Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 9/8 tsamba 19
  • Maphunziro a Pakoleji—Kukonzekera Kaamba ka Chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maphunziro a Pakoleji—Kukonzekera Kaamba ka Chiyani?
  • Galamukani!—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Maphunziro Owonjezereka Kapena Ayi?
    Galamukani!—1994
  • Makolo—kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Achichepere Kodi Mudzachitanji ndi Moyo wanu?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kuchokera kwa Aŵerengi Athu
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 9/8 tsamba 19

Maphunziro a Pakoleji—Kukonzekera Kaamba ka Chiyani?

ZAKA zochepa zapitazo, wolemba nkhani mu danga la nyuzipepala Bill Reel analemba nkhani yomwe inawoneka mu Daily News, nyuzipepala ya mu mzinda wa New York, mu imene iye anapereka nsonga zodzutsa maganizo ponena za maphunziro a pakoleji.

“Nchiyani chimene mumadziwa pambuyo pa zaka zinayi za maphunziro apamwamba?” iye anafunsa. “Palibe chokhumudwitsa, koma simudziwa zambiri. Eee, mungadziwe zambiri ponena za ndakatulo za Chikondi kapena zopaka utoto za Kubadwanso kwa luso la zochitachita kapena luso la zopangapanga za kompyuta kapena njira zowerengera. Ndikhulupirira munaphunzira zambiri zokwanira kupanga moyo. . . . Komabe palibe aliyense wa zaka 22 amene amadziwa zambiri. Simunakhale kwambiri mokwanira. Nzeru zimabwera kokha ndi msinkhu. Chotero dzichepetseni.

“Mumamaliza maphunziro pa koleji ndi maloto kaamba ka mtsogolo. Mwachisoni, zambiri za zolingalira zanu zidzatembenukira ku phulusa. Sindifuna kukunyazitsani inu, koma mungamvetsere ku chowonadi: Pamene mupeza chuma chimene musirira, ngati mungachipeze, ndipo pamene mufikira zipambano zimene muzilondola, ngati mungazifikire izo, sizidzakukhutiritsani. Mmalo mwake, panthawi imodzimodziyo pamene mudzayembekezera kukhala mukupambana mu chipambano, mudzadzimva kukhala wopanda kanthu mmalo mwa kudzimva wokwaniritsidwa, wopsyinjika mmalo mwa chimwemwe, wokwiyitsidwa mmalo mwa wamtendere.”

Ponena za ziyeso zakuthupi zomwe zidzayang’anizana ndi omaliza maphunziro a pakoleji oterowo, Reel analoza “kuti magazini onse amalunjika pa achichepere a chiAmerica owala, opita patsogolo, olemera,—olunjikitsidwa m’mawu ena, pa inu—ali odzazidwa ndi kusatsa malonda kaamba ka magalimoto owoneka bwino kunja ndi zakumwa zoledzeretsa zapamwamba ndi zovala zaposachedwapa zamakono ndi mastereo okhala ndi mbali zambiri zothandizira kuwoneka bwino zakunja. Ofalitsa nkhani akuyembekezera kukukokani inu kulowa mu mkhalidwe wosatha wa kumwerekera mu kuwononga ndalama kosayenerera kokhazikitsidwa ndi kudziwonetsera kwa mayanjano. Iwo adzayesa mwamphamvu kukukakamizani kuti mofulumira mufunsire kokha chimene mukhumba. Adzayesa kusokoneza zosowa zanu ndi zofuna zanu mu malingaliro anu osindikiza.

“Ambiri a inu mudzanyengedwa ndi osonkhezera osalala a nkhani amenewa, amene ali akatswiri pa kudyerera pa zolakwika zanu za khalidwe. . . . Zopeza zanu zowala sizidzakupatsani chikwaniritso chirichonse. Mchenicheni, mosiyanako. Kufunafuna kwa chuma kuli chikhumbo chosakhutiritsika chomwe chidzakoka moyo wanu.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena