MAWU A M’BAIBULO
Yesu “Anaphunzira Kumvera”
Yesu wakhala akumvera Yehova kuyambira kalekale. (Yoh. 8:29) Ndiye n’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti: Iye “anaphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo”?—Aheb. 5:8.
Yesu ali padzikoli anakumana ndi zinthu zomwe sizinkachitika kumwamba. Mwachitsanzo, analeredwa ndi makolo oopa Mulungu koma sanali angwiro. (Luka 2:51) Anazunzidwanso ndi atsogoleri a chipembedzo achinyengo komanso olamulira opanda chilungamo. (Mat. 26:59; Maliko 15:15) Komabe iye “anadzichepetsa ndipo anakhala womvera mpaka imfa,” yomwe inali yowawa kwambiri.—Afil. 2:8.
Zimenezi zinachititsa kuti Yesu aphunzire kumvera m’njira imene siikanatheka ali kumwamba. Choncho anakhala Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe wabwino kwambiri, yemwe akhoza kutimvetsa. (Aheb. 4:15; 5:9) Yesu anakhala wamtengo wapatali kwambiri kwa Yehova ataphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo. Ifenso tingakhale amtengo wapatali kwambiri kwa Yehova ndipo angatigwiritsire ntchito pa utumiki uliwonse ngati titakhalabe omvera ngakhale pamene takumana ndi mavuto.—Yak. 1:4.