MAWU A M’BAIBULO
Muzigwiritsa Ntchito ‘Mphatso Yanu ya Uzimu’
Tonsefe timasangalala tikamalimbikitsana ndi abale komanso alongo athu. Koma kuti tilimbikitsane, tikufunika kuchita zambiri kuposa kungokhala ndi abale komanso alongo athu. Baibulo limanena kuti mwayi umene tili nawo wolimbikitsana ndi ‘mphatso yauzimu.’ (Aroma 1:11, 12) Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito mphatso imeneyi mokwanira?
Zolankhula zanu zizilimbikitsa anthu ena. Mwachitsanzo, tingapereke ndemanga kumisonkhano zimene zingapangitse anthu kuti aziganizira za Yehova, Mawu ake komanso anthu ake, osati za ifeyo. Tikamacheza ndi abale komanso alongo athu, tingachite bwino kumakambirana nkhani zolimbikitsa.
Zosankha ndi zochita zanu zizilimbikitsa anthu ena. Mwachitsanzo, anthu ena amasankha kupitiriza kuchita utumiki wa nthawi zonse ngakhale kuti akukumana ndi mavuto. Ena amapezeka pa misonkhano ya m’kati mwa mlungu nthawi zonse ngakhale kuti amapanikizika ndi ntchito kapena ali ndi matenda okhalitsa.
Kodi zimene mumalankhula komanso kuchita zimalimbikitsa abale ndi alongo anu? Kodi mumaona zimene abale ndi alongo anu amalankhula komanso kuchita pofuna kukulimbikitsani?