Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi ndi “maganizo” ati amene Yehova adzaike m’mitima ya mayiko posachedwapa?
Pofotokoza za mmene chisautso chachikulu chidzayambire, lemba la Chivumbulutso 17:16, 17 limanena kuti: “Nyanga 10 zimene waziona zija komanso chilombo, zidzadana ndi hulelo. Zidzatenga zinthu zake zonse nʼkulisiya lamaliseche ndipo zidzadya minofu yake nʼkulipsereza ndi moto. Chifukwa Mulungu anaika pulani mʼmitima yawo kuti zichite mogwirizana ndi maganizo ake komanso kuti zikwaniritse maganizo awo ofanana aja, popereka ufumu wawo kwa chilombo.” M’mbuyomu mabuku athu akhala akufotokoza kuti “maganizo” amene Yehova adzaike m’mitima ya mayiko ndi akuti awononge zipembedzo zabodza.
Komabe pakufunika kusintha mmene timamvera mfundo imeneyi. “Maganizo” amene Yehova adzaike m’mitima ya mayikowa ndi akuti apereke “ufumu wawo kwa chilombo.” Kuti timvetse mmene zimenezi zidzachitikire, tiyeni tiganizire mafunso otsatirawa.
Kodi ndi ndani amene akutchulidwa mu ulosiwu? Ulosiwu ukunena za “hule” lomwe limadziwikanso kuti “Babulo wamkulu.” Huleli limaimira zipembedzo zonse zabodza. Pamene “chilombo chofiira kwambiri” chimaimira bungwe lokhazikitsa mtendere la League of Nations, limene linayamba kugwira ntchito mu 1919 ndipo panopa limadziwika kuti United Nations. (Chiv 17:3-5) “Nyanga 10” zikuimira maulamuliro onse a anthu amene amathandiza chilombochi.
Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa hule ndi chilombo chofiira kwambiri? Huleli “lakhala” pa chilombochi kutanthauza kuti limachithandiza, kulamulira chilichonse chimene chikuyenera kuchita komanso kuchita zimene huleli likufuna.
Kodi n’chiyani chidzachitikire huleli? Chilombo komanso nyanga 10 zimene zimathandiza chilombochi ‘zidzadana ndi huleli.’ Posonyeza mkwiyo wawo iwo adzalanda chuma cha huleli komanso kusonyeza zinthu zoipa zimene huleli limachita. Kenako adzapereka chiweruzo cha Yehova kwa huleli poonetsetsa kuti lawonongedwa kotheratu. (Chiv 17:1; 18:8) Amenewa adzakhala mapeto a zipembedzo zonse zabodza. Koma zimenezi zisanachitike Yehova adzachititsa kuti mayiko achite zinthu zimene sizinachitikepo m’mbiri ya ulamuliro wa anthu padzikoli.
Kodi Yehova adzachititsa kuti mayiko achite zotani? Iye adzaika “maganizo ake” m’mitima ya nyanga 10 amene ndi maulamuliro a anthu. Zimenezi zidzachititsa kuti maulamulirowa “apereke mphamvu zawo ndi ulamuliro wawo kwa chilombo chofiira kwambiri,” lomwe ndi bungwe la United Nations. (Chiv. 17:13) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Kodi maboma a anthu adzasankha okha kuti apereke mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chilombochi? Ayi. Ulosiwu ukusonyeza kuti Mulungu mwiniwakeyo ndi amene adzachititse zimenezi. (Miy. 21:1; yerekezerani ndi Yesaya 44:28.) Kodi kumeneku kudzakhala kusintha kwa pang’onopang’ono kwa ulamuliro? Ayi. Zimenezi zidzachitika mwadzidzidzi komanso mofulumira kwambiri. Kenako chilombochi chidzagwiritsa ntchito mphamvu zake popereka chiweruzo cha Yehova kwa mabungwe onse a zipembedzo zabodza powachotsa ndipo sadzakhalaponso mpaka kalekale.
Ndiye kodi tikuyembekezera kuti n’chiyani chidzachitike kutsogoloku? Tisayembekezere kuti tidzayamba kumva nkhani zosonyeza kuti mwapang’onopang’ono maboma ayamba kuthandiza kwambiri bungwe la United Nations. Zimene tingayembekezere ndi zakuti mwadzidzidzi, Yehova adzachititsa kuti mayiko apereke mphamvu zawo kwa chilombo. Zimenezi zikadzachitika tidzadziwa kuti chisautso chachikulu chatsala pang’ono kuyamba. Choncho tiyeni “tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino” chifukwa posachedwapa, zinthu zisintha mwadzidzidzi.—1 Ates. 5:6.