Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi amene analemba Miyambo 30:18, 19, ankatanthauza chiyani pomwe ananena kuti “njira ya mwamuna ndi mtsikana” ndi ‘yodabwitsa kwambiri?’
Anthu ambiri kuphatikizapo akatswiri a Baibulo amazunguzika ndi mawu amenewa. Mu Baibulo la Dziko Latsopano, mawu onse amamveka kuti: “Pali zinthu zitatu zimene nʼzodabwitsa kwambiri kwa ine, ndiponso zinthu 4 zimene sindizimvetsa. Zinthu zake ndi izi: njira ya chiwombankhanga mumlengalenga, njira ya njoka pamwala, njira ya sitima pakatikati pa nyanja, ndiponso njira ya mwamuna ndi mtsikana.”—Miy. 30:18, 19.
M’mbuyomu, tinkaona kuti mawu akuti “njira ya mwamuna ndi mtsikana” amanena za zinazake zolakwika. Tinkaganiza choncho chifukwa mavesi ena a m’chaputalachi amanena za zinthu zina zoipa zimene sizinena kuti “ndakhuta.” (Miy. 30:15, 16) Ndipo vesi 20 limanena za “mkazi wachigololo,” yemwe amanena kuti sanachite choipa chilichonse. Choncho tinkaganiza kuti mofanana ndi chiwombankhanga mumlengalenga, njoka pamwala kapenanso sitima panyanja, mwamunayo akhoza kuchita zinazake anthu osadziwa. Ndiye tinkaganiza kuti mawu akuti “njira ya mwamuna ndi mtsikana,” akutanthauza zinazake zoipa. Mwachitsanzo, mnyamata kupusitsa mtsikana kuti agone naye.
Koma pali zifukwa zotichititsa kukhulupirira kuti akunena za zinthu zabwinobwino. Wolembayu ankangodabwa ndi zinthu zomwe anatchulazi.
Mipukutu yoyambirira ya Chiheberi imasonyezanso kuti vesili limanena za zinthu zabwinobwino. Mogwirizana ndi zimene buku lina linanena, mawu a Chiheberi omwe anamasuliridwa kuti “n’zodabwitsa kwambiri” pa Miyambo 30:18, “amafotokoza za zinthu zimene munthu . . . angaone kuti n’zosamvetsetseka, zosatheka kapenanso zochititsa chidwi.”—Theological Lexicon of the Old Testament.
Pulofesa wina wa kuyunivesite ya Harvard ku United States dzina lake Crawford H. Toy, ananenanso kuti vesili silimanena za zinthu zinazake zolakwika. Iye anati: “Apa nkhani ndi ya kudabwitsa kwa zinthu zimene zatchulidwa basi.”
Choncho m’pomveka kunena kuti mawu a pa Miyambo 30:18, 19 akunena za zinthu zodabwitsa kwambiri, kapena kuti zovuta kumvetsa. Mofanana ndi wolemba Baibuloyu, nafenso timagoma tikamaganizira mmene chiwombankhanga chimaulukira mumlengalenga, mmene njoka yomwe ilibe miyendo imayendera pamwala, mmene sitima yolemera imayendera panyanja komanso mmene zimakhalira kuti mnyamata ndi mtsikana ayambe kukondana kwambiri kenako kudzakwatirana n’kumasangalala.