Dziko Lapansi Chiyambire 1914
Gawo 6: 1946-1959 Kupita Patsogolo Konyenga Pakati pa Mtendere Womwe Sunalipo
“DZIKO la lerolino kaya tikulifuna kapena ayi, liri chotulukapo cha Hitler,” akunena tero wopeza mphotho ya olemba ndiponso wolemba nkhani mu nyuzipepala Sebastian Haffner. Iye akulongosola kuti: “Popanda Hitler sipakanakhala malire a Germany ndi Europe; popanda Hitler sipakanakhala anthu a ku America ndi ku Russia mu Berlin; popanda Hitler sikukanakhala Israel; popanda Hitler sipakanakhala kutha kwa kulamuliridwa ndi dziko lina, sipakanakhala ufulu wa kulamulira mu Arab ndi akuda mu Africa ndipo sikukanakhala kugwa kwa Europe.”
Ndithudi atsogoleri ena a dziko a mtsikulo nawonso anachita zithu zokhala ndi chotulukapo chachikulu. Mwachitsanzo, “odziŵa za mbiri yakale amakono ambiri analondola kugawanika kwatsopano kwa East-West kwa Europe ku zosankha zofikiridwa pakati pa Akulu Atatu [pa] [Msokhano kumapeto kwa 1943] pa Tehran,” ikunena tero magazini ya ku Canada Maclean’s. Ikupitiriza kuloza mwachindunji, ngakhale kuli tero, kuti “[Msonkhano wochitidwa mu February 1945] mu Yaita unadziŵika kwambiri pakati pa anthu odziŵa za mbiri yakale . . . monga msonkhano pa umene Stalin anachenjeretsa anzake onse Akumadzulo ndi kuba ufumu . . . Mkati mwa milungu magulu ankhondo a Stalin analimbikitsa ndi kukulitsa kukangamira kwawo pa Eastern Europe . . . nkhondo ya zida inali kutha, koma Nkhondo Yoputana ndi Mawu inali itangoyamba kumene.”
Nkhondo Yoputana ndi Mawu? Inde. Aka ndi kanenedwe komwe Bernard Baruch, mlangizi wa presidenti wa ku U.S. anagwiritsira ntchito mu 1947 kulongosola mkangano pakati pa United States ndi Soviet Union. Inali Nkhondo Yoputana ndi Mawu yomenyedwa pa ndale zadziko, ndi za chuma, ndi makonzedwe kaamba ka za mtsogolo.
Pakutha kwa nkhondo Mphamvu zothandizana zinagawa Germany m’mbali zinayi zokhalidwa. A French, a British, ndi anthu a chiAmerica anatenga mbali za kum’mawa. Chotero magulu a maiko ophatikizana anakhalako limodzi la demokratiki ndi lina la komyunisti. Kuyambira pamenepo, iwo akhala akuyang’anizana ndi diso la nkhwezule modutsa nsalu yochinga yachitsulo yosawoneka.
Berlin nayonso inagawidwa mu zigawo zinayi. Popeza mzinda waukulu wa Germany unaikidwa mkati mwa gawo la Soviet, zinthu zoyenera kupita ku madera ake a British, French, ndi aku America zinayenera kudutsa mugawo la Soviet. Ichi chinapangitsa mavuto, ndipo mkati mwa 1948 anthu a ku Soviet anatsekeredwa njira zonse za pamtunda zochokera ku Berlin kumka ku Madzulo. Mphamvu za kumadzulo zinayankha mwakunyamula ndi ndege zakudya zawo zonse zofunika ndi mafuta. Kufikira pa kutha kwa miyezi 11 pambuyo pake, kutsekedwa kwa Berlin ndipo kunyamula zinthu kwa m’mlengalenga kunapititsa patsogolo kukwinjika kwa Nkhondo Yoputana ndi Mawu.
“Chifupifupi usiku wonse,” akulemba tero Profesala Alfred Grosser wa pa Yuniversite ya Paris, “Berlin anasintha fanizo lake kuchokera ku chizindikiro cha gulu lankhondo la Prussia ndi ulamuliro wankhalwe wa Hitler m’chizindikiro cha ufulu.” Lerolino, Berlin idakali chizindikiro chotchuka, ndipo anthu andale ponse paŵiri a Kum’mawa ndi Kumadzulo nthaŵi zina amachigwiritsira ntchito kaamba ka kusonkhereza malaŵi a Nkhondo Yoputana ndi Mawu.
