Mtsogolo mwa Chipembedzo M’chiyang’aniro cha Nthaŵi Yake ya Kumbuyo
Gawo 14:622 C.E. kupita mtsogolo—Kugonjera ku Chifuniro cha Mulungu
“Pakati pa athenga amenewa Takweza ena pamwamba pa enawo.”—Al-Baqarah (“sūrah” 2), vesi 253, kuchokera mu Qur’āna
ANTHU okhulupirira mwa wamphamvuzonse, Mulungu wachikondi amazindikira nzeru ya kugonjera ku chifuniro chake. Iwo amayamikira chitsogozo chimene iye wapereka kwa iwo kupyolera mwa athenga ake oikizidwa ndi chidziŵitso chaumulungu. Ena a athenga amenewa amazindikiridwa ndi zoposa pa chimodzi cha zipembedzo zazikulu zadziko. Mwachitsanzo, atsatiri oposa 800 miliyoni a Chisilamu amawona anthu a chiyambi cha Chiyuda ndi Chikristu onga Adamu, Nowa, Abrahamu, Mose, Davide, ndi Yesu kukhala aneneri aakulu a Mulungu. Koma wachisanu ndi chiŵiri, iwo amakhulupirira kuti, wakwezedwa pamwamba pa athenga ena onse—mneneri Muḥammad.
Dzina lakuti Chisilamu liri latanthauzo, popeza kuti limazindikiritsa chigonjero kapena kudzipereka—m’mawu ozungulira lemba amenewa, ku lamulo ndi chifuniro cha Allah. Munthu woyenda njira imeneyi ya chigonjero ndi kudzipereka amatchedwa “Msilamu,” liwu lolongosola kachitidwe la liwu la islam. Uyo kwa amene Asilamu ayenera kugonjerako ali Allah. Lowonedwa kukhala dzina laumwini, Allah liri kufupikitsidwa kwa Al-Ilah, mawu Achiarabu otanthauza “Mulungu Wamphamvuyonse.” Dzinalo limawonekera mu Qur’ān nthaŵi 2,700.
Mneneri Wofunika Koposa wa Chisilamu
Muḥammad bin Abdullah (mwana wa Abdullah), muyambitsi wa Chisilamu, anabadwira mu Mecca, Saudi Arabia, chifupifupi chaka cha 570 C.E. Iye anali wosakhutiritsidwa ndi kukhulupirira m’milungu yambiri kwa kumaloko ndi miyambo. Iye mwachiwonekere sanadzimve wotengeka ku Chiyuda kapena Chikristu. H. M. Baagil, mkonzi wa Chisilmu, akufotokoza kuti: “Chifukwa chakuti Chikristu chinali chitapatuka motalikira kuchoka ku ziphunzitso zoyambirira za Yesu, Allah kenaka anatumiza monga mbali ya kakonzedwe Kake koyambirira Mneneri Wake womalizira, Muhammad, monga m’bwezeretsi kudzabwezeretsa masinthidwe onsewa.”
Muḥammad anapatsa miyambo ndi malamulo a mwambo kukometsera kwa Chiarabu. Yerusalemu ndi kachisi wake zinaloŵedwa m’malo ndi Mecca ndi kachisi wake wachisilamu wopatulika, Kaaba. Loŵeruka kaamba ka Ayuda ndi Sande kaamba ka Akristu zinaloŵedwa m’malo ndi Lachisanu monga tsiku la pemphero la mayanjano. Ndipo m’malo mwa kaya Mose kapena Yesu, Muḥammad tsopano anadzawonedwa ndi Asilamu kukhala monga mneneri wofunika koposa wa Mulungu.
Pamene anali pa msinkhu wa chifupifupi 40, Muḥammad analengeza kuti iye anaitanidwa kukhala mthenga wa Mulungu. Poyambirira iye anagawana zikhulupiriro zake ndi achibale ndi mabwenzi, mwapang’onopang’ono akumapanga gulu la atsatiri. Chiyambi chenicheni cha nyengo ya Chisilamu chinali mu 622 C.E., pamene iye anasamuka kuchokera ku Mecca kupita ku Medina, chochitika chotchedwa hijrah, m’Chiarabu lotanthauza “kusamuka.” Chotero, madeti Achisilamu akuperekedwa kukhala A. H. (Anno Hegirae, chaka chosamuka).
