Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 8/8 tsamba 8-10
  • Kodi Ndi Makhalidwe Otani Amene Amalamulira Moyo Wanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndi Makhalidwe Otani Amene Amalamulira Moyo Wanu?
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupangitsa Cholakwika Kuwoneka Chabwino
  • Magwero a Makhalidwe Abwino
    Galamukani!—1992
  • Pindulani Polimbikira Kuchita Zinthu Zauzimu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Mapindu a Makhalidwe Abwino Amene Amabweretsa Chimwemwe
    Galamukani!—1990
  • Makhalidwe Abwino Angakuthandizeni Kuti Muzisangalala
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 8/8 tsamba 8-10

Kodi Ndi Makhalidwe Otani Amene Amalamulira Moyo Wanu?

MUSANAYANKHE funso limenelo, mungafune kulingalira iri: Kodi nchiyani chomwe mumafuna m’moyo? Chuma, kutchuka, chisangalalo, zochitika zosangulutsa, kukhutiritsidwa kwa za kugonana? Kapena mwinamwake chonulirapo chanu chiri kutchuka kaamba ka kuwona mtima, kukoma mtima, chifundo, utumiki wapoyera, uzimu? Chirichonse chomwe icho chiri, lamulo la Baibulo iri likhalabe lowona: ‘Chirichonse chomwe muchifesa, chimenecho ndicho mudzatuta.’—Agalatiya 6:7.

Ngati mutaya makhalidwe owona, muyenera kukhala ofunitsitsa kukhala ndi zotulukapo zake. Woweruza wa Khoti Lalikulu Paul R. Huot akutchula zina za izo. Akumatchula kupatuka kuchoka pa kulemekeza lamulo, makhalidwe a mayanjano, ndi kudzilanga, iye anati: “Zinthu sizirinso kokha zabwino ndi zoipa. Chirichonse chiri chokaikiritsa. Tataya mayendedwe abwino. Tataya ulemu. Tataya ubwino. Kokha anthu oŵerengeka amazindikira kusiyana pakati pa chabwino ndi cholakwika. Chimo tsopano likugwidwa, osati kulakwira lamulo.”

Pamene chidziŵitso chikukula ndi mphamvu kuwonjezeka, pali kufunikira kokulira kaamba ka makhalidwe abwino kulamulira kugwiritsiridwa ntchito kwawo. (Miyambo 24:5) Mwatsoka, kuwonjezereka kwa chidziŵitso ndi mphamvu kwatsagana ndi kunyonyotsoka m’makhalidwe abwino. Katswiri wa mbiri yakale Arnold Toynbee akuchitira ndemanga pa ichi: “Chiri changozi kuganiza kuti takhala achipambano koposa m’munda wa zopangapanga, pamene kuli kwakuti mbiri yathu ya kulephera kwa mkhalidwe wabwino iri chifupifupi yosayerekezeka. . . . Ngati mpata wa makhalidwe upitirizabe kukula, ndikuwoneratu nthaŵi pamene nzika zochepera zingayambe kumayenda ndi mabomba amthumba a atomic.”

Chikhoterero cha nthaŵi ino chiri cha kutsitsa makhalidwe owona ndi kupereka uchimo ku malo otairako zinyalala. Mkhalidwe uli wofanana ndi uja wa mkazi wachigololo wa pa Miyambo 30:20: “Chomwecho njira ya mkazi wachigololo; adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachita zoipa.” Koma chimo lidakali ndi ife, kukhala munthu wabwino, kumangogwira ntchito kokha pansi pa mawu achiphamaso chotero monga kumasuka, ufulu, nthanthi yokhulupirira kuti nzeru imadalira pa okhala nayo, kuwongoleredwa kwa makhalidwe, kusapereka chiweruzo—zonse kuikidwa pamodzi kukhala “makhalidwe atsopano.”

Kupangitsa Cholakwika Kuwoneka Chabwino

Palibe chimene chasintha kwenikweni chiyambire nthaŵi ya Yesaya. Mawu ake adakali chandamale: “Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m’malo mwa kuyera, ndi kuyera m’malo mwa mdima; amene aika zowawa m’malo mwa zotsekemera; ndi zotsekemera m’malo mwa zowawa!” (Yesaya 5:20) Kupangitsa zolakwika kuwoneka zabwino, iwo amasintha zizindikiro pa thermometer (chiwiya chopimira kutentha kwa thupi) kupangitsa malungo kuwoneka achibadwa.

Kodi ndi makhalidwe ati omwe amapereka zotulukapo zabwino? Ndi ati omwe amakupangitsani kukhala wachimwemwe, kutulutsa mabwenzi okhulupirika, kupangitsa mtendere wa mkatikati ndi chikhutiritso? Kodi mumafuna kutchuka kaamba ka kuwona mtima, kunena zowona, kudera nthaŵa kaamba ka ena? Kukhala wofunika, wolemekezedwa, wokondedwa? Kapena kodi mumakuwona kwaphindu mowonjezereka kukhala ndi zinthu zopanda polekezera, kulawa mphamvu ya chuma chambiri? Kodi kukhutiritsidwa kwa zikhumbo zakuthupi kuli ndi mbali yokulira? Kodi chiri chofunika kaamba ka inu kusumika pa kukwaniritsa zinthu kwaumwini?

