Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 41
  • Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yoikidwa Magazi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yoikidwa Magazi?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kulemekeza Moyo ndi Mwazi Mwaumulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mwazi
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Moyo ndi Mwazi—Kodi Mumachita Nazo Monga Zopatulika?
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 41

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yoikidwa Magazi?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo limatilamula kuti tisamadye magazi. Choncho, tiyenera kupewa kudya kapena kuikidwa magazi kapena zigawo zake zikuluzikulu. Taonani malemba otsatirawa:

  • Genesis 9:4. Chigumula chitachitika, Mulungu analola Nowa ndi banja lake kuti azidya nyama koma anawauza kuti asamadye magazi ake. Mulungu anauza Nowa kuti: “Koma musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake.” Lamulo limeneli likugwiranso ntchito kwa anthu onse chifukwa tonsefe ndife zidzukulu za Nowa.

  • Levitiko 17:14. “Musamadye magazi a nyama iliyonse, chifukwa moyo wa nyama ina iliyonse ndi magazi ake. Aliyense wodya magaziwo ayenera kuphedwa.” Mulungu amaona kuti moyo wa nyama ndi wake ndipo uli m’magazi. Ngakhale kuti lamuloli linaperekedwa kwa Aisiraeli okha, likusonyeza kuti Mulungu amaona kuti ndi kulakwa kwambiri kudya magazi.

  • Machitidwe 15:20. ‘Pewani magazi.’ Lamulo limene Mulungu anapereka kwa Nowa analiperekanso kwa Akhristu. Akatswiri a mbiri yakale amati Akhristu oyambirira ankapewa kudya magazi, ngakhale atagwiritsidwa ntchito ngati mankhwala.

N’chifukwa chiyani Mulungu anatilamula kuti tizipewa magazi?

N’zoona kuti kuikidwa magazi tikadwala kukhoza kuyambitsa mavuto ena m’thupi. Koma chifukwa chachikulu chopewera magazi n’chakuti Mulungu anatilamula zimenezi chifukwa magazi amaimira moyo womwe ndi wopatulika kwa iye.​—Levitiko 17:11; Akolose 1:20.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena