Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/99 tsamba 8
  • Kodi Mukanena Chiyani kwa Msilamu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukanena Chiyani kwa Msilamu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Gawo 14:622 C.E. kupita mtsogolo—Kugonjera ku Chifuniro cha Mulungu
    Galamukani!—1989
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 11/99 tsamba 8

Kodi Mukanena Chiyani kwa Msilamu?

1 Kodi munayamba mwalalikirapo Msilamu? Ngati ndi choncho, ndiye kuti munaona kuti Asilamu amakhulupirira kwambiri Mulungu. Komabe, amadziŵa zochepa za Paradaiso wa padziko lapansi amene akudzayo monga momwe aneneri a Yehova ananeneratu, ndipo tikufuna kuwauza za chiyembekezo chimenechi. (1 Tim. 2:3, 4) Chidziŵitso chotsatirachi chikuthandizani kupereka umboni wogwira mtima.

2 Asilamu amakhulupirira Allah, kapena Mulungu, ndipo amakhulupirira kuti Muḥammad ndi mneneri wa Mulungu. Buku lawo lopatulika ndilo Koran, ndipo chipembedzo chawo chimatchedwa Chisilamu, kutanthauza kuti “kugonjera.” Koran imafotokoza kuti bodza ndi kulambira mafano n’zoipa, kuti Mulungu ndi mmodzi, komanso sali mbali ya Utatu. Ndiponso, imaphunzitsa za kusafa kwa moyo, moto wa helo, ndi paradaiso wakumwamba. Asilamu amaona Baibulo monga Mawu a Mulungu koma amakhulupirira kuti linasinthidwa, pamene Koran, imene idakali m’chinenero chake choyambirira, sinaipitsidwe.

3 Khalani Waubwenzi, Waluso, ndi Wozindikira: Pamene mukulankhula ndi Msilamu, khalani waubwenzi ndi wochenjera. (Miy. 25:15) Kumbukirani kuti zikhulupiriro za Asilamu n’zokhomerezeka kwambiri m’maganizo mwawo ndi kuti zambiri za izo anaziphunzira mongoloŵeza. Choncho, kukambirana ziphunzitso zachipembedzo ndi kuti azitsimikizira okha chimene chili chifuno cha Mulungu, si zimene zimachitika pa kukula kwawo kwauzimu. (Aroma 12:2) Kuti tithandize Asilamu, n’kofunika kuleza mtima ndi kuwamvetsetsa.—1 Akor. 9:19-23.

4 Peŵani kugwiritsa ntchito mawu amene angachititse munthu wachisilamu kuganiza kuti ndinu wa m’chipembedzo chachikristu wamba. Muuzeni momveka kuti simuli m’chipembedzo cha Chikatolika kapena Chipolotesitanti, muli osiyana nawo. Tchulani Baibulo kuti Buku la Mulungu. Popeza Asilamu sakonda mawu akuti “Mwana wa Mulungu,” nthaŵi zambiri ndi bwino kusagwiritsa ntchito mawuŵa ngakhalenso kukambirana nkhani imeneyi mpaka pamene munthuyo wapita patsogolo mwauzimu. Komabe, mutha kukamba za Yesu, momutchula monga mneneri kapena mthenga. Peŵani kukangana. Ngati muona kuti pakubuka zaukali, mwaulemu chokanipo msanga.

5 Ndi bwino kukambirana ndi munthu m’modzi osati gulu. Kaŵirikaŵiri, ndi kwanzeru akazi kukambirana ndi akazi anzawo, ndipo amuna ndi amunanso. Mwachionekere, pali nthaŵi zina pamene zimenezi sizingagwire ntchito, koma muyenera kuganiza bwino. Komanso, Asilamu ambiri amalingalira mofulumira zimene amati sikuvala kapena kudzikongoletsa kwabwino kwa akazi. Alongo ayenera kuzindikira zimenezi.—1 Akor. 10:31-33.

6 Zinthu Zoyenera Kukambirana: Lankhulani zoonadi za ukulu wa Mulungu ndi chikondi chake. Musakayikire kutchula kuti ndinu wokhulupirira woona, kuti Mulungu ndi mmodzi (osati Utatu), ndiponso kuti kulambira mafano n’kolakwika. Lankhulani za kuipa kumene kulipo m’dziko lerolino—nkhondo, zipolowe, udani waufuko, ndi chinyengo chimene chili chofala mwa anthu ambiri achipembedzo.

7 Bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? lidzakupatsani nzeru zina zowonjezereka za mitu imene ingagwiritsidwe ntchito poyamba kukambirana ndi Asilamu. Linapangidwa kuti likope Asilamu okhala kumalo kumene ali aufulu kuphunzira Baibulo.

8 Paulaliki, munganene kuti:

◼ “Ndikufunafuna kulankhula ndi Asilamu. Ndakhala ndikuŵerenga za chipembedzo chanu ndipo ndikhulupirira kuti sindinganame nditanena kuti Asilamu amakhulupirira Mulungu mmodzi woona ndi aneneri onse. [Yembekezani yankho.] Ndikufuna kulankhula nanu za ulosi wakale wonena za kusandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso. Kodi ndingakuŵerengereni zimene mneneriyo analemba? [Ŵerengani Yesaya 11:6-9.] Ulosi umenewu umandipangitsa kuganiza za chimene chili chifuno cha Mulungu padzikoli. Chikutchulidwa m’bulosha ili.” Tsegulani bulosha la Mulungu Amafunanji phunziro 5, ndiyeno ŵerengani ndime 1 ndi 7. Ngati asonyeza chidwi, pitirizani kukambirana naye ndime zotsala paphunzirolo. Msiyireni buloshalo, ndipo panganani za ulendo wobwereza.

9 Popempha Msilamu kuphunzira naye bulosha la Mulungu Amafunanji, ndi bwino kunena kuti kukambirana, osati phunziro la Baibulo. Mutamaliza buloshali, wophunzira ayenera kukhala wokonzeka kuphunzira buku la Chidziŵitso.

10 Ndi chidziŵitso cha zikhulupiriro ndi malingaliro a Asilamu chimenechi, tingasankhe mabuku amene tingagaŵire Asilamu ndi njira imene tingachitire umboni kwa iwo mozindikira. Yehova apitirizetu kudalitsa zoyesayesa zathu pothandiza anthu a mitundu yonse kuitanira pa dzina lake ndi kupeza chipulumutso.—Mac. 2:21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena