KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?
Kuchita Zinthu Zothandiza Abale Athu Komanso Zosawononga Chilengedwe
1 APRIL 2025
A Mboni za Yehovafe tikudziwa kuti posachedwapa Yehova Mulungu akonza dzikoli, lomwe anthu aliwononga kwambiri. (Chivumbulutso 11:18) Komabe timachita zomwe tingathe kuti tilisamalire. Mwachitsanzo, tikumanga nyumba zathu zomwe timazigwiritsira ntchito polambira Yehova m’njira yoti zisamawononge chilengedwe.
Cholinga chathu ndi choti zinthu zimene tikumanga zisamawononge kwambiri chilengedwe. Kodi ndi zinthu ziti zimene tachita pofuna kukwaniritsa cholinga chimenechi? Nanga kodi zimenezi zathandiza bwanji kuti zopereka za abale ndi alongo zizigwiritsidwa ntchito mwanzeru?
Njira Yothandiza Kuti Pamalo a Msonkhano Pazikhala Kamphepo Kayeziyezi
Poyamba, Malo a Msonkhano a Matola ku Mozambique anali osatseka m’mbali okhala ndi denga lamalata. Dzuwa likaomba padengali, malo amene anthu akhala ankatentha kwambiri. M’bale wina anena kuti: “Kutentha kumeneku kunkachititsa kuti tizituluka thukuta kwambiri. Nthawi yopuma ikangokwana, abale ankathamangira panja kuti akapitidweko mphepo.” Kodi tikanatani kuti tithandize abale athu kukhala ndi malo ochitirapo msonkhano abwino n’cholinga choti azipindula mokwanira?
Kuti tithane ndi vutoli, tinasankha kugwiritsira ntchito njira yosawononga chilengedwe. Tinaika mafani oyendera mphepo komanso tinaika kudenga zinthu zochepetsa kutentha kwa dzuwa. Zimenezi zimathandiza kuti malowa asamatenthe kwambiri komanso pazidutsa kamphepo kayeziyezi. Mafaniwa sayendera magetsi ndipo amathandiza kuti mpweya wotentha womwe uli pamalowa uzichotsedwa m’njira yachilengedwe. Fani iliyonse inagulidwa ndi madola 50.a
Mafani oyendera mphepo pa Malo a Msonkhano a Matola
Njira imeneyi yathandiza kuti pamalo a msonkhanowa pazikhala mpweya wabwino. Chifukwa choti mpweya ukumayenda bwinobwino, pamalopa sipakumakhala chinyezi komanso nkhungu (nguwi). Njirayi yathandizanso kuti pamalowa pasamakhale mpweya woipa. Choncho anthu akumamvetsera mwatcheru komanso akumakhala momasuka pa nthawi ya misonkhano. M’bale tamutchula kale uja anati: “Panopa sitithamangiranso panja nthawi yopuma ikakwana. Komanso pa nthawi ya chakudya cha masana, timakhala momwemo n’kumacheza ndi anzathu. Zimangokhala ngati takhala pamthunzi wa mtengo waukulu.”
Panopa abale athu amasangalala kwambiri pamisonkhano yadera ndi yachigawo
Kugwiritsira Ntchito Magetsi a Mphamvu ya Dzuwa
Kuzungulira padziko lonse, tinaika masola panyumba zambiri za gulu lathu n’cholinga choti tizigwiritsa mphamvu za dzuwa popanga magetsi. Zimenezi zachititsa kuti tisamagwiritse ntchito kwambiri magetsi ochokera ku zinthu monga malasha, mafuta ndi gasi, zomwe zimatulutsa mpweya wowononga chilengedwe. Masola sawononga kwambiri chilengedwe komanso amathandiza kuti tisamawononge ndalama zimene abale amapereka.
Mu 2022, masola anaikidwa ku ofesi ya nthambi ya Slovenia. Masolawa amatulutsa 30 peresenti ya magetsi amene amagwiritsidwa ntchito panthambiyi. Ngati pa nthawi ina masolawa angapange magetsi ambiri kuposa amene akufunikira, magetsi otsalawo amatha kugwiritsidwa ntchito m’deralo. Masola amenewa anagulidwa pa mtengo wokwanira madola 360,000. Pakamatha zaka 4, ndalama zimene tipulumutse zidzakhala zambiri poyerekeza ndi zimene tinagulira masolawa.
