MARCH 23-29
YESAYA 48-49
Nyimbo Na. 89 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Mukamamvera Yehova Zinthu Zidzakuyenderani Bwino
(10 min.)
Yehova amaphunzitsa atumiki ake (Yes 48:17; it-E “Mphunzitsi, Kuphunzitsa” ¶2-mwbr)
Timafunika kusankha kumvera Yehova (Yes 48:18a; ijwbq nkhani na. 44 ¶2-3-mwbr)
Tikatero mtendere wathu udzakhala “ngati mtsinje” ndipo chilungamo chathu chidzakhala “ngati mafunde a mʼnyanja” (Yes 48:18b; lv 199 ¶8-mwbr)
TANTHAUZO: Mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti “mtendere” anganenenso za thanzi, chitetezo, mphamvu, moyo wabwino, ubwenzi kapenanso kukwanira bwino.
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 49:8—Kodi ulosiwu unakwaniritsidwa m’njira zitatu ziti? (it-E “Nthawi Yovomerezeka” ¶1-3-mwbr)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 48:9-20 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Itanirani wachibale yemwe anasiya kusonkhana ku nkhani yapadera komanso ku Chikumbutso. (lmd phunziro 5, mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Fotokozerani munthu yemwe akufuna kukapezeka ku Chikumbutso zokhudza zimene zikachitike. (lmd phunziro 9, mfundo 3)
6. Ulendo Wobwereza
(5 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pambuyo pa nkhani ya Chikumbutso, yankhani mafunso a munthu wachidwi yemwe anapezekapo. (lmd phunziro 8, mfundo 3)
Nyimbo Na. 107
7. Zimene Mungachite Kuti Mudzapindule pa Tsiku Lofunika Kwambiri pa Chaka
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Tikamapezeka pa Chikumbutso chaka chilichonse timasonyeza kuti timamvera lamulo la Yesu komanso timayamikira Yehova chifukwa cha mphatso ya dipo. (Lu 22:19) Komabe mwambowu umatikumbutsanso kuti Yehova ndi Mwana wake amatikonda kwambiri. (Aga 2:20; 1Yo 4:9, 10) Kodi tingatani kuti tidzapindule kwambiri ndi mphatso imene Yehova anatipatsayi? Kodi tingathandize bwanji ena kuti nawonso adzapindule?
Kuyamba kuwerenga Baibulo panyengo ya Chikumbutso tsiku lililonse
Kuganizira mphatso ya dipo komanso kuchita zinthu m’njira yosonyeza kuti timaliyamikira
Kuchita zonse zomwe tingathe kuti tiitanire anzathu, achibale ndi anthu a m’gawo lathu ku nkhani yapadera komanso mwambo wa Chikumbutso
Kulandira anthu amene abwera ku Chikumbutso mwansangala. Kuwonjezera pa kuchita chidwi ndi anthu amene inuyo munawaitanira, muzidzachitanso chidwi ndi anthu ena omwe abwera, ndipo ngati n’kotheka mudzakhale nawo limodzi
Mudzakhale okonzeka kuyankha mafunso a alendo omwe abwera
Mudzakhale okonzeka kulandira anthu amene anasiya kusonkhana. Makamaka akulu adzakhale tcheru kulandira omwe anachotsedwa
Onerani VIDIYO yakuti Yesu “Anabwera Kudzafunafuna Ndi Kupulumutsa Anthu Osochera.” Kenako funsani funso ili:
Kodi mwaphunzira chiyani pa nkhani yolandira anthu amene anafooka omwe adzabwere ku Chikumbutso?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 72-73