Magwero a Makhalidwe Owona
LAMULO la makhalidwe abwino liripo m’zitaganya zonse za anthu. Kaya angachikane icho kapena ayi, anthu onse amadzimva kukhala ofunikira magwero achitsogozo apamwamba ndipo opambana iwo. Iwo mwachibadwa amayang’ana ku mphamvu yapamwamba kuilambira kapena kuitumikira. Iyo ingakhale dzuŵa, mwezi, nyenyezi, phiri, mtsinje, nyama, munthu, kapena gulu. Lamulo lawo la makhalidwe lingakhazikitsidwe mu imodzi ya zolembera zopatulika zambiri za miyambo yosiyanasiyana. Chosowacho chimapezeka mwa anthu kulikonse. Icho chiri chachibadwa mwa munthu.
“Chipembedzo,” mogwirizana ndi katswiri wa za maganizo wotchuka C. G. Jung, “chiri mkhalidwe wachibadwa wodabwitsa kwa munthu, ndipo ziwonetsero zake zingatsatiridwe m’mbiri yonse ya anthu.” Wasayansi wodziŵika bwino Fred Hoyle analemba za “lamulo la makhalidwe lopezeka m’zitaganya zonse za anthu” ndipo anawonjezera kuti: “Chikakhala chosavuta kupanga mtsutsano wolingalirika kusonyeza kuti nzeru ya makhalidwe abwino mwa munthu imakhalirirabe mosasamala kanthu za ziyeso zonse [ndi zizunzo] zomwe mokhazikika zimagwira ntchito motsutsana nalo.”
Chodziŵika bwino koposa ndipo chofalitsidwa mokulira koposa cha zolembera zopatulika zonse, Baibulo, limazindikira choloŵa chimenechi cha nzeru ya makhalidwe abwino mwa munthu. Ilo limanena pa Aroma 2:14, 15 kuti: “Pakuti pamene anthu amitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo awonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana.”
Hoyle akulingalira chisinthiko kukhala “lamulo lotseguka kaamba ka mtundu uliwonse wa kachitidwe kamwaŵi,” ndipo akupitiriza kuti: “Mosabisa, ndikuvutitsidwa ndi kukhutiritsidwa kuti nthanthi ya uchigawenga imene lingaliro limene otchedwa ophunzira anaisankha mwa kutsatira chofalitsidwa cha The Origin of Species inapereka mtundu wa anthu ku kachitidwe ka kudziwononga okha kodzichitikira. Makina owononga kenaka anayamba kuŵerenga nthaŵi. . . . Chiŵerengero cha anthu amene lerolino akuzindikira kuti chinachake chikusoweka mokulira ndi chitaganya cha anthu sichiri chaching’ono, koma mwachisoni amataya nyonga zawo m’kutsutsa molimbana ndi chinthu chimodzi chopanda phindu pambuyo pa chinzake.”
Luntha Kumbuyo kwa Chiyambi cha Moyo
Kenaka, ndi kulongosoka kwa masamu, Hoyle akupitiriza kusonyeza kuti kulibiretu kuthekera kwa moyo kukhala unayambika pa dziko lapansi mwamwaŵi. Asayansi a chiorthodox, iye akutero, akhala akuchotsedwako ku lingaliro la magwero olenga ndi “kupambanitsa kwa kumbuyo kochitidwa ndi chipembedzo.” Koma Hoyle amakhulupirira kuti moyo unalengedwa ndi mphamvu yaluntha kutali kumwamba m’mlengalenga. Iye amakhulupirira kuti chimene sichinali chotheka pa dziko lapansi chinali chotheka kutali m’mwamba—koma iye akutsimikizira kuti ngakhale kutali kumeneko mtundu winawake waluntha unali kugwira ntchito. Ngakhale mtundu wopepuka koposa wa moyo, bacterium (kachirombo kosawoneka ndi maso), uli wocholoŵanacholoŵana modabwitsa kotero kuti luntha linafunikira kuloŵetsedwamo m’kulengedwa kwake, koma sangadzibweretse iyemwini kutchula luntha limenelo kukhala Mulungu.
Ena omwe “amalingalira kuti chinachake chikusoŵeka mokulira ndi chitaganya cha anthu” sali ozengereza kuchita tero. Mmodzi wa oterowo ali dokotala wa matenda a maganizo Jung, wogwidwa mawu poyambirirapo: “Munthu amene sali wozikidwa mwa Mulungu sangapereke kutsutsa kulikonse pamaziko a iyemwini ku kuipitsidwa kwakuthupi ndi kwa makhalidwe kwa dziko. Kuti achite chimenechi iye amafunikira umboni wa mkhalidwe wa mkati wopambana, umene iwo wokha ungamtetezere iye kuchokera ku mwinamwake kugonjera kosapeweka kokulira.”