Kugonana kosakhala kwa lamulo kuli kofalikira, kusangalala ndi chivomerezo chochokera pa kuwulutsa kwa pa wailesi ndi chitaganya mwachisawawa. Koma nchovulaza chotani nanga ku ukwati ndi banja ndi moyo wabwino wa ana! Zotulukamo m’kugonana kololedwa kumeneku ziri kupambanitsa kwakukulu kwa zilakolako zosakhala za chibadwa za kugonana kwa ofanana ziŵalo kofalikira chotero lerolino ndipo kumene kwalekereredwa ndipo ngakhale kuvomerezedwa ndi zipembedzo zina zazikulu za Chikristu cha Dziko. Mogwirizana ndi kachitidwe koteroko, Mawu a Mulungu akufunsa ndi kuyankha kuti: “Kodi iwo ali amanyazi ndi kachitidwe kawo konyansa? Ayi, iwo alibe manyazi nkomwe; sakunyazitsidwa nkonse.”—Yeremiya 6:15, New International Version.

Yesu anagogomezera kufunika kwauzimu, akumanena kuti: “Odala ali osauka mumzimu, chifukwa uli wawo ufumu wa kumwamba.” (Mateyu 5:3) Koma ambiri akukaniza chosoŵa chimenechi monga cha phindu lochepera ndipo sakuchita chirichonse kuchikwaniritsa icho; komabe miyoyo imene imachikana icho imathera m’kukhala yopanda pake. Ngakhale ndi zokwaniritsidwa zambiri za kudziko, miyoyo yoteroyo iri chikhalirebe yopanda pake ndipo yosoŵa chimwemwe chenicheni ndi chikhutiritso cha mzimu. Ndipo mwachisoni, awo odziŵa za chosoŵacho ndi kumafunafuna kukwaniritsidwa kwake m’matchalitchi a Chikristu cha Dziko abwerako opanda kanthu, popeza kuti mu Chikristu cha Dziko muli, monga mmene mneneri Amosi ananeneratu, “si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva Mawu a Yehova.”—Amosi 8:11.

Kuwonjezerapo, ambiri m’matchalitchi sali m’kakhalidwe kamaganizo kofuna chiphunzitso chabwino chauzimu, koma ‘mogwirizana ndi zikhumbo zawo, amasonkhanitsa aphunzitsi kaamba ka iwo eni kuyabwitsa makutu awo; ndipo amatembenuza makutu awo kuchoka ku chowonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.’ (2 Timoteo 4:3, 4) Ponse paŵiri atsogoleri achipembedzo ndi olambira wamba amadzimva monga mmene anachitira aja a m’tsiku la Yesaya, akumanena kwa awo owona chosowa chauzimu kuti: “Mtima wanu usapenye, ndi kwa aneneri, ‘Musanenere kwa ife zinthu zowona, munene kwa ife zinthu zamyadi; munenere zonyenga. Chokani inu munjira, patukani m’bande, tiletsereni woyera wa Israyeli pamaso pathu.”—Yesaya 30:10, 11.

Makhalidwe aumulungu afunikira kukhala ozama mwa inu. Ngati chigamulo chanu chiri kuwunikira makhalidwe owona ovemerezedwa ndi Mulungu, njira ya kachitidwe kaamba ka inu kuitsatira yandandalitsidwa m’Mawu a Mulungu: “[Vulani] munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo [valani] watsopano, amene ali kukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha iye amene anamlenga iye.”—Akolose 3:9, 10.

Ngakhale kuli tero, inu mungakhale mulibe chidaliro m’Baibulo kukhala Mawu a Mulungu. Mungakhale munafooketsedwa ndi ziphunzitso zoterezo zonga kuzunzidwa kosatha kwa miyoyo yosafa mu helo wa moto, kapena kusuliza kwapamwamba kumene kumakankhira Baibulo pambali kukhala nthano wamba, kapena ndi kachitidwe kosayenera ka chiphamaso, kamachenjera ka chinyengo, ka alaliki olanda ndalama odzinenera monyenga kukhala akuimira ilo.

Kufufuza kwaumwini kudzasonyeza kuti “mphoto ya uchimo ndiyo imfa,” osati kuzunzidwa m’moto; kuti kufukula zofotseredwa kwamakono kwatsimikizira Baibulo kukhala mbiri yakale yolongosoka, osati nthano; kuti ambiri a atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko ali ofanana ndi atsogoleri onyenga a m’nthaŵi za Baibulo, osati aneneri okhulupirika ndi atumwi a masiku aja.—Aroma 6:23; Mateyu, mitu 5-7, 23.

Baibulo liri magwero a makhalidwe owona. Kuwalola iwo kulamulira moyo wanu kudzatanthauza chivomerezo cha Mulungu ndipo kudzatsogolera ku moyo wosatha m’dziko latsopano la chilungamo, kumene “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso [pa mtundu wa anthu]; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chibvumbulutso 21:4; Yohane 17:3.

Chotero lolani kuti makhalidwe owona okwezedwa m’Mawu a Mulungu alamulire moyo wanu, ndipo chotero kupindula inu eni: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”—Yesaya 48:17, 18.

[Chithunzi patsamba 9]

Mtendere monga mtsinje

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena