Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Nchifukwa Ninji Zinthu Zanga Zifunikira Kukhala za Udongo Chotero?
“Iyi ndi nthaŵi yotsiriza imene ndidzakuuza iwe. Yeretsa chipinda chako!”
KODI ichi chikumveka kukhala chozoloŵereka kwa inu? Icho chingakhale, popeza kuti oŵerengeka a ife tiri ndi chizoloŵezi cha chibadwa kulinga ku udongo.
Komabe, kufunika koteroko kungawonekere kukhala kosayenera kwa inu. Inu mungakonde chipinda chanu kukhala chosakometseredwa pang’ono. Pambali pa icho, popeza kuti pangakhale malamulo ambiri kaamba ka nyumba yonse, kodi pafunikiranso kukhala malamulo ponena za njira imene mungasungilire chipinda chanu? Inu mungadzimve kuti popeza kuti simukumwa kapena kugwiritsira ntchito anamgoneka monga achichepere ena, cholakwa chaching’ono chimodzi chonga ngati kusakometsera sichiri chinthu chachikulu. Ndipo kodi sichiri chowona kuti inu muli ndi mabwenzi omwe zipinda zawo ziri zauve kwambiri? Nchifukwa ninji, pamenepo, chimene makolo ena amapangira kugogomezera ponena za udongo? Kodi iwo ali ndi zifukwa zenizeni za kuchitira tero?
Udongo Molimbana ndi Kusakometsera
Inu mungakonde kuti makolo anu atsatire uphungu wa profesala mmodzi wa za malingaliro yemwe ananena kwa makolo kuti: “Chosankhapo chanu chabwino chiri kungotseka chitseko ku chipinda chonyansa.” Ena, ngakhale kuli tero, amalingalira kuti makolo ali ndi malingaliro abwino a kufunira udongo. Katswiri wa za malingaliro Paul Adams wagwidwa mawu mu Ladies’ Home Journal kukhala monga akunena kuti: “Chimapanga nzeru kuuza mwana kuti chipinda chake chifunikira kukhala chaudongo. Longosolani zomwe sizifunikira kuchitidwa. Nenani kuti ngati iye sadzasunga chipinda chake chogonamo kukhala chaudongo mochepera ndiko kuti inu mudzachotsako maubwino ena ake.”
Mutalingalira ponena za icho, makolo anu ali ndi kuyenera kwa kuika malamulo ngakhale kaamba ka chipinda chanu, kodi iwo alibe? Iwo anawononga nthaŵi yochulukira ndi ndalama kotero kuti inu mukhale ndi chipinda chanuchanu, ndipo mwinamwake anachidzaza icho ndi zinthu. Chotero iwo moyenera angaike malamulo onena za kuchisamalira kwake. Inu mudzachipeza kukhala chopindulitsa kulabadira iwo.
Henry W. Longfellow, mu ndakatulo yake The Builders, anagogomezera kanenedwe kakuti, “Chinthu chirichonse m’malo ake chiri chabwino.” Motsimikizirika makolo anu amadzimva kuti ichi chiri chowona, popeza kuti pali mapindu a kukhala “ndi chinthu chirichonse m’malo ake.” Kodi ndi ati omwe ali ena a iwo?
Mapindu Ena a Udongo
Phindu lenileni limodzi liri lakuti chiri chopepuka kupeza zinthu. Munthu wosakhala waudongo angawononge nthaŵi yochulukira kufunafuna mfungulo, chipeso, kapena kansalu kominira, kusanenapo chirichonse ponena za nsapato ina ija yomwe mwanjira ina yake inakankhidwira pansi pa kama. Ndiponso, zovala zimakhala zoyera ndi kusungirira kusitidwa kwawo, ndipo chotero zimakhala kwa nthaŵi yaitali zitakolowekedwa moyenera. Ndiponso, sipamakhala ngozi ya kukhumudwa pa zinthuzo kapena nsapato zomwe zaikidwa m’malo ake. Ichi chiri kwenikweni chofunika pamene mukugawana chipinda ndi mbale kapena mlongo.
