Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mrt nkhani 34
  • Kodi Uchigawenga Udzatha?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Uchigawenga Udzatha?
  • Nkhani Zina
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mulungu amaona bwanji uchigawenga?
  • N’chiyani chimachititsa zauchigawenga?
  • Kutha kwa uchigawenga
  • Uchigaŵenga Utha Posachedwapa!
    Galamukani!—2001
  • Mtendere Udzabweradi Padziko Lapansi!
    Galamukani!—2006
  • Mbiri Yodzaza ndi Kukhetsa Magazi
    Galamukani!—2006
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Nkhani Zina
mrt nkhani 34
Wozimitsa moto akuthandiza anthu pamalo amene nyumba ziwiri zagwera.

Kodi Uchigawenga Udzatha?

Kukachitika zauchigawenga, mungadzifunse kuti: ‘Kodi Mulungu amatiganizira? N’chifukwa chiyani zinthu ngati zimenezi zimachitika? Kodi uchigawengaa udzatha? Kodi tingatani kuti ndisamachite mantha nthawi zonse?’ Baibulo limapereka mayankho abwino a mafunso amenewa.

Kodi Mulungu amaona bwanji uchigawenga?

Mulungu amadana ndi zachiwawa komanso uchigawenga. (Salimo 11:5; Miyambo 6:16, 17) Ndipotu Yesu, yemwe amaimira Mulungu, anadzudzula ophunzira ake pamene anachita zachiwawa. (Mateyu 26:50-52) Ngakhale kuti anthu ena amanena kuti akuchita zachiwawa m’dzina la Mulungu, iye sasangalala ndi zimene akuchitazo. Mulungu samva ngakhale mapemphero awo.​—Yesaya 1:15.

Mulungu amaganizira anthu onse amene akuvutika, kuphatikizapo amene akuvutika chifukwa cha zauchigawenga. (Salimo 31:7; 1 Petulo 5:7) Baibulo limasonyezanso kuti Mulungu adzathetseratu zachiwawa.​—Yesaya 60:18.

N’chiyani chimachititsa zauchigawenga?

Baibulo limasonyeza chimene chimachititsa kuti anthu azichita zauchigawenga. Limati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Kuyambira kale, anthu audindo akhala akupondereza anthu ena powaopseza. Komanso anthu ena akaopsezedwa amabwezera pochita zauchigawenga.​—Mlaliki 7:7.

Kutha kwa uchigawenga

Mulungu amalonjeza kuti adzathetsa chilichonse chochititsa mantha komanso zachiwawa ndipo adzabweretsa mtendere padzikoli. (Yesaya 32:18; Mika 4:3, 4) Iye adzachita zotsatirazi:

  • Adzachotsa zimene zimachititsa zauchigawenga. Mulungu adzachotsa maboma a anthu n’kuika boma lake lolamulira dziko lonse. Wolamulira wa bomali, yemwe ndi Yesu Khristu, adzachitira aliyense zachilungamo ndipo adzathetsa kupondereza kulikonse komanso zachiwawa. (Salimo 72:2, 14) Pa nthawi imeneyo, palibe amene adzachite zauchigawenga. Anthu “adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”​—Salimo 37:10, 11.

  • Kukonza zonse zimene zachitika chifukwa cha uchigawenga. Mulungu adzachiritsa anthu amene apwetekedwa ndi zauchigawenga ndipo adzawathandiza kuti asavutikenso mumtima mwawo. (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:3, 4) Iye amalonjezanso kuti ngakhale akufa adzawaukitsa kuti akhalenso ndi moyo padziko lapansi lamtendere.​—Yohane 5:28, 29.

Baibulo limasonyezanso kuti Mulungu adzachita zimenezi posachedwapa. Koma mwina mungadzifunse kuti, “N’chifukwa chiyani Mulungu sanathetse uchigawenga mpaka pano?’ Kuti mudziwe yankho lake, onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

a Nthawi zambiri mawu oti “uchigawenga” amanena za zimene anthu ena amachita poopseza anthu anzawo, makamaka anthu wamba, ndi zachiwawa n’cholinga choti asinthe zinthu pa nkhani ya ndale, chipembedzo kapena zinthu zina. Koma anthu angasiyane maganizo pa nkhani ngati zinthu zinazake zimene zachitika ndi zauchigawenga kapena ayi.

Baibulo limathandiza anthu kuti apirire

Baibulo limatilimbikitsa kuchita zinthu ziwiri zotsatirazi zomwe zingatithandize.

  • Muzipemphera kwa Mulungu.​—Afilipi 4:6, 7.

  • Muziganizira zimene Baibulo limanena kuti tingayembekezere m’tsogolo.​—Aheberi 6:19.

Kuti mudziwe zinthu zina zimene Baibulo limatilimbikitsa kuchita, onani nkhani yakuti “Kodi Tingatani Kuti Tisamade Nkhawa Kwambiri?”

A Mboni za Yehova za Yehova amene akhudzidwa ndi zauchigawenga athandizidwa ndi Akhristu anzawo. Zitsanzo ziwiri ndi izi:

  • Nkhata zamaluwa achikumbutso zaikidwa kusukulu ya ku Beslan ku Russia.

    Natalya ndi mwana wake wazaka 9 dzina lake Aslan, anali kusukulu ina ya ku Beslan ku Russia pamene zigawenga zonyamula mfuti zinalowa n’kugwira anthu oposa 1,000. N’zomvetsa chisoni kuti anthu mahandiredi angapo anafa ndipo ambiri mwa iwo anali ana. Ngakhale kuti Natalya ndi Aslan anapulumuka, pambuyo pake ankavutika kwambiri maganizo. Onani zimene zawathandiza.

  • Pablo ndi Sophie.

    Pablo ndi mkazi wake Sophie anaferedwa mwana wawo pamene nsanja ziwiri zija ku New York zinaphulitsidwa. Onerani vidiyoyi kuti mudziwe zimene zawathandiza iwowo komanso anthu ena amene akhudzidwa ndi zauchigawenga.

Baibulo limathandiza anthu kuti asinthe

Anthu ambiri amadandaula chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zomwe zimachitika m’dzikoli. Mwina amaona kuti kuchita zachiwawa kapena kuopseza anthu ndi zokhazo zimene angachite kuti asinthe zinthu padzikoli. Kodi anthu ngati amenewa angasinthe? Inde. Kuti muone mmene mfundo za m’Baibulo zathandizira anthu ena kuti asinthe, werengani nkhani yakuti “Kodi Uchigawenga Udzatha Padzikoli?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena