APRIL 27–MAY 3
YESAYA 56-57
Nyimbo Na. 12 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Timasangalala Kuti Yehova Ndi Mulungu Wathu
(10 min.)
Mafano sangamve kufuula kopempha thandizo kwa anthu amene amalambira mafanowo (Yes 57:13; ip-2 269 ¶14-16-mwbr)
Anthu amene satumikira Yehova sakhala ndi mtendere ndipo sagwirizana (Yes 57:20; w18.06 7 ¶16-mwbr; it-E “Dziko” ¶21-mwbr)
Anthu oipa alibe mtendere (Yes 57:21; it-E “Mtendere” ¶3-mwbr)
DZIFUNSENI KUTI, Kodi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kumandithandiza bwanji kukhala ndi moyo wosangalala?
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 56:6, 7—Kodi ulosiwu ukukwaniritsidwa bwanji? (w07 1/15 10 ¶3-mwbr; w06 11/1 27 ¶1-mwbr)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 56:4-12 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Fotokozerani munthu mfundo inayake imene mwaphunzira posachedwapa pamisonkhano. (lmd phunziro 2, mfundo 4)
5. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(5 min.) Nkhani. ijwbq nkhani na. 90—Mutu: Kodi Pali Vuto Ngati Munthu Atakhala Kuti Sali M’chipembedzo Chilichonse? (th phunziro 16)
6. Kuphunzitsa Anthu
Nyimbo Na. 58
7. Tisasiye Kuuza Ena Zokhudza Yehova
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Anthu amene satumikira Yehova sapeza malangizo odalirika, sakhala ndi zolinga zomwe zingawathandize kukhala osangalala komanso alibe chiyembekezo chodzakhala ndi tsogolo labwino. Komabe iwo amakana kumvetsera uthenga wa Ufumu ngakhale kuti ungawathandize kwambiri. Tiyeni tione zina mwa zifukwa zomwe zimachititsa kuti tisasiye kuuza anthu zokhudza Yehova.—Mla 11:6.
Kusamuka kwa anthu. Eninyumba omwe samafuna kutimvetsera angasamuke ndipo anthu ena omwe alowa nyumbazo angatimvetsere
Sitingalandiridwe ndi munthu yemwe anatikana poyamba. M’malomwake, tingalandiridwe ndi munthu wina wachikulire, wachinyamata yemwe poyamba anali mwana, mnzake wa munthuyo kapena mlendo
Anthu amasintha. (1Ti 1:13) Kuwonjezereka kwa mavuto padzikoli kapena zinthu zokhumudwitsa zimene anthu akumana nazo zingachititse kuti amvetsere
Tikamachitabe khama timasonyeza kuti timakonda Yehova.—Lu 6:45; 1Yo 5:3
Onerani VIDIYO yakuti Yehova “Sali Kutali.” Kenako funsani funso ili:
Kodi mwaphunzira chiyani pa nkhani yopitirizabe kulalikira ngakhale ena asamvetsere?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 80-81