Pamwamba pa zonse, pamene chiwalo chirichonse cha banja chichita mbali yake, kusunga chipinda chake chaudongo ndi choyera, chimachepetsako katundu kwa ena ndipo chotero chimathandizira ku banja la chimwemwe. Kuloza ku ichi Carolyn wa zaka za kubadwa 14 walemba kuti: “Amayi ali ndi ntchito yonga iyi ya kuchita panyumba pano. . . . Pali achichepere asanu ndi mmodzi pambali pa ine ndipo palibe ndi mmodzi yense yemwe amadzisamalira bwino lomwe ndipo amayi amafunikira kutero ndipo ali ndi ntchito yoipa.” Chikanakhala kuti ana asanu ndi aŵiri amenewo anasunga “chinthu chirichonse m’malo ake,” icho motsimikizirika chikanachepetsako katundu wa amayi awo, kodi icho sichikanatero?
Phindu lina liri lakuti ngati musunga chipinda chanu kukhala chaudongo, inu mwachiwonekere mudzachita chofananacho m’mbali zinanso. Chizoloŵezi chimenechi chaudongo chidzasonyezedwanso m’njira imene mumasamalira galimoto la banja ndi zinthu zina ndipo icho mwachiwonekere chidzakhalirira ngakhale ku uchikulire. Tsiku lina pamene inu mudzafuna kugwira ntchito ya kuthupi, kumveka kaamba ka udongo kungatheketse ngakhale kuthekera kwanu kwa kupita patsogolo—chiyembekezo chabwinopo, kodi simukuganiza tero?
Kuti chiri choyenerera kumvera malamulo a makolo anu chatsimikiziridwanso ndi zotsatirapozi: Achichepere ambiri ali ofunitsitsa kuyendetsa galimoto. Koma kodi ndi liti pamene afunikira kuyamba? Osati kwenikweni pamene iwo afikira msinkhu wofunidwa mwalamulo. Adokotala J. E. Schowalter ndi W. R. Anyan, Jr., alongosola mu The Family Handbook of Adolescence: “Pamene wachichepere angadaliridwe kutsatira malamulo ndipo ali wodalirika mwachisawawa, chiri chachidziŵikire kuti maluso amenewa adzalamulira mkhalidwe wake pamene akuyendetsa galimoto.” (Kanyenye ngwathu.) Kodi simumadzimva, pamenepo, kuti chiri chophulapo kanthu kudziphunzitsa inu eni kukhala wodalirika ndi kukhulupirika ndi kutsatira malamulo ngakhale m’kusamalira chipinda chanu? Baibulo limanena kuti ali: “Iye amene akhulupirika m’chaching’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu.”—Luka 16:10.
Kwa achichepere Achikristu, ngakhale kuli tero, chifukwa chachikulu kaamba ka kukhalira waudongo ndi wosamalitsa chinapatsidwa ndi mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo, koma wamtendere.” Iye analembanso kuti: “Khalani akutsanza Mulungu, monga ana okondedwa.”—1 Akorinto 14:33; Aefeso 5:1.
Kulongosoka kumeneku kumbali ya Mulungu kunali kowonekera m’makonzedwe amene iye anapanga m’kachisi, kapena chihema, cholambiriramo cha mtundu wa Israyeli. Kokha ziwalo za banja la ansembe (Alevi) zinaloledwa kulowa mkati mwa kachisi. Ndiponso, Yehova analola Mose kulemba kumene kwenikweni chinthu chirichonse m’kachisi chinafunikira kuikidwa, ndipo Iye anapereka malangizo atsatanetsatane onena za mmene ansembe ndi Alevi anafunikira kuchita ndi izo. (Eksodo 40) Mwanjirayi, Aisrayeli osakhala Alevi anakhoza kulingalira chirichonse chomwe chinkachitika m’kachisiyo m’chigwirizano ndi kulambira kwawo Yehova. Ichi motsimikizirika chikawapanga iwo kudzimva kukhala mbali ya malamulowo ndi kuwapatsa iwo kudzimva kwakukhala mbali yake. Kodi inu simukulingalira kuti iwo anali osangalala kwenikweni kuti Yehova anali Mulungu wa dongosolo?
Chomwe Chingachitidwe Ponena za Chipinda Chija?
Ndimotani pamenepo, mmene mungapangire kulungamitsa m’chipinda chanu? Monga momwe zanenedwera poyambirirapo, makolo anu angakhale kale ndi zofunika zachindunji. Koma pali zochulukira zomwe mungachite pa kudziyambirapo kwanu. Yambani ndi zenizeni: Kolowekani chovala chirichonse chomwe chiri pansi. Zokolowekako zovala zidzasunga mashati, mabulauzi, ndi madresi kukhala audongo. Pokoloweka nsapato (kapena chola cha pulasikiti cha nsapato) chidzachita zozizwitsa m’kusunga nsapato kukhala m’malo ake, kuwongolera kawonedwe ka mosungira zovala. Bwanji ponena za zovala za dothi? M’malo mwa kungoziponya kokha pa ngondya, bwanji osangokhala ndi choikamo kapena mwinamwake chola kokha kaamba ka chifunocho? Kenaka, kama. Mphindi zoŵerengeka pa tsiku zimapanga kusiyana pakati pa kama lowoneka mwauve ndi laudongo. Bwanji osapanga chosankha kaamba ka laudongo?