Muḥammad anayesera kugwirizanitsa Ayuda mu Medina ku chipembedzo chake chatsopano ndi ku ntchito yake monga mneneri. Koma kukopako kunalephera. Iwo anamutsutsa iye ndi kupanga chiwembu ndi adani ake ponse paŵiri mu Mecca ndi mu Medina. M’kupita kwa nthaŵi magulu aakulu a Ayuda anapitikitsidwa, ndipo fuko limodzi, Qurayẓah, linawonongedwa mwa kupha amuna ake ndi kuika mu ukapolo akazi ndi ana.
Potsirizira pake, Mecca inalandidwa mwamtendere mu 8 A.H. (630 C.E.), monganso momwe inachitidwira mbali yaikulu ya Arabian Peninsula. Zaka makumi angapo pambuyo pa imfa ya Muḥammad, kukangana pa yemwe adzaloŵa m’malo kunatsogolera ku kukanthana wamba kotero kuti, monga chotulukapo, chitaganya cha anthu chinatenga kaimidwe ka maganizo chifupifupi koyanja kulinga ku magulu ndi malingaliro osakhala Achisilamu.
Choposa Kokha Chipembedzo
Chisilamu chiri njira ya moyo kotheratu, chomakuta Boma, malamulo ake, malamulo ake a mayanjano, ndi mwambo wake, ndipo chotero sichiri kokha chipembedzo. Ichi chimalongosola chifukwa chimene bukhu lakuti Early Islam limanena kuti kwa zaka zoposa 600, “Chisilamu chinali chipembedzo chopereka chitokoso koposa cha dziko, mphamvu yake ya ndale zadziko yolimba koposa ndi mwambo wake wofunika koposa.”
Ndithudi, mkati mwa kokha zaka zana limodzi pambuyo pa imfa ya Muḥammad, ulamuliro wa Chiarabu, wokulira kuposa Ulamuliro wa Chiroma pachimake chake, unatambasuka kuchokera ku India modutsa North Africa mpaka ku Spain, ukumathandizira kutumiza zopanga zatsopano zimene zinalemeretsa kutsungula kwa Kumadzulo. Iwo unapanga zopereka zowonekera m’ntchito za lamulo, masamu, ukatswiri wa za m’mlengalenga, mbiri yakale, kulemba mabukhu, maphunziro a dziko ndi zokhalamo, nthanthi, luso la zomangamanga, mankhwala, nyimbo, ndi masayansi a mayanjano.
Monga Nyenyezi Yodutsa ndi Kuzimiririka
“Zigonjetso za Arabu zinali chotulukapo chachindunji cha kulalikira kwa Muhammad,” ikutero The Collins Atlas of World History. Mosakaikira, zochititsa zina zinathandiziranso ku kufutukuka kwa Chisilamu. Mwachitsanzo, kukangana kwa chipembedzo pakati pa Akristu a ku Byzantium ndi Azoroastrian a ku Persia kunawachititsa khungu onse aŵiriwo kusawona kufikira kwa Arabu.
Kukalamira kugwirizanitsa ulamuliro wofika patali mogwiritsira ntchito chipembedzo sikunali kwachilendo. Koma “Asilamu anakhutiritsidwa kuti iwo anali ndi mawu a chowonadi omalizira osatsutsika mu Koran,” akulongosola tero mkonzi Desmond Stewart. Iwo anakhala ochepekera nzeru, “akumakhulupirira kuti zonse zofunikira kudziŵidwa zinadziŵidwa kale, ndi kuti malingaliro a osakhala Asilamu anali opanda pake.” Kusintha “kunatsutsidwa mowuma khosi.”
