MARCH 2-8
YESAYA 41-42
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. “Usachite Mantha”
(10 min.)
Yehova adzapatsa mphamvu “winawake kuchokera kotulukira dzuwa,” yemwe adzachititse anthu kunjenjemera (Yes 41:2, 5; ip-2 21 ¶10-mwbr)
Anthu amene ankalambira Yehova sankafunika kuchita mantha (Yes 41:10; ijwbv nkhani na. 5 ¶4-7-mwbr)
Yehova akanawathandiza (Yes 41:13)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi ulosi wa mu Yesaya chaputala 41, umathandiza bwanji Akhristu masiku ano?—w16.07 18 ¶4-5-mwbr.
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 41:8—Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti Abulahamu anali mnzake? (w01 10/1 20 ¶3-mwbr)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 42:1-13 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwininyumba walandira kapepala komuitanira ku Chikumbutso ndipo wasonyeza chidwi kuti adzapita. (lmd phunziro 6, mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Itanirani wachibale kumwambo wa Chikumbutso ndipo gwiritsani ntchito jw.org kuti mupeze malo a kufupi ndi kwawo, komwe kukachitikire mwambowu. (lmd phunziro 3, mfundo 5)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(5 min.) Nkhani. ijwbq nkhani na. 60—Mutu: Kodi Mungatani Kuti Musamaope Kwambiri Imfa? (th phunziro 1)
Nyimbo Na. 19
7. Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Iyamba Loweruka pa 7 March
(5 min.) Nkhaniyi ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani zimene mpingo wanu wakonza zokhudza ntchitoyi, nkhani yapadera komanso mwambo wa Chikumbutso. Limbikitsani onse kuti ayesetse kuchita zambiri mu utumiki m’miyezi ya March ndi April. Ofalitsa angachite upainiya wothandiza wa maola 15.
8. Vidiyo ya Zimene Gulu Lathu Lachita ya March
(10 min.) Nkhani yokambirana.
Onerani VIDIYOYI. Kenako funsani mafunso omwe aoneka muvidiyoyi.
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 66-67