kosangalala. Zimenezi zimamuthandiza kuti nayenso azikumbukira kuti tsiku lina adzafa ndipo afunika kumachita zinthu zoyenera pamaso pa Mlengi wake.

w19.06 23 ¶15

Tizithandiza Anthu Amene Ali ndi Nkhawa

15 M’bale wina dzina lake William, yemwe mkazi wake anamwalira zaka zingapo zapitazo, ananena kuti: “Ndimayamikira kwambiri anthu akafotokoza zinthu zabwino zokhudza mkazi wanga. Zimanditsimikizira kuti anthu ankamukonda komanso kumulemekeza ndipo zimandilimbikitsa kwambiri. Zili choncho chifukwa mkazi wanga anali wamtengo wapatali kwa ine ndipo ndinkamukonda kwambiri.” Mlongo wina wamasiye dzina lake Bianca anati: “Ndimalimbikitsidwa anthu ena akapemphera nane limodzi komanso kundiwerengera malemba. Zimandithandiza anthuwo akanena zinthu zabwino zokhudza mwamuna wanga kapena akamamvetsera ndikamawauza za iyeyo.”

w17.07 16 ¶16

“Lirani ndi Anthu Amene Akulira”

16 Kupemphera ndi Akhristu anzathu amene aferedwa kapena kuwapempherera kumathandizanso kwambiri. Pa nthawi yovuta ngati imeneyi munthu akhoza kuvutika kuti anene zomveka m’pemphero. Koma ngakhale atapemphera uku akunjenjemera kapena kulira, akhoza kuthandiza kwambiri munthu woferedwayo. Mlongo Dalene, amene tamutchula uja, ananena kuti: “Nthawi zina alongo akabwera kudzandilimbikitsa ndinkawapempha kuti apemphere. Nthawi zambiri akamayamba pempherolo ankavutika koma kenako mawu awo ankayamba kumveka bwinobwino ndipo mapemphero awo ankakhala olimbikitsa kwambiri. Ndimalimbikitsidwa ndikaganizira chikhulupiriro chawo, chikondi chawo komanso mtima wawo woganizira ena.”

w17.07 16 ¶17-19

“Lirani ndi Anthu Amene Akulira”

17 Anthu amamva chisoni mosiyanasiyana. Choncho ndi bwino kupitiriza kulimbikitsa munthu ngakhale achibale kapena anzake amene ankamulimbikitsa pa nthawi ya maliro atachoka. Paja “bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Abale ndi alongo ayenera kulimbikitsa munthu mpaka nthawi imene chisoni chake chachepa.​—Werengani 1 Atesalonika 3:7.

18 Tizikumbukira kuti anthu oferedwa akhoza kumvanso chisoni pa nthawi inayake pa chaka, akamva nyimbo inayake, kuona zithunzi, kuchita zinthu zina komanso akamva fungo kapena phokoso linalake. Munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wamwalira angavutike kwambiri akayambiranso kuchita zinthu zina payekha monga kupita kumsonkhano kapena ku Chikumbutso. M’bale wina anati: “Ndinkaona kuti ndidzavutika kwambiri likadzafika tsiku limene tinakwatirana ndipo zinalidi zovuta. Koma abale ndi alongo ena anakonza zoti ndikacheze ndi anzanga apamtima pa tsikulo n’cholinga choti ndisakhale ndekha.”

19 Koma tizikumbukiranso kuti anthu amene aferedwa amafunikira kuwalimbikitsa nthawi zonse, osati pa nthawi zapadera zokha. Junia ananena kuti: “Anthu akacheza nawe ndiponso kukuthandiza, ngakhale pamene palibe zifukwa zapadera, umalimbikitsidwa kwambiri.” N’zoona kuti sitingathetseretu chisoni cha munthu amene waferedwa koma tikhoza kumulimbikitsa m’njira zosiyanasiyana. (1 Yoh. 3:18) Gaby anati: “Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha akulu achikondi amene ankandithandiza kwambiri mwamuna wanga atamwalira. Ndinkamva ngati Yehova wandikumbatira mwachikondi.”