Monga chotulukapo, podzafika mu zana la 11, ulamulirowo unali kale m’njira ya kugwa. Stewart akufanizira iwo ndi “nyenyezi yodutsa mwaliŵiro kupyola mlengalenga usiku [imene] . . . mphamvu yake mwamsanga imazimiririka yokha.” Chotero, chipembedzo chimenechi, chomwe chinapanga lingaliro la ubale ndi kupereka njira yopepuka moyerekeza ya kufikira kwaumwini kwa Mulungu, m’chenicheni chinathandizira kugwetsa ulamuliro weniweniwo womwe pa nthaŵi ina chinathandizira kupanga. Monga liŵiro la kukula kwake, kunalinso tero kugwa kwake kwadzidzidzi. Ulamulirowo unatha, koma chipembedzo chake chinakhalabe.b
Chigonjero chowona chimaphatikizapo kumvera Mulungu, malamulo ake, ndi oimira ake. Muḥammad anapambana m’kugwirizanitsa mafuko a Chiarabu mu Arabia, ndi kupeza chitaganya cha Chisilamu (Ummah) chozikidwa pa iye ndi Qur’ān. Linali boma la chipembedzo m’limene chigonjero chinathandiza m’kuwapanga iwo kukhala abale pansi pa mtsogoleri mmodzi. Chisilamu chinalola kugwiritsira lupanga m’kumenyana ndi adani a mafuko a Chiarabu. Lupanga limeneli linathandiza kufutukula ulamuliro wawo ndi chipembedzo chawo. Pamene Muḥammad anamwalira, kukangana kwachiwawa kunabuka. Uku poyamba kunali kwa ndale zadziko, kochokera ku kukangana kwa kusankha Khalifah, mtsogoleri. Chinafulumiza ambiri kutenga malupanga awo kukamenyana ndi abale awo. Kukangana kwa chipembedzo ndi boma kunatumikira kugawanitsa chitaganya. “Chigonjero” sichinakhoze kugwirizanitsa anthu pansi pa mtsogoleri mmodzi.
Mwambo umanena kuti Muḥammad iyemwini anawoneratu mipatuko yotsutsa 72 ya Chisilamu ikuyambika. Koma lerolino maulamuliro ena amalankhula za mazana angapo.
Kugawikana kuŵiri kwakukulu kuli Shia ndi Sunni. Kulikonse, ngakhale kuli tero, kuli ndi kugawanikana kwambirimbiri. Pa Asilamu 100 aliwonse, chifupifupi 83 ali Asunni ndipo chifupifupi 15 Ashiite. Ena ake ali a magulu a mpatuko osiyanasiyana olekanitsidwa monga Adruze, Asilamu Akuda, ndi a Abangan a ku Indonesia, omwe amasakaniza Chisilamu ndi Chibuda, Chihindu, ndi zipembedzo za kumaloko.
Chodziŵika kwambiri ndi Ashiite ochepera chiri kukhulupirira kwawo kuti chipembedzo ndi Qur’ān ziri ndi matanthauzo amseri, kapena obisika. Koma chinali pa kukangana kwa yemwe adzakhala m’loŵa m’malo pamene kupatukana kwa Chishiite m’chenicheni kunabuka. Ashiite (liwu lotanthauza “atsatiri olimba,” m’kulozera ku “atsatiri olimba a ‛Alī”) amasungirira chiphunzitso chotchedwa legitimism (kumamatira m’maprinsipulo a lamulo), akumadzinenera kuti kuyenera kwa kulamulira kuli kokha kolekezera kwa ‛Alī, msuwani wa Muḥammad ndi mpongozi, ndi wa mbadwa za ‛Alī.
‛Alī ndi mbadwa zake anali aimam, atsogoleri okhala ndi ulamuliro wauzimu wotheratu. Pali kusavomerezana pa unyinji wa aimam omwe akhalapo kumeneko, koma gulu lalikulu koposa la Shiite, lotchedwa Twelver Shia, limakhulupirira kuti akhalapo 12. Mu 878 C.E. imam wa chi 12 “anabisika,” uko ndiko kuti, iye anazimiririka pambuyo pa kulonjeza kuti akabwerera pa kutha kwa dziko kudzakhazikitsa boma la Chisilamu lachilungamo.
