MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Zimene Mungachite Kuti Muzikhulupirira Kwambiri Kuti Yehova Ali Ndi Mphamvu Zotha Kupulumutsa
Werengani Numeri 13:25–14:4 kuti muone mmene Aisiraeli anasonyezera kuti sankakhulupirira Yehova.
Onani nkhani yonse. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ankayenera kukhulupirira kuti Yehova akhoza kuwapulumutsa pamene ankachoka ku Iguputo? (Sal. 78:12-16, 43-53) Kodi n’chiyani chimene chinachititsa kuti asiye kudalira Yehova? (Deut. 1:26-28) Kodi Yoswa ndi Kalebe anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Yehova?—Num. 14:6-9.
Fufuzani Mozama. Kodi Aisiraeli akanatani kuti azikhulupirira kwambiri Yehova? (Sal. 9:10; 22:4; 78:11) Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kukhulupirira Yehova ndi kumulemekeza?—Num. 14:11.
Onani zimene mukuphunzirapo. Muzidzifunsa kuti:
‘Kodi ndi pa zochitika ziti pamene zingakhale zovuta kwambiri kuti ndikhulupirire Yehova?’
‘Kodi ndingatani kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova panopa komanso m’tsogolo?’
‘Kodi sindikufunika kukayikira chiyani pamene chisautso chachikulu chikuyandikira?’—Luka 21:25-28.