Kodi Muli ndi Oda Yokhazikika ya Magazini?
1 Kodi munayamba mwapita kumsonkhano wa utumiki wakumunda ndi kupeza kuti m’chikwama chanu mulibiretu magazini? Chabwino, kumbukirani mphatika ya mutu wakuti “Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa,” yopezeka mu Utumiki Wathu Waufumu wa September 1995. Inatiuza ‘kukhala ndi oda yoikika ya magazini,’ ikumati: “Lembetsani oda yokuyenerani kwa mbale wosamalira magazini ya unyinji wodziŵika wa makope a magazini alionse. M’njira imeneyi, inu ndi banja lanu mudzakhala mukulandira magazini okwanira mokhazikika.” Kodi mwachita zimenezi?
2 Bwanji osalembetsa oda yokhazikika ya magazini? Mudzakakamizika kugaŵira magaziniwo mlungu uliwonse, ndipo mwa kuchita zimenezi mudzapeza chimwemwe chochuluka. Ngati muli nayo kale oda yokhazikika, onani ngati chiŵerengero cha magazini amene mumalandira chikugwirizana ndi magazini amene mumafunikira mwezi uliwonse mu utumiki. N’zoona, tifunika kukhala odalirika potenga oda yathu mlungu uliwonse ndipo tiyenera kuchita zimenezo. Ngati mungachoke pampingopo kwa nthaŵi yaitali, muuzeni wosamalira magazini ngati mukufuna kuti magaziniwo aziwapereka kwa munthu wina mpaka inu mutadzabwera.
3 Mphatika imene yatchulidwa pamwambayi inanenanso kuti tiyenera “kulinganiza tsiku la magazini lokhazikika.” Kodi mudzachirikiza Tsiku la Magazini mlungu uliwonse? Monga mmene zasonyezedwera pa Kalenda ya 1999 ya Mboni za Yehova, limeneli ndi Loweruka lililonse pachaka! Musachepetse kufunika kogaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pamene tiyesetsa kutengamo mbali mokwanira m’ntchito ya magazini, ndiye kuti ‘tikudza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino’ kwa anansi athu.—Yes. 52:7.