Asilamu Achishiite chaka ndi chaka amakumbukira kuphedwera chikhulupiriro kwa Ḥusayn, mdzukulu wa Muḥammad. Mkonzi Rahman akuchitira ndemanga kuti: “Wophunzitsidwa kuchokera ku ubwana ndi kuimiridwa kwa kukhazikitsa chochitikachi, Msilamu wa Shī‘ī mwachidziŵikire adzakulitsa lingaliro lozama la tsoka ndi chisalungamo chotulukapo m’kupambana kwa kuphedwera chikhulupiriroko.”
Maumboni a Kusagwirizana?
“Kubweretsedwa kwa nthanthi ya Chigriki ndi nzeru m’zana la chisanu ndi chinayi,” ikuchitira ndemanga The Columbia History of the World, “kunayambitsa nthanthi yosiyanako ya Chisilamu (falsafa) yomwe inali ndi chisonkhezero chofika patali pa kawonekedwe kosankha ndi maphunziro a zaumulungu a Chisilamu. . . . Ndi kupita kwa nthaŵi Chisilamu chenichenicho, monga chipembedzo ndi njira ya moyo, chinapita m’masinthidwe aakulu oyambukira chigwirizano chake.”
Mwachitsanzo, Sufism, liwu la Kumadzulo kaamba ka chinsinsi cha Chisilamu, inafalikira m’mazana a chisanu ndi chitatu ndi chisanu ndi chinayi ndipo inakula mofulumira kukhala gulu lalikulu la chipembedzo. Podzafika zana la 12, malamulo a Sufi, kapena ubale, anafalikira. Nyumba ya achipembedzo mwalumbiro ya Sufi inayamba kuphimba msikiti m’kutchuka. Machitachita opezeka mu Chisufi amaphatikizapo kumwerekera kopambanitsa kwa maganizo kochititsidwa ndi machenjera a kusumika maganizo kapena kuvina kwachilendo, kuchita matsenga, chikhulupiriro mu zozizwitsa, ndi kulambira oyera.
Asufi anavomerezana ndi miyambo ndi zikhulupiriro za kumaloko. Anthu a ku Turk anasungilira machitachita awo a kuwombeza, anthu a mu Africa ng’anga zawo, Amwenye anasungirira oyera awo ndi milungu ya Chihindu ndi nthaŵi ya Chihindu chisadakhale, ndipo a ku Indonesia—monga mmene The New Encyclopœdia Britannica ikuchilongosolera icho—“kawonedwe [kawo] ka dziko la Islām isadakhale kamakhala komvana ndi machitachita a Islām.”
Kukula kwa mpatuko kodziŵika kwa nthaŵi za posachedwapa kwambiri kuli chipembedzo cha Baha’i chomwe chinachokera ku Chisilamu cha Chishiite mu Iran wa pakati pa zana la 19. Kwina kuli mpatuko wa Sunni wotchedwa Aḥmadīyah, womwe unayambika kothera kwa India wa zana la 19, pamene Mirza Ghulam Ahmad, mneneri wodzilengeza yekha, anadzinenera kukhala kuwonekera kwa Muḥammad, Yesu wobweranso, ndi kusinthasintha kwa Hindu Krishna. Iye anaphunzitsa kuti Yesu, pambuyo pothaŵa imfa ku Golgota, anathaŵira ku India, kumene anakhalabe wokangalika kufikira imfa yake pa zaka 120.
Mu ndemanga zake pa Qur’ān, mkonzi wa Chisilamu S. Abul, A‛la Maududi akunena kuti: “Pa nthaŵi ya chivumbulutso cha Al-Baqarah [sūrah yogwidwa mawu pa mutu wa nkhani ino], mitundu yonse yachinyengo inayamba kuwonekera.” Iyi imaphatikizapo “‘Asilamu,’ a munāfiqīn (achinyengo) omwe anali okhutiritsidwa m’nzeru za maphunziro ponena za chowonadi cha Chisilamu koma sanakhale ndi chilimbikitso chokwanira cha makhalidwe kuleka miyambo yawo yakale.”