Nthambi ya Slovenia
Mu 2024, tinaika masola komanso batire lalikulu pa ofesi ya nthambi ya Sri Lanka. Tinagwiritsa ntchito madola okwana 3 miliyoni pa ntchitoyi ndipo masolawa amatulutsa 70 peresenti ya magetsi amene amagwiritsidwa ntchito panthambiyi. Pakamatha zaka zitatu, ndalama zimene tipulumutse zidzakhala zambiri poyerekeza ndi zimene tinagulira masolawa. M’chaka chomwechi, tinaikanso masola ku ofesi ya nthambi ya Netherlands. Kuti tiike masolawa, tinagwiritsa ntchito madola 1.1 miliyoni ndipo amatulutsa 35 peresenti ya magetsi amene amagwiritsidwa ntchito panthambiyi. Pakamatha zaka 9, ndalama zimene tipulumutse zidzakhala zambiri poyerekeza ndi zimene tinagulira masolawa.
Nthambi ya Netherlands
Tinaikanso masola m’maofesi ambiri omasulira mabuku (RTO) ku Mexico. Chitsanzo ndi Tarahumara (Central) RTO yomwe ili ku Chihuahua. M’nyengo ya chisanu, kumazizira kwambiri kupitirira 0 digiri seshasi, ndipo m’nyengo ya chilimwe kumatentha kuposa 40 digiri seshasi. Koma chifukwa choti magetsi amadula kwambiri, abale ankapewa kugwiritsa ntchito zipangizo zotenthetsera komanso zoziziritsira m’nyumba. Jonathan, yemwe amatumikira pa RTO imeneyi, ananena kuti: “M’nthawi yozizira tinkafunda mabulangeti ndiponso kuvala zamphepo, pomwe m’nthawi yotentha tinkatsegula mawindo.”
Mu 2024, masola anaikidwa pa RTO imeneyi. Tinagwiritsa ntchito madola okwana 21,480, koma pakamatha zaka 5, ndalama zimene tipulumutse zidzakhala zambiri poyerekeza ndi zimene tinagulira masolawa. Tsopano abale athu akhoza kumagwiritsa ntchito momasuka zipangizo zotenthetsera komanso zoziziritsira m’nyumba. Jonathan anati: “Panopa timasangalala kwambiri ndi utumiki wathu ndipo tikuchita zambiri. Timasangalalanso kudziwa kuti tikugwiritsa ntchito bwino ndalama za gulu komanso tikusamala chilengedwe.”
Timu yomasulira Chitarahumara (Chapakati) ikugwira ntchito pamalo abwino
Kukolola Madzi a Mvula
M’madera ena ku Africa, zimakhala zovuta kupeza madzi oti azigwiritsidwa ntchito pa Nyumba za Ufumu. Choncho abale amafunika kuyenda mtunda wautali kuti akatunge madzi. Pa Nyumba za Ufumu zina, abale amagula madzi pa chigalimoto, koma madziwa amakhala odula komanso amawononga zachilengedwe.
Pofuna kuthandiza abale kuti azikhala ndi madzi, tinaika m’madenga zinthu zokololera madzi komanso mathanki pa Nyumba za Ufumu zambiri ku Africa. Asanaike zinthu zimenezi, abale amafufuza kaye nyengo ya kumene kuli Nyumba ya Ufumuko n’cholinga choti aike zipangizo zoyenera. Pamafunika ndalama za pakati pa madola 600 ndi 3,000 kuti zipangizozi ziikidwe pa Nyumba ya Ufumu. Komabe, zinthu zimenezi nthawi zambiri zimachepetsa ndalama zogwiritsidwa ntchito pa Nyumba ya Ufumu chifukwa abale safunika kumalipira madzi.
Thanki ya madzi pa Nyumba ya Ufumu ya ku Phuthaditjhaba ku South Africa
Njira yokolola madziyi yathandiza kwambiri abale athu. Mlongo wina wa ku Mozambique dzina lake Noemia ananena kuti: “M’mbuyomu tinkakatunga madzi kutali kwambiri moti tinkafika ku Nyumba Ya Ufumu titatoperatu. Ndipo popeza madzi anali osowa, zinali zovuta kumachita zinthu mwaukhondo. Panopa aliyense akhoza kumasamba m’manja. Timasangalala kwambiri ndi misonkhano panopa chifukwa sitimakhalanso otopa. Zikomo kwambiri.”
Mlongo wa ku South Africa ndi mwana wake akusamba m’manja pogwiritsa ntchito madzi a mvula
Kodi ndalama zochitira zinthu zonsezi zimachokera kuti? Zimachokera pa zopereka za padziko lonse zimene nthawi zambiri zimaperekedwa pogwiritsa ntchito njira zomwe zili pa donate.jw.org. Zikomo chifukwa chopereka mowolowa manja.
a Madola onse otchulidwa munkhaniyi ndi a ku America.