Mfundo Zothandiza

w23.03 31 ¶18

“Mwakutero, Onse Adzadziwa Kuti Ndinu Ophunzira Anga”

18 Nthawi zina tingaone kuti n’zofunika kuti tikambirane ndi Mkhristu mnzathu yemwe watilakwira. Koma choyamba tingachite bwino kudzifunsa mafunso monga: ‘Kodi ndikudziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyi?’ (Miy. 18:13) ‘Kodi n’kutheka kuti iye sanandilakwire mwadala?’ (Mlal. 7:20) ‘Kodi inenso ndinayamba ndalakwitsapo mwanjira imeneyi?’ (Mlal. 7:21, 22) ‘Ngati nditakambirana naye, kodi ndichititsa kuti nkhaniyi ikule kwambiri m’malo moti ithe?’ (Werengani Miyambo 26:20.) Pambuyo poganizira mafunso amenewa, tingaone kuti chifukwa chokonda m’bale wathuyo tingonyalanyaza nkhaniyo.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwfq nkhani na. 50

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Zotani pa Nkhani ya Mwambo wa Maliro

Malo: Banja loferedwa ndi limene limasankha malo ochitira mwambo wa maliro. Ena angasankhe ku Nyumba ya Ufumu, kunyumba kwawo, malo otenthera mitembo kapena kumanda.

Mwambo wa maliro: Pamwambowu pamakambidwa nkhani yofotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza imfa komanso zoti akufa adzauka. (Yohane 11:25; Aroma 5:12; 2 Petulo 3:13) Wokamba nkhaniyi angafotokozenso makhalidwe abwino amene munthu womwalirayo anali nawo komanso zimene anthu ena angaphunzirepo.​—2 Samueli 1:17-27.

Pamwambowu pangaimbidwenso nyimbo yochokera M’malemba. (Akolose 3:16) Mwambowu umatha ndi pemphero lotonthoza.​—Afilipi 4:6, 7.

Malipiro: Sitimauza anamfedwa kuti apereke ndalama zolipirira wokamba nkhani ya maliro. Komanso mofanana ndi mmene timachitira pamisonkhano yathu, sitiyendetsa mbale ya zopereka pamwambo wamaliro.​—Mateyu 10:8.

Anthu oyenera kupezekapo: Mofanana ndi mmene zimakhalira ndi misonkhano yathu, anthu onse ngakhale omwe si a Mboni ndi olandiridwa pamwambo wa maliro womwe umachitikira ku Nyumba ya Ufumu.

OCTOBER 20-26

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MLALIKI 9-10

Muziona Mavuto Anu Moyenera

w13 8/15 14 ¶20-21

‘Musakwiyire Yehova’

20 Dziwani zimene zayambitsa mavuto anu. Kudziwa zimenezi n’kofunika chifukwa chakuti nthawi zina timadzibweretsera tokha mavuto. Ngati izi zitachitika, ndi bwino kungovomereza. (Agal. 6:7) Si bwino kuimba Mulungu mlandu pa mavuto athu. N’chifukwa chiyani si nzeru kuimba Mulungu mlandu? Tiyerekeze kuti munthu wina akuyendetsa galimoto yothamanga kwambiri. Ndiye atafika pakona, sakuchepetsa liwiro ndipo akuchita ngozi. Kodi munthuyo angaimbe mlandu kampani imene inakonza galimotoyo? Ayi. N’chimodzimodzinso ndi Yehova. Potilenga, iye anatipatsa ufulu wosankha. Komanso watipatsa malangizo othandiza kuti tizisankha zinthu mwanzeru. Choncho, palibe chifukwa choimbira mlandu Mlengi wathu ngati ifeyo talakwitsa zinazake n’kukumana ndi mavuto?

21 Sikuti mavuto onse amabwera chifukwa choti ifeyo talakwitsa zinazake. Mavuto ena amangobwera chifukwa cha “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka.” (Mlal. 9:11) Tisamaiwalenso kuti mavuto anayamba chifukwa cha Satana Mdyerekezi. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:9) Mdani wathu ndi Satanayo osati Yehova.​—1 Pet. 5:8.

w19.09 5 ¶10

Yehova Amaona Kuti Atumiki Ake Odzichepetsa Ndi Amtengo Wapatali

10 Kudzichepetsa kumathandizanso kuti zinthu zisamatisowetse mtendere. Kunena zoona, anthufe timakumana ndi zinthu zina zimene zimaoneka kuti si zachilungamo. Mwachitsanzo, Solomo yemwe anali mfumu yanzeru ananena kuti: “Ndaonapo antchito atakwera pamahatchi, koma akalonga akuyenda pansi ngati antchito.” (Mlal. 10:7) Nthawi zina anthu aluso kwambiri sayamikiridwa pomwe amene ali ndi luso lochepa ndi amene amalemekezedwa. Koma Solomo ananena kuti ndi nzeru kungovomereza mmene zinthu zilili m’malo molimbana nazo. (Mlal. 6:9) Tikakhala odzichepetsa, sitingavutike kuvomereza mmene zinthu zilili m’malo mokakamira kuti zisinthe.

w11 10/15 8 ¶1-2

Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?