Chotero kuchokera pa chiyambi penipeni, atsatiri ambiri mwachiwonekere analephera kudzigonjetsera kwa Allah m’njira imene Muḥammad anafunira. Koma ena anatero. Kuchotsapo chitokoso chomwe iwo anachipereka, Chikristu cha Dziko sichinali pamwamba pa “Kutembenukira ku Lupanga” monga momwe chidzalongosoledwera m’kope lathu lino.
[Mawu a M’munsi]
a “Qur’ān” (limene limatanthauza “kubwerezanso”) kali kalembedwe koyanjidwa ndi alembi Achisilamu ndipo komwe tidzagwiritsira ntchito pano m’malo mwa kalembedwe ka Kumadzulo ka “Koran.”
b Kawonedwe kofala kakuti Chisilamu chiri kwenikweni chipembedzo cha Chiarabu kali kolakwika. Unyinji wa Asilamu amakono sali Aarabu. Indonesia, dziko lokhala ndi Asilamu ochuluka koposa, liri ndi omamatira ku chipembedzocho 150 miliyoni.
[Bokosi patsamba 12]
Kukuthandizani Inu Kumvetsetsa Bwinopo Chisilamu
Mizati Isanu Yachisilamu imafuna kuti Asilamu mosachepera pa kamodzi apange mwapoyera kulapa kwa chikhulupiriro chodziŵika kukhala Shahādah—“Palibe mulungu koma Mulungu; Muḥammad ali mneneri wa Mulungu”; kunena mapemphero kasanu pa tsiku; kupereka zakat, msonkho wa lamulo, tsopano wosonkhetsedwa kaŵirikaŵiri pa maziko odzifunira; kusala kudya kuchokera pa kutuluka kwa dzuŵa mpaka kuloŵa kwa dzuŵa mkati mwa mwezi wachisanu ndi chinayi, Ramadan; ndipo mosachepera pa kamodzi, ngati ali okhoza m’zandalama, kutenga hajj (ulendo wachipembedzo) kupita ku Mecca.
“Jihad” (“nkhondo yoyera” kapena “kulimbana koyera”) ikuwonedwa kukhala mzati wachisanu ndi chimodzi ndi mpatuko wa Khariji koma osati ndi Asilamu mwachisawawa. Cholinga chake, ikutero The New Encyclopædia Britannica, “sichiri kutembenuzira anthu ku Islām koma m’malomwake kupeza ulamuliro wa ndale zadziko pa zochitika zonse chapamodzi za zitaganya kuzilamulira izo mogwirizana ndi maprinsipulo a Islām.” Qur’ān imalola “nkhondo yoyera” yoteroyo, ikumati: “Usaphe munthu aliyense yemwe Allah wakuletsa iwe kumupha, kusiyapo kaamba ka chifukwa cha chilungamo.”—Sūrah 17:33.
Magwero aakulu a chiphunzitso cha Chisilamu ndi lamulo ali Qur’ān, yolembedwa pa utali wa nyengo ya chifupifupi kota ya zana; sunnah (miyambo); ijmāʽ (chivomerezo cha chitaganya cha anthu); ndi qiyās (lingaliro la mmodzi ndi mmodzi). Ndandanda ya malamulo Achisilamu, Sharī‘ah, yochita ndi chiwonkhetso cha moyo wachipembedzo, wandale zadziko, wamayanjano, wazapanyumba, ndi wamseri wa Asilamu, inakonzedwa mwa dongosolo mkati mwa mazana a chisanu ndi chitatu ndi chisanu ndi chinayi C.E.
Mecca, Medina, ndi Yerusalemu, m’dongosolo limenelo, ali malo atatu opatulika koposa a Chisilamu: Mecca chifukwa cha malo opatulika ake otchedwa Kaaba, amene mwambo umanena kuti Abrahamu ndiye anawamanga; Medina, kumene msikiti wa Muḥammad unakhazikitsidwa; ndi Yerusalemu chifukwa kuchokera kumeneko, mwambo umanena kuti Muḥammad anakwera kuloŵa kumwamba.
[Mapu/Zithunzi patsamba 13]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Ulamuliro wa Chisilamu monga mmene unawonedwera pa kupambana kwake