Masiku asanu isanathe Nkhondo ya Dziko II, Soviet Union inalengeza nkhondo pa Japan ndipo inalowelera Korea wolamulidwa ndi anthu a ku Japan kumpoto kwake. Pamene Japan anagonjera mphamvu zothandizana zinavomereza kuti ankhondo a ku Japan akumpoto kwa mzera wa 38 ayenera kuperekedwa ku Soviet ndi aja a kumwera kwa mzera umenewu ku America. Mu 1950 kugawa dziko kosakhala kwachilengedwe kumeneku kunatsogolera ku nkhondo. Nkhondoyo isanathe chifupifupi maiko 20 anaphatikizidwa mu nkhondo, ndipo oposa 40 ena anapereka zida za nkhondo kapena zogwiritsira ntchito. Pa July 27, 1953, kuleka nkhondo kunayamba kugwira ntchito pambuyo pa kufa kwa mazana zikwi za anthu. Kaamba ka chiyani? Lerolino, kuposa pa zaka 30 pambuyo pake, yankho ku vuto la ku Korea silinapezedwe. Amatcha kumwazikanako Bamboo Curtain.
Mneneri Danieli anawoneratu kuti kukangana koteroko kudzachitika pakati pa mafumu aŵiri ophiphiritsira. Nkhondo Yoputana ndi Mawu yapatsa mafumu aŵiri amphamvu zazikulu a lerolino nthaŵi ya kukambitsirana wina ndi mnzake, m’kupitiriza lamulo lawo la nthaŵi yaitali la kulankhula “pagome limodzi bodza.” Chotero iwo alondola zikondwerero za utundu, pamene pa nthaŵi imodzimodziyo akudzilowetsa mokangalika m’kuvomereza “kukankha” kolimbana wina ndi mnzake kaamba ka mwaŵi waumwini.—Danieli 11:27-45.
“Kubadwa Kokwanira kwa Makanda” Osalamulirika
Pamene bomba la atomu linaphulitsidwa poyamba mwachipambano mu New Mexico, U.S. prezidenti Truman anatumiziridwa uthenga wachinsinsi woŵerengedwa kuti: “Kubadwa kokwanira kwa makanda.” Koma ndi osalamulirika ndi owumirira chotani nanga mmene makanda amenewa anatembenukira kukhala! Anagawanitsa mitundu, yaikulu ndi yaing’ono m’chimango chosayembekezereka cha ankhondo a dziko lonse, kuwakakamiza iwo kuwononga ndalama zomwe akanagwiritsira ntchito kudyetsa ndi kuphunzitsa zosowa zawo. Alimbikitsa lamulo lowopsya la kusungirira mtendere mwa kulinganiza mantha. Anapatsa gulu la Mitundu Yogwirizana ufulu wonse wa kulingalira mkangano uliwonse wa mtundu kapena mitundu yonse, mosasamala kanthu kuti ndi ochepa chotani, iwo ali chipiyoyo chosapeweka cha nyukliya. Iwo anayeneretsa kukhazikitsidwa kwa magulu atsopano osunga mtendere onga ngati NATO (North Atlantic Treaty Organization) mu 1949 ndi Warsaw Pact mu 1955.
Pamene unyinji wa “makanda” a atomiki ndi mtundu wa makolo awo wakula, yatero nayonso ngozi ya nkhondo ya nyukliya ya dziko lonse. Alipangitsa dziko kuthunthumira ku “mantha ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza kudziko lapansi.”—Luka 21:26.
Chotero ngati kuliza mfuti komwe kunayambidwa ndi Nkhondo yomenyera Ufulu ya U.S. mu 1775 kunali “kuliza mfuti komwe kunamveka dziko lonse,” monga mmene wolemba ndakatulo Ralph Waldo Emerson anaitcha iyo, chotero kuphulika kwa bomba la atomu komwe kunatha Nkhondo ya Dziko II mu 1945 motsimikizirika kunali ‘kuphulika komwe kunamveka dziko lonse.’
The World Book Encyclopedia imatiuza ife ponena za “makanda” ena osalamulirika amene anabadwa mokwanira mkati mwa nthaŵi ya pamapeto pa nkhondo. Kulozera ku “Kubuka kwa Mitundu Yatsopano,” iyo ikulongosola kuti: “Limodzi ndi limodzi, Great Britain, France, Belgium, Netherlands, ndi maiko ena akulu omwe amalamulira pa maiko anzawo anafooketsedwa ndi zotayikiridwa zawo mkati mwa nkhondo. Sakanalamuliranso maiko ena mokakamiza.” Pakati pa maiko oyambirira kupeza ufulu panali Indonesia, Philippines, Pakistan, India, Ceylon (tsopano lotchedwa Sri Lanka), Israel, Libya, Tunisia, ndi Ghana.
