Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 December tsamba 31
  • Kodi Mukukumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukumbukira?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukukumbukira?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Gawo 1
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 December tsamba 31

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini a chaka chino a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

N’chiyani chimatilimbikitsa kuti tizipatsa Yehova ulemerero?

Timachita zimenezi chifukwa timamulemekeza komanso kumukonda kwambiri. Timafunanso kuti anthu ena amudziwe.—w25.01, tsamba 3.

Ngati munthu wina watikhumudwitsa, kodi tingatani kuti timukhululukire?

Tisamanyalanyaze mmene tikumvera. Komabe tikasankha kuti tisapitirize kukwiya komanso kusunga chakukhosi zidzatithandiza kuti tisadzivulaze.—w25.02, tsamba 15-16.

N’chifukwa chiyani Maliko ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa achinyamata?

Maliko anavomera mofunitsitsa kutumikira ena. Ngakhale kuti anakhumudwa ndi zimene zinamuchitikira, sanafooke. Anayambiranso kugwirizana kwambiri ndi Paulo komanso abale ena olimba mwauzimu.—w25.04, tsamba 27.

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anapemphera kuti: “Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu”? (Yoh. 17:26)

Ophunzira ake ankadziwa kale dzina la Mulungu. Koma iye anawathandiza kudziwa zimene dzinali linkaimira kuphatikizapo zolinga zake, zochita zake komanso makhalidwe ake.—w25.05, tsamba 20-21.

Kodi kudzichepetsa kumatithandiza kuzindikira mfundo iti?

Kumatithandiza kuzindikira kuti sitidziwa zonse. Mwachitsanzo, sitidziwa tsiku limene mapeto adzafike, mmene Yehova adzachitire zinthu pa nthawiyo komanso zimene zichitike mawa. Sitidziwanso mmene Yehova amatidziwira.—w25.06, tsamba 15-18.

Kodi mungatani kuti muzipindula mukamawerenga nkhani kapena kumvetsera nkhani ya onse?

Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi agwiritsa ntchito umboni uti pofuna kuwafika anthu pamtima?’ ‘Kodi pali fanizo labwino limene ndingagwiritse ntchito pophunzitsa?’ ‘Kodi ndi ndani angachite chidwi ndi nkhaniyi?’—w25.07, tsamba 19.

Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yehova pa nkhani yokhululuka tikaona mmene anachitira zinthu ndi Davide?

Ngakhale kuti Davide anachita machimo aakulu, atalapa kuchokera pansi pamtima Yehova anamukhululukira. (1 Maf. 9:​4, 5) Yehova akatikhululukira, saganiziranso zoipa zimene tinachitazo.—w25.08, tsamba 17.

Kodi tizitani ngati amene tikuphunzira naye Baibulo akuvutika kumvetsa mfundo inayake?

Ngati akuvutikabe kumvetsa pambuyo poti tayesetsa kumuphunzitsa pogwiritsa ntchito Baibulo, tingasiye kaye mfundoyo kuti tidzaikambirane nthawi ina.—w25.09, tsamba 24.

Baibulo limanena kuti uchimo uli ndi “chinyengo champhamvu.” (Aheb. 3:13) N’chifukwa chiyani zili choncho?

Uchimo umachititsa kuti tizikopeka n’kuchita zinthu zolakwika. Ukhozanso kutipusitsa kuti nthawi zonse tizikayikira zoti Yehova amatikonda.—w25.10, tsamba. 16.

Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene zingathandize kuti mapemphero athu azikhala ochokera pansi pa mtima?

(1) Tiziganizira makhalidwe a Yehova. (2) Tiziganizira vuto limene tikulimbana nalo n’kulitchula m’pemphero, mwachitsanzo ngati pali winawake amene tikufunika kumukhululukira. (3) Tizipemphera kwa nthawi yaitali. Zimenezi zidzatipatsa mwayi womuuza Yehova zamumtima mwathu.—w25.10, tsamba 19-20.

Kodi tingatani kuti tithandize achikulire?

Tiziwayendera, kuwaimbira foni, kuwaperekeza kuchipatala kapena kuchitira nawo limodzi maulaliki osiyanasiyana.—w25.11, tsamba 6-7.

Ndi zinthu ziti zimene zimapangitsa ukwati wa Chikhristu kukhala wolemekezeka?

Kutsatira malamulo aboma okhudza ukwati. Kuonetsetsa kuti pa ukwati wanu anthu akusonyeza makhalidwe abwino. Kupewa kuvala modzionetsera komanso miyambo yosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Kulankhulana momasuka komanso mwaulemu mukamakambirana mapulani a ukwati wanu.—w25.12, tsamba 21-24.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena