Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 9/8 tsamba 20-21
  • Ntchito ya Magazini ku Japan Ibwera ‘mu Dongosolo’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito ya Magazini ku Japan Ibwera ‘mu Dongosolo’
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugwira Ntchito Kwatawatawa kwa Dongosolo
  • Kugwiritsira Ntchito Chuma Molongosoka
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Magazini Amalengeza Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Kodi Muli ndi Oda Yokhazikika ya Magazini?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 9/8 tsamba 20-21

Ntchito ya Magazini ku Japan Ibwera ‘mu Dongosolo’

KUSINDIKIZA, kulonga, ndi kutumiza makope a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mamiliyoni 3.5 mwezi uliwonse: Iyi ndi imodzi ya ntchito zimene nthambi ya ku Japan ya Watch Tower Society ifunikira kuchita m’malo mofuna kufikiritsa zosowa za Mboni za Yehova m’kuchita ntchito yawo yolengeza mu Japan ndi chiŵerengero cha maiko ena a ku Far East. Ndithudi, kulongosoka kuli mfungulo.

Kuti zifikire kusowaku, Mboni mu Japan zinalinganiza ndipo, pambali yokulira, zinapanga dongosolo la makina lopatsirana limene limachotsapo ntchito zowononga nthaŵi zambiri ndi zofuna ogwira ntchito ambiri, zonga ngati kusonkhanitsa magazini ndi kuchotsanso mu mbali zosiyanasiyana za dongosolo la kugwira ntchito.

Choyamba, chiwiya chokha chimene chinalipo mwa chuma chinali makina a rotari, omwe anali ndi mbali yake ya kulonga, ndi makina okhala ndi mipeni itatu yomwe imadula magazini ku mlingo. Mboni zinapita ku ntchito ndipo zinabwera ndi dongosolo la kugwirizanitsa mbali ziŵirizi ndi zinthu zina zodzipangira okha, kotero kuti chiri chotheka kusindikiza, kusonkhanitsa, kudula, ndi kulonga magazini m’kugwira ntchito kumodzi.

Kugwira Ntchito Kwatawatawa kwa Dongosolo

Kuyang’ana pa zithunzithunzi m’kutsatizana kolongosoka kudzakupatsani lingaliro labwino la mmene kachitidwe ka ‘dongosoloka’ kamagwirira ntchito. Poyamba, pepala kuchokera ku mipukutu iŵiri imalowa mu makina a rotari (chithunzi A) paliwiro la kufika ku mapazi 25 (8 m) pa kamphindi kamodzi. Kuchokera ku malekezero ena amakina (B) kukudza kutuluka kopitirizabe kwa magazini yokongola ya mitundu inayi, chifupifupi makope chikwi pa mphindi imodzi. Ziwiya zopatsirana zozungulira zimatumiza magazini ku makina osonkhanitsa (C), amene amawalekanitsa mu miulu yosatsirizika bwino ya magazini 50 uliwonse.

Ndiyeno magazini osonkhanitsidwawo amatumizidwa ku mbali ya makina yopanikiza (D), yomwe imapereka mphamvu za kupanikiza kufika ku matani 50 pa timphindi tiŵiri ku unyinji umodzi ndi umodzi kuti uchotse mpweya pakati pa masamba. Mbali yokhayi imachotsapo ntchito yonse yophatikizidwapo ya kuchita ndi kuchotsa magazini pa dongosolo la kupatsirana, kuwasonkhanitsa pa matabwa opangidwa bwino kuti akanikizidwe usiku onse, ndiyeno kuwalonganso kapena kuwapereka pa chodulira mu unyinji wa 50, unyinji umodzi panthaŵi imodzi ndi manja.

Pambuyo pa kukanikizidwa, madongosolo aŵiri onyamula magazini amakumana ndi kupanga imodzi ndiyeno kutumizidwa ku chodulira (E), chomwe chimadula magazini ku mlingo. Malamba onyamula magazini amatenga magazini, odulidwa bwino tsopano ndi kulinganizidwa bwino kuwapereka, ku mbali yolongeza yodzipangira wokha (F), ku imene amaikidwa mu makatoni, omwe amatsekedwa ndiyeno ndi kuikidwa maadresi ndi kompyuta, okonzekeretsedwa kuperekedwa ku galimoto lalikulu lomwe limakhala loyembekeza pa malo olongera.

Kugwiritsira Ntchito Chuma Molongosoka

Kodi ziwiya zoyenera zimenezi ziri zofunikadi? “Ngati tikanachita ntchito yokulira iripoyi tsopano ndi makonzedwe akale,” anatero Yasuyuki, woyang’anira wa kagwiridwe ka ntchito yonseyo, “tikanafunikira kuwonjezera chifupifupi antchito khumi ku antchito onse. Ndipo icho chiri chakuti ngati tikanapeza malo osungira magazini onsewo m’dongosolo lake.” Ndi kachitidwe ka ‘dongosoloka’, anthu oyendetsa makina 11 ogwira ntchito monga gulu angatulutse magazini 54,000 pa ora. Chiri chopepuka kuwona chifukwa chimene Mboni pa nthambiyi ziriri zosangalala kwenikweni kuti kugwira ntchito kwa magazini a Chijapani kunapeza ‘dongosolo.’

[Zithunzi pamasamba 20, 21]

A. Makina a Rotari

B. Magazini kuchokera ku makina yosindikizira

C. Kuchokera ku malamba onyamulira kufika ku kusonkhanitsa

D. Mbali ya makina yopanikiza

E. Chodulira

F. Mbali yolongeza

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena