Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi wolemba Miyambo 30:19, (“NW”), analingaliradi kuti njira imene mwamuna amakopa nayo namwali inali “yodabwitsa kwambiri”?
Limenelo nditanthauzo lothekera la Miyambo 30:19, limene kunena zowona ndivesi lovuta kumvetsetsa.
Pofuna tanthauzo la vesi limeneli, sitiyenera kunyalanyaza mawu apatsogolo ndi apambuyo. Mwamsanga asanafike pandime imeneyi, wolemba wouziridwa anandandalika zinthu zinayi zimene mwanjira ina sizimakhuta. (Miyambo 30:15, 16) Ndiyeno anandandalika zotsatirazi: “Zinthu zitatu [zimandidabwitsa kwambiri, NW], ngakhale zinthu zinayi, sindizidziŵa; njira ya mphungu m’mlengalenga, njira ya njoka pamwala, njira ya ngalaŵa pakati pa nyanja, njira ya mwamuna ndi namwali.”—Miyambo 30:18, 19.
Kodi nchiyani chimene chikanakhala ‘chodabwitsa’ m’zinthu zinayi zimenezi?
Mwinamwake poganiza kuti liwu lakuti ‘chodabwitsa’ liyenera kutanthauza chotsimikizirika kapena chabwino, akatswiri ena amafotokoza kuti chirichonse cha zinthu zinayizo chimasonyeza nzeru ya Mulungu yakulenga: kuzizwitsa kwa mmene mbalame yaikulu ingaulukire, mmene njoka yopanda miyendo ingadutsire pamwala, mmene ngalaŵa yolemera ingayandamire panyanja yoŵinduka, ndi mmene mnyamata wojintcha angakopedwere mosayembekezereka kukonda ndi kukwatira namwali wokongola, ndiyeno kubala mwana wochititsa kaso. Profesa wina anawona kufanana kwina mwa zinthu zinayizo, kuti zonse zimayenda panjira imene iri yatsopano nthaŵi zonse—mayendedwe a mphungu, njoka, ndi ngalaŵa pamalo opanda njira ndi njira yatsopano imene mwamuna ndi mkazi amakulitsira chikondi.
Komabe, zinthu zinayizo sizifunikira kukhala ‘zodabwitsa’ m’lingaliro lakuti nzabwino, ngati kuti kufanana kwawo kuli kanthu kena kotsimikizirika. Miyambo 6:16-19 imasanja “zinthu . . . [zimene] Mulungu azida.” Ndipo monga momwe tawonera, mwamsanga isanafike pamavesi amene funso lazikidwapo, Miyambo 30:15, 16 imatchula (Manda, chumba, dziko losakhuta madzi, ndi moto) kukhala zinthu zimene sizimanena konse kuti, “Kwatha.” Ndithudi zimenezo sizodabwitsa m’lingaliro lakuti nzabwino.
Liwu Lachihebri lomasuliridwa ‘chodabwitsa’ pa Miyambo 30:18, (NW) limatanthauza “kulekanitsa, kusiyanitsa; kukhala chapadera, chozizwitsa, chodabwitsa.” Chinthu chikhoza kukhala chapadera, chozizwitsa, kapena chodabwitsa popanda kukhala chabwino. Danieli 8:23, 24 inalosera za mfumu yowopsa imene ikawononga “modabwitsa” ndi “kuwononga amphamvuwo,” kuphatikizapo oyera mtima.—Yerekezerani ndi Deuteronomo 17:8; 28:59; Zekariya 8:6.
Vesi lotsatira Miyambo 30:18, 19 lingatithandize kudziŵa zimene wolembayo anapeza kukhala zovuta kumvetsetsa. Vesi 20 limatchula mkazi wachigololo amene “adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachita zoipa.” Mwinamwake mkaziyo adachimwa mwakabisira ndi mwamachenjera, koma popeza kuti upandu wake sunadziŵike, akatha kunena kuti ngwopanda liŵongo.
Pali kufanana ndi ndandanda yoyambirira. Mphungu imauluka m’mlengalenga, njoka imadutsa thanthwe, ngalaŵa imadutsa mafunde—zonsezo sizimasiya nkukuluzi, ndipo kukakhala kovuta kuyesa kulondola njira ya chirichonse cha zinthu zitatuzo. Ngati kumeneko ndiko kufanana kwa zinthu zitatu zimenezo, bwanji nanga za chachinayi, “njira ya mwamuna ndi namwali”?
Nayonso ingakhale yosalondoleka. Mnyamata angagwiritsire ntchito chinyengo, kusyasyalika, ndi njira zamachenjera kukopa namwali wosazindikirayo kuti amkonde. Pokhala wosadziŵa, namwaliyo sangazindikire machenjera a mnyamatayo. Ngakhale atanyengedwa, sangathe kufotokoza mmene mwamunayo anamkopera; choteronso anthu openyerera angakupeze kukhala kovuta kufotokoza. Chikhalirechobe, asungwana ambiri ataya mkhalidwe wawo wabwino kwa okopa osyasyalika. Nkovuta kufufuza njira ya amuna osyasyalika otero, komabe ali ndi cholinga, monga momwe imachitira mphungu pouluka, njoka yokwaŵa, kapena ngalaŵa panyanja. Kwa onyengawo, cholinga chawo ndikugonana basi.
Mogwirizana ndi zimene tapenda, mfundo ya Miyambo 30:18, 19 simaphatikizapo zinthu za sayansi kapena zopanda moyo m’chilengedwe. Mmalomwake, mawuwo amatichenjeza m’zamakhalidwe, monga momwe Miyambo 7:1-27 imachenjezera za kupeŵa maupandu a hule lonyengerera. Njira imodzi imene alongo Achikristu angalabadirire chenjezo la Miyambo 30:18, 19 njophatikizapo amuna amene amawonekera kusonyeza chikondwerero m’kuphunzira Baibulo. Ngati mwamuna waubwenzi, ngakhale wogwira naye ntchito, awonekera kusonyeza chikondwerero chotero, mlongoyo ayenera kumlongoza kwa mbale mumpingo. Mbaleyo adzakhoza kukhutiritsa chikondwerero chowona chirichonse chimene munthuyo angakhale nacho popanda upandu wa “mwamuna ndi namwali.”