APRIL 20-26
YESAYA 54-55
Nyimbo Na. 86 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kodi Inuyo Mupereka Chiyani?
(10 min.)
Yehova analonjeza kuti azidzaphunzitsa ana ake (Yes 54:13; w09 9/15 21 ¶3)
Muzigula choonadi pogwiritsa ntchito nthawi yanu (Yes 55:1, 2; w18.11 4 ¶6-7)
Kumvetsera mwatcheru kumafuna khama, koma n’kothandiza kuti tidzapeze moyo (Yes 55:3; be 14 ¶3-5)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Ndingatani kuti ndizichita khama ndikamaphunzira pandekha?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 54:17—Kodi mbali yoyamba ya vesili ikutikumbutsa mfundo zofunika zitatu ziti? (w19.01 6 ¶14-15)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 54:1-10 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani mfundo imodzi ya choonadi mu Zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu. (lmd phunziro 1, mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Kambiranani mfundo imodzi ya choonadi mu Zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu. (lmd phunziro 2, mfundo 3)
6. Ulendo Wobwereza
(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. M’patseni munthu limodzi mwa makadi athu. (lmd phunziro 9, mfundo 3)
7. Nkhani
(5 min.) be 28 ¶3–31 ¶2—Mutu: Kaphunziridwe Koyenera. (th phunziro 14)
Nyimbo Na. 97
8. Musamalole Chilichonse Kukulepheretsani Kuphunzira Panokha
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Pali zinthu zambiri zimene zingamatilepheretse kuphunzira Baibulo patokha nthawi zonse. Tiyerekeze kuti mukufuna kuthandiza Mkhristu mnzanu yemwe akulephera kumaphunzira payekha mokhazikika kapena kuwerenga Baibulo tsiku lililonse. Iye wakuuzani zinthu zotsatirazi zomwe zikumulepheretsa. Pa vuto lililonse lembani njira imodzi, mfundo ya M’malemba kapena lifalensi imene ingamuthandize.
“Sindimawerenga bwino”
“Kuphunzira sikumandisangalatsa”
“Ndimasowa poyambira kuwerenga Baibulo komanso kuti ndiziwerenga zochuluka bwanji pa tsiku”
“Pali zambiri zoti n’kuphunzira, ndiye ndiziphunzira zinthu ziti mlungu uliwonse?”
“Ndimakhala ndi zochita zambiri moti n’zovuta kupeza nthawi yophunzira”
“Zimandivuta kuika maganizo pa zimene ndikuphunzira ndipo nthawi zina sindikumbukira zimene ndawerenga”
Onerani VIDIYO yakuti Kuphunzira Mwakhama. Kenako funsani funso ili:
Ndi mfundo ziti zokhudza kuphunzira patokha zomwe mwaona muvidiyoyi zimene zakusangalatsani?
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 78-79