“Ngwazi ya Nkhokera”
Khate liri nthenda yowopsya yomwe imayambukira mwinamwakwe anthu ochulukira pa mamiliyoni 15, makamaka mu Africa, India, Burma, Thailand, ndi mbali zina za South America. Tsopano armadillo yokhala ndi mizere isanu ndi inayi pathupi ikuwonedwa monga “ngwazi ya nkhokera” mu kumenyana kwa munthu molimbana ndi matendawa.
Koma ndimotani mmene nyama yochepa imeneyi yomwe iri chifupifupi mapazi aŵiri mu utali (61 cm), yolemera kufikira ku mapaundi 15 (6.8 kg) ndipo yokhala ndi chikamba chopangidwa ndi mafupa olimba ndi osalala, yagwirizanira mu kumenyanaku?
Chabwino, chapezedwa kuti nyama zokha zopambana ku khate la anthu ziri makoswe ndi armadillo. Chotero asayansi akugwiritsira ntchito armadillo kupanga mankwala oyamba ochinjirizira molimbana ndi khate, popeza kuti makoswe amatulutsa unyinji wochepa kwambiri wofunikira kugwiritsiridwa ntchito. Armadillo imodzi yoipitsidwa imakhala ndi mankhwala 750 ochinjiriza. Tsopano, minda yapadera yakhazikitsidwa mu United States ndi Britain kuti ichulukitse nyama yochinjirizayo.