Mmene Mungadzitetezerere ku AIDS
CHOYAMBA, pewani magwero oipitsa. Kodi ndimotani mmene mumachitira zimenezo? Mwa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya kudzisungira imene Mulungu Wamphamvuyonse amapereka. Talingalirani mmene zimenezi zikanatetezerera anthu zikwi zambiri amene tsopano alinkuphedwa ndi AIDS.
Kagulu Koyambukiridwa Koposa
Amenewa ndiwo anthu amene mwachangu amagonana ndi ofanana nawo ziwalo zogonanira, makamaka awo amene amafunafuna anzawo atsopano mosalekeza. Baibulo limati:
“Usamagonana ndi nyama iriyonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana; chisokonezo chowopsa ichi.”—Levitiko 18:22.
“Amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chawo wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho ya kuyenera kulakwa kwawo.”—Aroma 1:27.
“Musapange cholakwa: palibe wachigololo kapena wolambira mafano, palibe aliyense wa amene ali ndi liwongo mwina la kukhala wadama kapena la nyere yakugonana ndi wofanana naye ziwalo . . . amene adzalandira ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10, The New English Bible.
Kodi Ndani Enanso Amene Ali Oyambukiridwa?
Anthu amene agonana ndi aliyense yemwe ali ndi kachirombo ka AIDS, mosasamala kanthu kuti munthuyo ndimwamuna kapena ndimkazi. Baibulo limati ponena za izi:
“Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.”—Ahebri 13:4.
“Chifukwa chake fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, . . . chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu.”—Akolose 3:5, 6.
Enanso Amene Ali Paupandu Waukulu
Ogwiritsira ntchito moipa mankhwala ogodomalitsa omwe amadetsa matupi awo ndi mankhwala ogodomalitsawo, akumadzibaya ndi majekisoni oipitsidwa. Kutsutsa kuledzera kochitidwa ndi Baibulo mosakaikira kukanagwiritsiridwa ntchito kwa ogwiritsira ntchito moipa mankhwala ogodomalitsa amakono omwe ziyambukiro zake zopusitsa kapena zosokoneza maganizo ziri pafupifupi zamphamvu mofanana ndi zija zochititsidwa ndi zakumwa zoledzeretsa.
“Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu.”—2 Akorinto 7:1.
“Musasocheretsedwe; adama, . . . kapena oledzera . . . sadzalowa Ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10.
Kagulu Kena Kamene Kali Paupandu Waukulu
Anthu omwe amalandira mwazi woipitsidwa kupyolera mwa kuthiriridwa mwazi. Mwachiwonekere, Baibulo linaletsa anthu kudya mwazi. Iro limati:
“Musamadya mwazi wa nyama iriyonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndimwazi wake; aliyense akaudya adzasadzidwa.”—Levitiko 17:14.
“Pakuti chinakomera mzimu woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; kuti musale . . . mwazi.”—Machitidwe 15:28, 29.
Simunthu aliyense yemwe ali wofunitsitsa kugwiritsira ntchito miyezo ya makhalidwe abwino Yabaibulo ponena za nkhani zimenezi kapena kuvomereza chenicheni chakuti Mulungu ali ndi kuyenera kwa kutiuza chochita. Koma anthu amene atero ali achimwemwe kuti anachita.