Woweruza wotsogolera Francis T. Murphy wa Appellate Division akunena kuti munthu wamakono “sadziŵa tanthauzo lokwanira la moyo wake ndipo amakaikira kuti moyo uli ndi tanthauzo lirilonse. Mosasamala kanthu ndi mmene kuyerekezera kwake kwa makhalidwe kungakhalire, iye m’chenicheni wachotsa Mulungu m’moyo wake, mu ofesi yake, m’nyumba yake. Iye chotero akusoŵeka maziko a makhalidwe abwino.” Kuchokera ku dziko la zamaseŵera, Howard Cosell ananena lingaliro limodzimodzilo pamene anali kukambitsirana vuto la kugwiritsira ntchito molakwa kwa anam’goneka kochitidwa ndi othamanga. Iye ananena kuti: “Palibenso malo a makhalidwe abwino olongosoleka mu America . . . ndipo limenelo ndilo vuto la mwambo wonse wa anthu.”
“Chiri chosatheka,” akutero wolemba m’danga la nyuzipepala Georgie Anne Geyer kuti, “kukhala ndi chitaganya cha anthu cha makhalidwe kapena mtundu wopanda chikhulupiriro mwa Mulungu, chifukwa chakuti chirichonse mofulumira chimabwera kwa ‘ine,’ ndipo ‘ine’ pa yekha ali wopanda tanthauzo. . . . Pamene ‘ine’ akhala muyeso wa zinthu zonse—m’kupondereza Mulungu, tchalitchi, banja ndi miyambo yolandiridwa ya makhalidwe ndi kachitidwe ka anthu—tiri m’vuto.”
Aleksandr Solzhenitsyn ananena kuti atafunsidwa kutchula m’mawu oŵerengeka chikhoterero chachikulu cha zana la 20, iye akanena kuti: “Anthu aiwala Mulungu.” Iye anapitiriza kuti: “Zana la makumi awiri lonse likukokeredwa mu dziŵe la chiphunzitso chokana Mulungu ndi kudziwononga okha. . . . Zoyesayesa zonse za kupezera njira yotulukira m’tsoka la dziko la lerolino ziri zosaphula kanthu pokhapo titalozanso zikumbumtima zathu, m’kulapa, kwa Mlengi wa onse: popanda ichi, palibe potulukira pomwe padzawunikiridwa, ndipo tidzafunafuna mwachabe.”
Kwa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi, munthu wayesera njira yake, kudzigamulira chomwe chiri chabwino ndi chomwe chiri cholakwika. Tsopano chikhoterero chamakono chiri kuchita chinthu chako chako—palibe chabwino ndi cholakwika. Mbiri yakale yadzala ndi zotulukapo zoipitsitsa za njira zonse ziŵirizo, kutsimikizira kuti sichiri mwa munthu kutsogoza mapazi ake. “Iripo njira yowoneka kukhala yabwino kwa munthu, koma matsiriziro ake ali njira yonkira ku imfa.” (Miyambo 14:12, Revised Standard Version; Yeremiya 10:23) Yehova Mulungu anapanga munthu, amamdziŵa iye mkati ndi kunja, ndipo iye wapereka mapu yonkira ku chimwemwe: “Mawu anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuwunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Mawu Ake, Baibulo, limadziŵikitsa makhalidwe owona kaamba ka dalitso la munthu. Bokosi lotsaganalo limandandalitsa zina za zofunikira kuchita ndi zosafunikira kuchita.
[Bokosi patsamba 7]
Makhalidwe Okhalira Ndi Moyo
▸ Udzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima
▸ wako wonse, maganizo, moyo, ndi nyonga.
▸ Udzikonda mnzako monga iwemwini.
▸ Chitani kwa ena monga momwe mukafunira iwo kuchita kwa inu.
▸ Tsatirani Yesu monga Chitsanzo chanu.
▸ Khululukirani ena monga mmene inu mufunira kukhululukidwa.
▸ Lemekezani atate anu ndi amanu.
▸ Mu ulemu lingalirani ena.
▸ Khalani okhulupirika m’zochita zanu zonse.
▸ Londolani mtendere ndi onse.
▸ Funafunani chifatso, kukoma mtima, kudziletsa.
▸ Musabwezere choipa pa choipa kwa munthu aliyense.
▸ Gonjetsani choipa ndi chabwino.
▸ Musalambire milungu yonyenga.
▸ Musagwadire mafano.
▸ Musaphe.
▸ Musabe.
▸ Musachitire umboni wonama.
▸ Musatchule dzina la Mulungu mwachabe.
▸ Musakhumbe zinthu za mnansi wanu.
▸ Musalole dzuŵa kuloŵa muli chikwiyire.