Kupondezera kwa ufulu wandale kunapitiriza kufikira tsiku lino ndipo chatulukapo m’kubadwa kwa chifupifupi mitundu yatsopano zana limodzi chiyambire 1945.
Kulamulira pa maiko ena kunali ndi zobweza m’mbuyo zake, koma chomwe chinalowa mmalo mwake sichiri moyenerera chabwinopo. Wolemba nkhani m’danga la nyuzipepala wovomerezedwa Georgie Anne Geyer anadziŵa kuti: “Pamene maiko olamulira pa maiko ena anatha, ambiri a maiko atsopano anayamba chimene chikanadzakhala nyengo imodzi yaitali ya kugwa kwa pang’onopang’ono kaŵirikaŵiri yozindikiridwa ndi nkhondo ya chiweniweni.” Chotero chakula chitsimikiziro chakuti munthu sangadzilamulire yekha mwachipambano.—Mlaliki 8:9; Yeremiya 10:23.
Kupita Patsogolo—Koma kwa Mtengo ndi Konyenga
Mu 1945 nzika za m’dziko losakazidwa ndi nkhondo la Europe ndi Asia zinali m’mavuto. Kaamba ka zifukwa za umunthu, komanso zosonkhezeredwa ndi zikondwerero zaumwini, mphamvu zothandizana zinakonza Programu ya Kupezanso ya ku Europe. Linali bungwe lomwe linapereka thandizo m’kumanganso ma indastri a ku Europe omwe anaphulitsidwa ndi mabomba odziŵika kwambiri monga Marshall Plan yotchedwa pambuyo pa mlembi wa boma la U.S. amene anayambitsa lingalirolo, programuyi ya chichite wekha; ngakhale inali ya mtengo, inali yopindulitsa.
Kubwezedwanso kwa chuma ku maindastri kunali kodabwitsa. Maindastri amakono odzaza ndi makina amakono anatheketsa maiko ogonjetsedwa kukhala bwino, ndipo mwinamwake kupitirira, maiko apafupi, opambana omwe kaŵirikaŵiri anakakamizidwa kugwiritsira ntchito makina ndi zogwirira ntchito zakale. Mkati mwa ma 1950 yomwe inatchedwa chozizwitsa cha chuma cha Germany chinali kugwira ntchito, ndipo podzafika kumapeto kwa nyengo ya zaka khumi, Japan anayamba programu yomanga yomwe ikatheketsa iye kugonjetsa mbali yaikulu ya dziko mu za malonda.
Opambanawo, pa nthaŵiyi, analinso kuyesayesa kubwezeretsa malamulo awo am’dziko ndi a zachuma ku mkhalidwe wabwino. Kumangidwa kwa nyumba ndi kupangidwa kwa zinthu zogwiritsiridwa ntchito pa nyumba kunadukizidwa kwenikweni mkati mwa nkhondo, pamene zinthu zonse zinalunjikitsidwa ku kupangitsa nkhondo. Tsopano panali msika waukulu kaamba ka zinthu zomwe anthu anasiya kalekale kuzigwiritsira ntchito. Ichi chinatanthauza ntchito kaamba ka onse kwa kanthaŵi, kusowa ntchito sikunali vuto. Dziko tsopano linali kupita kulinga ku nthaŵi ya kupita patsogolo komwe kunali kusanawonekepo chiyambire kusanafike Kupsyinjika Kwakukulu.
Koma kupita patsogolo kunali ndi mtengo wake. Amayi ambiri anatenga ntchito yakuthupi kunja kwa nyumba, nthaŵi zina kunyalanyaza ana m’kuchita chimenecho. Kukwera kwa miyezo ya makhalidwe kunatheketsa kukhala ndi zosangulutsa zochuluka, koma nthaŵi zonse sichinali chabwino. Kupenyerera TV kunayamba kulowa m’malo mwa kukambitsirana kwa banja. Kusweka kwa moyo wa banja kunatsogolera ku kuwonjezeka kwa kutha kwa zikwati. Mkhalidwe umenewu pambuyo pake unalinganizidwa pang’ono ndi chikhoterero chomakulakulabe cha anthu osakwatira akukhala pamodzi popanda ukwati. Mikhalidwe yonse iŵiri inapangitsa kukula kwa chikhoterero cha kugogomezera zikondwerero zaumwini pa chivulazo cha ena. Mapindu auzimu ndi a makhalidwe abwino, opasulidwa kale ndi nkhondo, tsopano anali kuchotsedwa.
