MARCH 16-22
YESAYA 45-47
Nyimbo Na. 2 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. “Ine Ndine Mulungu Ndipo Palibe Aliyense Wofanana ndi Ine”
(10 min.)
Palibe aliyense wofanana ndi Yehova (Yes 46:9; w20.06 5 ¶14-mwbr)
Palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake (Yes 46:10, 11; cl 42 ¶14-mwbr; it-E “Ayuda Omwe Anali ku Ukapolo ku Babulo Anabwerera Kwawo” ¶1-mwbr)
Anthu amene amadalira milungu yabodza ndi amene amagwiritsidwa fuwa lamoto (Yes 46:6, 7; w99 5/15 14 ¶18-19-mwbr)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 46:10—Kodi Yehova anadziwiratu pachiyambi kuti Adamu ndi Hava adzachimwa? (w11 1/1 14 ¶2-3-mwbr)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 45:1-11 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Fotokozerani munthu yemwe si Mkhristu zimene zimachitika pamwambo wa Chikumbutso. (lmd phunziro 5, mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pemphani munthu amene pa ulendo wapita analandira kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 9, mfundo 5)
6. Kuphunzitsa Anthu
Nyimbo Na. 38
7. Amene Tingamudalire Kuti Azitithandiza
(7 min.) Nkhani yokambirana.
Tikakumana ndi mavuto, tizidalira Mulungu wathu Yehova kuti azitithandiza.—Ahe 13:5, 6.
Werengani Salimo 55:22. Kenako kambiranani zitsanzo zotsatirazi ndi omvetsera.
Pa chitsanzo chilichonse, lembani njira imodzi yomwe tingasonyezere kuti timadalira Yehova komanso imene iye amatithandizira.
Atichotsa ntchito kapena tikuvutika kupeza ndalama zosamalira banja lathu
Akuluakulu a boma aletsa ntchito yathu
Tikudwala matenda aakulu
Takumana ndi vuto lalikulu monga ngozi ya m’chilengedwe kapena imfa ya munthu amene timamukonda
8. Lipoti la Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga la 2026
(8 min.) Nkhani.
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 70-71