Sitolo Yochedwetsedwa
Chithunzithunzi choseketsa cholembedwa posachedwapa mu “Scranton Times,” ya Scranton, Pennsylvania, chinapanga ndemanga ponena za kuchedwetsedwa kotalika kwa tauniyo kumaliza makonzedwe kaamba ka sitolo yogulako zinthu. Chithunzithunzi chimodzi chinanena kwa chinzake kuti: “Chikuwoneka ngati chikutenga nthaŵi yosatha kuyamba sitoloyo!” chinacho chinayankha kuti: “Iwo ayenera kuitcha iyo ‘Sitolo ya Nyumba ya Ufumu!’ Mboni za Yehova zidzaimanga iyo m’masiku 3!”
M’maiko ambiri Mboni za Yehova zikudziŵidwa mofala kaamba ka mazana angapo a Nyumba za Ufumu zawo zomangidwa mofulumira. Iwo ali ndi magulu omanga ophunzitsidwa mwapadera ndi kulinganiza kwabwino kwapasadakhale. Monga chotulukapo, Nyumba za Ufumu zikumangidwa kuchokera m’maora 30 kufikira masiku 4. Ndipo anthu akuchiwona icho.