APRIL 13-19
YESAYA 52-53
Nyimbo Na. 18 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
Yesu akupita kukaphedwa
1. Yesu Anatisonyeza Chikondi Chachikulu
(10 min.)
Yesaya analosera kuti Yesu adzanyozedwa (Yes 53:3; Mt 26:67, 68; w10 11/15 7 ¶2-mwbr)
Yesu analola kuti azunzidwe (Yes 53:7; ip-2 205 ¶25-mwbr)
Chifukwa cha chikondi, Yesu anali wofunitsitsa kuvutika kuti achite zimene Yehova ankafuna komanso kunyamula machimo athu (Yes 53:10-12; Yoh 14:31; 15:13)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 52:11—Kodi Aisiraeli akanatsatira bwanji lamulo la mu ulosiwu, nanga ifeyo tingalitsatire bwanji? (it-E “Ziwiya” ¶2-mwbr)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 53:3-12 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pemphani mwininyumba kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 4, mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani mfundo imodzi ya choonadi mu Zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu. (lmd phunziro 3, mfundo 3)
6. Ulendo Wobwereza
(5 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pemphani munthu amene anapezeka pa Chikumbutso kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 8, mfundo 3)
Nyimbo Na. 20
7. Khalani Bwenzi la Yehova—Anasonyeza Chikondi Chachikulu Kwambiri
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Onerani VIDIYO. Kenako funsani funso ili:
Kodi nsembe ya Yesu ndi mphatso m’njira yotani?
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira nsembe yake?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 76-77