FEBRUARY 23–MARCH 1
YESAYA 38-40
Nyimbo Na. 4 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
M’busa wa m’nthawi ya Aisiraeli wanyamula nkhosa mwachikondi pachifuwa chake
1. “Iye Adzasamalira Gulu la Nkhosa Zake Ngati Mʼbusa”
(10 min.)
Yehova wapereka komanso kuteteza Mawu ake, Baibulo, kuti tikhale naye pa ubwenzi (Yes 40:8; w23.02 2-3 ¶3-4)
Iye amatisamalira mwachikondi (Yes 40:11; cl 70 ¶7-mwbr)
Amatidziwa aliyense payekha komanso kutithandiza kupirira mavuto athu (Yes 40:26-29; w18.01 8 ¶4-6)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi zimene lemba la Yesaya 40:11 limafotokoza zokhudza m’busa, zimakhudza bwanji mmene mumaonera Yehova?
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 40:3—Kodi mawu a palembali anakwaniritsidwa bwanji Yesu asanayambe utumiki wake padzikoli? (ip-1 400 ¶7)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 40:21-31 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pezani mpata wofotokozera munthu mfundo inayake imene mwaphunzira pamisonkhano posachedwapa. (lmd phunziro 4, mfundo 3)
5. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pezani mpata wofotokozera munthu mfundo inayake imene mwaphunzira pamisonkhano posachedwapa. (lmd phunziro 4, mfundo 4)
6. Ulendo Wobwereza
(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 7, mfundo 5)
7. Kuphunzitsa Anthu
(5 min.) lff phunziro 18 zomwe taphunzira, kubwereza, komanso zolinga. Gwiritsani ntchito nkhani imene ili pagawo lakuti “Onani Zinanso” pothandiza wophunzira wanu kumvetsa chikondi chimene a Mboni za Yehova amasonyezana. (lmd phunziro 11, mfundo 3)
Nyimbo Na. 160
8. Lipoti la Chaka cha Utumiki
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Pambuyo powerenga chilengezo chochokera ku ofesi ya nthambi chokhudza lipoti la chaka cha utumiki, funsani omvetsera kuti afotokoze zinthu zabwino zomwe zili mu Lipoti la Chaka cha Utumiki cha 2025 la Mboni za Yehova Padziko Lonse. Funsani ofalitsa omwe munawasankhiratu kuti afotokoze zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo mu utumiki chaka chathachi.
Based on NASA/Visible Earth imagery
Mu 2025, anthu a Yehova anapitiriza kuchita khama polalikira kunyumba ndi nyumba komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo
Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zokhudza Lipoti la Chaka cha Utumiki cha 2025 zimene mungakonde kufotokoza?
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 64-65