M’BAIBULO muli mawu ambiri osonyeza kuti Yehova samangofuna kuti tikhale ndi moyo, koma kuti tizisangalala nawo. Mwachitsanzo, lemba la Masalimo 104:14, 15 limanena kuti Yehova amachititsa “kuti chakudya chituluke m’nthaka, komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu. Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta, komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.” Yehova ndi amene amatipatsa chakudya chimene chimatithandiza kuti tizikhala ndi moyo. Amameretsa mbewu kuti tipeze chakudya, mafuta ndi vinyo. Ngakhale kuti vinyo sali m’gulu la zinthu zofunika kwambiri pa moyo, ‘amachititsa mtima kusangalala.’ (Mlal. 9:7; 10:19) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala ndiponso kuti mitima yathu izikhala yodzaza ndi “chimwemwe.”​—Mac. 14:16, 17.

2 Choncho tisamaone ngati talakwitsa ngati nthawi zina timakonza nthawi yosangalala. Mwina timakonza zokaona “mbalame zam’mlengalenga” ndi “maluwa akutchire,” komanso kuchita zinthu zina zimene zimatitsitsimula. (Mat. 6:26, 28; Sal. 8:3, 4) Kukhala ndi moyo wosangalala “ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Mlal. 3:12, 13) Kudziwa kuti nthawi yosangalala ndi mphatso, kungatithandize kuti tiziigwiritsa ntchito m’njira yosangalatsa amene anaipereka.

Mfundo Zothandiza

it “Miseche, Kunenera Ena Zoipa” ¶4, 8

Miseche, Kunenera Ena Zoipa

Miseche ikhoza kuchititsa kuti anthu ayambe kunenera ena zoipa ndipo zimenezi zingawononge kwambiri munthu wonenera ena zoipayo. Mawu anzeru amene amapezeka pa lemba la Mlaliki 10:12-14 amatsimikizira kuti zimenezi ndi zoona. Mawuwa amati: “Milomo ya munthu wopusa imamubweretsera mavuto. Mawu oyamba otuluka mʼkamwa mwake amakhala opusa ndipo mawu ake omaliza amakhala misala yobweretsa chiwonongeko. Ngakhale zili choncho, munthu wopusa amangolankhulabe.”

Ngakhale kuti nthawi zina miseche singakhale yoipa kwambiri (koma ikhoza kupangitsa kuti anthu ayambe kunenera ena zoipa), nthawi zonse kunenera ena zoipa kungawononge mbiri ya munthu komanso nthawi zonse kumakhumudwitsa komanso kuyambanitsa anthu. Munthu akhoza kukhala ndi zolinga zabwino kapena zoipa pochita zimenezi. Koma kaya ali ndi zolinga zotani, munthu wonenera ena zoipa amadzipangitsa kukhala mdani wa Mulungu, chifukwa “aliyense amene amayambitsa mikangano pakati pa abale,” Mulungu amanyansidwa naye. (Miy 6:16-19) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kunenera ena zoipa” ndi di·aʹbo·los. Mawu amenewa amagwiritsidwanso ntchito m’Baibulo ponena za Satana “Mdyerekezi” yemwe ndi woneneza wamkulu, wa Mulungu. (Yoh 8:44; Chv 12:9, 10; Ge 3:2-5) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu amene amaneneza anzawo amakhala kuti akutengera Satana.

OCTOBER 27–NOVEMBER 2

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MLALIKI 11-12

Muzikhala Athanzi Komanso Osangalala

g 3/15 13 ¶6-7

Kamphepo Kayaziyazi Komanso Dzuwa Ndi Mankhwala

Dzuwa nalonso limapha tizilombo toyambitsa matenda. Magazini ina inanena kuti “tizilombo tambiri toyambitsa matenda monga chimfine, timafa tikawombedwa ndi dzuwa.”​—Journal of Hospital Infection.

Popeza taona kuti kamphepo kayaziyazi komanso dzuwa ndi mankhwala, si bwino kumangobindikira m’nyumba. Muzikonda kukhala panja nthawi zina n’kumaothera dzuwa komanso kupitidwa kamphepo kayaziyazi. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamadwaledwale.

w23.02 21 ¶6-7

Tiziyamikira Mphatso ya Moyo Imene Mulungu Anatipatsa

6 Ngakhale kuti Baibulo si buku lofotokoza za thanzi kapena za zakudya, limatithandiza kudziwa mmene Yehova amaganizira pa nkhanizi. Mwachitsanzo, iye amatilimbikitsa kuti ‘tiziteteza thupi lathu’ ku zinthu zomwe zingaliwononge. (Mlal. 11:10) Baibulo limaletsa kudya kwambiri komanso kumwa kwambiri mowa chifukwa zimenezi zingawononge moyo. (Miy. 23:20) Yehova amayembekezera kuti tizidziletsa pa nkhani ya kuchuluka kwa chakudya komanso mowa.​—1 Akor. 6:12; 9:25.