Mtendere Weniweni ndi Kupita Patsogolo
Monga onse, magulu azipembedzo zadziko sanawone kuipa kulikonse m’kutumiza ziwalo zawo kukapha anthu anzawo mkati mwa Nkhondo ya Dziko II. Chotero tsopano sanawone choipa chirichonse m’kupereka chirikizo la makhalidwe ndi la kuthupi ku Nkhondo Yoputana ndi Mawu ndi kuukira kwa ndale kotchedwa nkhondo za ufulu. Koma kunali kusiyana kumodzi kowoneka bwino.
Mboni za Yehova zinasungirira uchete Wachikristu mkati mwa Nkhondo ya Dziko II ndi pambuyo pake. Zikuchira kuchokera ku kuyesayesa kwa Hitler kuziwononga izo, chiŵerengero cha Mboni zokangalika mu Germany chinawonjezeka kuchokera ku ochepera pa 9,000 mu 1946 kufikira ku oposa 52,000 mkati mwa zaka zisanu. Pakati pa 1945 ndi 1959, anawonjezereka m’dziko lonse kuchokera pa Mboni 141,606 m’maiko 68 kufika ku 871,737 m’maiko 175. Pamene ziwalo za zipembedzo zina zambiri zinali mowonjezereka pa nkhondo wina ndi m’nzake pa nkhani za ndale ndi mayanjano, limodzinso ndi kusakhazikika chifukwa cha kutsika kwa kukhala chiwalo cha tchalitchi, Mboni za Yehova, m’njira yauzimu zinali kusangalala ndi mtendere weniweni ndi kupita patsogolo.
Ichi chinawonekera pa Msonkhano wawo wa Mitundu yonse wa Chifuno Chaumulungu mu 1958 mu Mzinda wa New York, pamene chiŵerengero chapamwamba cha opezeka pa gawo limodzi chinali choposa 250,000. Mlankhuli woikidwiratu ananena kuti: “Kuli kukula kopita patsogolo kwa paradaiso wauzimu komwe kumalongosola chimwemwe chosefukira cha Mboni za Yehova . . . Paradaiso wauzimu ameneyu amachitira chithunzi ulemerero wa Mulungu ndipo amatsimikizira kukhazikitsidwa kwa ufumu wake.”
Mtendere womwe unatsatira Nkhondo ya Dziko II, kwenikweni mtendere womwe sunalipo limodzi ndi kupita patsogolo kwa kukonda zinthu zakuthupi komwe kunakwezedwa, kunaloza ku nsongayi yosatsutsika: Mtendere weniweni ndi kupita patsogolo kungabwere kokha kupyolera mu Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu. Mkati mwa “Ma-1960—Nthaŵi ya Mtsutsano Wosalamulirika,” ichi chikakhala chowonekeratu bwino kwambiri. Ŵerengani za ichi m’kope lathu lotsatira.
[Bokosi patsamba 12]
Zinthu Zina Zimene Zinapanga Mbiri
1946—Ho Chi Minh alengeza kumenya nkhondo ya ufulu mu
Vietnam
1947—Dead Sea Scrolls, kuphatikizapo nkhani zakale
zolembedwa za mu Baibulo, zipezedwa
1948—Mohandas Gandhi aphedwa
1949—Khamu la anthu a nkhondo ya ufulu limaliza kulanda
mbali ya pakati ya China; Boma limene silinali la
chikomunisti linabwerera ku chisumbu cha Taiwan
1950—Zipolowe zotsutsana ndi tsankho la khungu mu
South Africa
1952—United States aphulitsa bomba loyamba la haidrogeni
1954—Bwalo lalikulu koposa la milandu la U.S. linalengeza
kuti kusankhana kwa utundu m’masukulu kuli kopanda
lamulo
1957—Soviet itumiza satellite ya pa dziko lapansi yoyamba,
Sputnik I, kuyamba kuzungulira dziko
1958—European Economic Community (Msika wa onse) unayamba
kugwira ntchito
1959—Rocket ya Soviet inaperekanso zithunzithunzi za mwezi
ku dziko
[Chithunzi patsamba 13]
Kupita patsogolo kwa pamapeto pa nkhondo kunabweretsa nyumba zabwino ndi magalimoto atsopano kwa mabanja ambiri
[Mawu a Chithunzi]
H. Armstrong Roberts