Tsopano kaamba ka zinthu zomwe siziri zenizeni. Sankhani drowa imodzi mu chipinda panthaŵi imodzi ndipo gwirirani ntchito pa iyo, kutaya zinthu zopanda ntchito zirizonse ndi kuika zinazo m’malo ake. Inu mungafune kuika mudrowa mabokosi ena ang’ono a mapepala kapena zola za pulasitiki, mukugwiritsira ntchito imodzi kaamba ka zovala zanu za mkati, inayake kaamba ka masokosi a afupi kapena atali, ndi kupitirizabe. M’nthaŵi yochepa chipinda chanu chidzakhala ndi kawonekedwe kosiyana kotheratu, ndipo mudzakhala mukukulitsa lingaliro la kudzimva ponena za iyo.
Achichepere—Yang’anani Mtsogolo Mwanu
Kodi chiri choyenera nthaŵi yochulukira chotere ndi kuyesayesa kwa kuphunzira kukhala waudongo? Carol, yemwe tsopano ali m’zaka zake za ma-20, amakumbukira kumenyera kumene iye anali nako. Ngati amayi ake anapeza chipinda cha Carol chosakhala kumlingo wofunika (mwachitsanzo, ngati masokosi a afupi ndi zovala za mkati sizinali zopindidwa mwaudongo mudrowa), iwo ankangodzichotsamo mu drowamo ndi kuziika pansi ndi kuleka Carol kubwezeretsa zinthu zonse mwaudongo. Kapena, monga chilango, Carol anasungidwa kukhala pamodzi kothera kwa mlungu konse.
Akuyang’ana kumbuyo, kodi Carol amadzimva kuti amayi ake anali osalingalira? “Ayi, ndinaphunzira zambiri kuchokera ku chimenecho. Tsopano ndimadziŵa kusita zovala zanga ndi mmene ndingasungire zinthu zaudongo ndi zoyera. Mwinamwake osati kumlingo wabwino wa Amayi, koma ndingasiye chifupifupi chitseko cha chipinda changa chogona chiri chotseguka.”
Ngati Carol adzakhala ndi ana a iyemwini mtsogolo, kodi nchiyani chimene iye adzawaphunzitsa iwo ponena za udongo? Iye analongosola kuti: “Sindiganiza kuti ndidzafufuza madrowa awo, koma ngati chipinda chawo chiwoneka chaudongo, chidzakhala CHABWINO.” Atafunsidwa ponena za uphungu umene iye anali nawo kaamba ka achichepere, Carol anayankha kuti: “Labadirani malamulo a makolo anu onena za udongo. Inu potsirizira pake mudzachipanga icho kukhala chizoloŵezi.”
Chanenedwa kuti munthu ali cholengedwa cha zizoloŵezi. Zina za zizoloŵezi zimenezi ziri zopindulitsa, zina siziri. Ndipo, Elbert Hubbard analemba mwanzeru kuti: “Kulitsani kokha zizoloŵezi zomwe muli ofunitsitsa kuti zidzakulamulireni.”
Kodi ndi zizoloŵezi zotani zimene mungafune kuti zikulamulireni—zija zaudongo kapena zosakhala zaudongo? Pamene musinkhasinkha pa ichi, sungani m’malingaliro mapindu a chizoloŵezi chaudongo: Chiri ndi maziko a m’Malemba, chimasunga nthaŵi ndi ndalama, chimamangirira ulemu waumwini, chimamangirira ulemu wa inu mwa ena. Ndipo chotsirizira ndipo osati chokhacho, chiri lingaliro lolongosoledwa ndi Carolyn wachichepere: “Amayi anga ndithudi amafunikira chithandizo changa, ndipo amachiyamikira icho mochulukira pamene ndiwathandiza iwo.”
[Zithunzi pamasamba 22, 23]
Ndi chiti chomwe mungasankhepo: ichi . . . kapena ichi?