7 Tingasonyeze kuti timayamikira kwambiri mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa pogwiritsa ntchito bwino luso loganiza. (Sal. 119:99, 100; werengani Miyambo 2:11.) Mwachitsanzo, tingagwiritse ntchito luso loganiza pa nkhani ya zakudya zomwe timasankha. Ngati timakonda chakudya chinachake koma timadziwa kuti tikadya chimatidwalitsa, kuganiza bwino kumatithandiza kuti tizichipewa. Tingasonyezenso kuti ndife oganiza bwino tikamagona mokwanira, kuchita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse, kukhala aukhondo komanso kusamalira pakhomo pathu.

w24.09 2 ¶2-3

“Muzichita Zimene Mawu Amanena”

2 N’chifukwa chiyani anthu amene timalambira Mulungu timakhala osangalala? Pali zifukwa zambiri, koma chifukwa chimodzi n’chakuti timawerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse ndipo timayesetsa kutsatira zimene timaphunzira.​—Werengani Yakobo 1:22-25.

3 ‘Kuchita zimene Mawu’ a Mulungu amanena kumatithandiza m’njira zambiri. Choyamba, tikamachita zimene timaphunzira timasangalatsa Yehova. Ndipo tikadziwa kuti tikusangalatsa Yehova timasangalala. (Mlal. 12:13) Tikamagwiritsa ntchito zimene timawerenga m’Mawu a Mulungu timakhala ndi mabanja abwino komanso timagwirizana ndi Akhristu anzathu. N’kutheka kuti inunso mwaona kale kuti zimenezi ndi zoona. Kuwonjezera pamenepo, timapewa mavuto amene anthu omwe satsatira mfundo za Yehova amakumana nawo. Timagwirizana ndi zimene Mfumu Davide inanena. Atanena za malamulo ndi zigamulo za Yehova, anamaliza nyimbo yake ndi mawu akuti: “Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.”​—Sal. 19:7-11.

Mfundo Zothandiza

it “Kuuzira” ¶10

Kuuzira

Maumboni amasonyeza kuti amuna amene Mulungu anawagwiritsa ntchito polemba Baibulo sankachita zinthu ngati maloboti, kumangolemba uthenga umene akuuzidwa. Timawerenga za mtumwi Yohane kuti Mulungu anamuuzira zokhudza Chivumbulutso kudzera mwa mngelo “pogwiritsa ntchito zizindikiro” ndipo kenako Yohaneyo “anachitira umboni mawu amene Mulungu anapereka ndiponso umboni umene Yesu Khristu anapereka, kutanthauza zonse zimene anaona.” (Chv 1:1, 2) ‘Atadzazidwa ndi mzimu woyera,’ Yohane anapezeka kuti ali “m’tsiku la Ambuye” ndipo anauzidwa kuti: “Zimene ukuona, uzilembe mumpukutu.” (Chv 1:10, 11) Choncho zikuoneka kuti Mulungu anaona kuti zingakhale bwino kwambiri kuti anthu amene analemba Baibulo azigwiritsa ntchito luso lawo la kuganiza posankha mawu komanso mmene angafotokozere masomphenya amene ankaona (Hab 2:2), kwinaku akuwatsogolera komanso kuwathandiza kuti zimene akulembazo zikhale zolondola, zoona komanso zogwirizana ndi cholinga chake. (Miy 30:5, 6) Wolemba Baibulo aliyense ankafunika kuyesetsa kuchita mbali yake ndipo zimenezi zinaonekera bwino pa mawu opezeka pa Mlaliki 12:9, 10, omwe amafotokoza kuti anaganizira mozama, kufufuza mosamala kwambiri komanso kuika mwandondomeko “mawu osangalatsa ndipo analemba mawu olondola a choonadi.”​—Yerekezerani ndi Lu 1:1-4.

[Mawu a M’munsi]

a M’Baibulo, kutchova juga kumatchulidwa mwachindunji kamodzi kokha pa nkhani yonena za asilikali a Roma omwe anachita maere, kapena kuti “anatchova juga” pa chovala cha Yesu.​—Mateyu 27:35; Yohane 19:23, 24; Contemporary English Version; Good News Translation.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena