Pompi Yodabwitsa ya Mtengo
Masamba omwe ali m’mwamba mu mtengo amafunikira madzi ndi zakudya, kaŵirikaŵiri zikwi za magaloni pa tsiku. Awa amafunikira kukwezedwa m’mwamba, koma motani?
“Kutulutsa madzi kozizwitsa kumeneku kumayambira pansi mu nthaka kumene mamiliyoni a zidutswa zazing’ono za mizu zimasonkhanitsa madzi ndi zakudya zofunika zosungunulidwa,” ikulongosola tero Compressed Air Magazine. “Pamene madzi akugwiritsiridwa ntchito, kusoweka kumapangidwa m’masamba komwe kumapangitsa zofunikazo kukwera m’mwamba ndipo m’chenicheni kukoka madzi owonjezereka kuchokera mu nthaka. Palibe makina operekera madzi opangidwa ndi munthu omwe angapereke madzi kuposa pa chifupifupi mamita 10.” Koma bwanji ponena za dongosolo la kupereka madzi la mtengo?
Liri lozizwitsa kwambiri kotero kuti kwanenedwa kuti lingakhoze, ngati kuli koyenerera, kupereka madzi mu mtengo kwa chifupifupi makilomita atatu m’mwamba! Nchosadabwitsa kuti kusatsa malonda kochitidwa ndi kampani yopanga mapompi yotchuka kumakokera chisamaliro ku “pompi yozizwitsa” ya mtengo wa maple ndipo imavomereza kuti: “Sitingalingane ndi chilengedwe m’kuleza mtima kapena kachitidwe.”