Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 6/8 tsamba 4-5
  • Malonda a Zida Zankhondo—Mmene Amakuyambukirani

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malonda a Zida Zankhondo—Mmene Amakuyambukirani
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Kuba” Kwakukulu
  • Kumawatengera kuphunzira kuchoka kwa iwo:
  • Kumawatengera ndalama kuchoka kwa iwo:
  • Kumawatengera zakudya ndi zakumwa kuchoka kwa iwo:
  • Kumawatengera umoyo ndi moyo kuchoka kwa iwo:
  • Kodi Mphamvu ya Munthu Ingaletse Iwo?
    Galamukani!—1989
  • Zoyesayesa za Kupulumutsa Ana
    Galamukani!—1994
  • Nchifukwa Ninji Pali Vuto la Mtengo wa Kakhalidwe?
    Galamukani!—1989
  • Kodi Ndani Amene Angabweretse Mtendere Wokhalitsa?
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 6/8 tsamba 4-5

Malonda a Zida Zankhondo—Mmene Amakuyambukirani

“VUTO mu ndalama zowonongedwa m’zotetezera liri kudziŵa utali umene muyenera kupita popanda kuwononga zam’dzikomo zimene mukuyesera kutetezera popanda zosungidwira iko zirizonse.” Pamene prezidenti wakale wa U.S. Eisenhower ananena chimenecho mu 1956, ndalama zankhondo zowonongedwa za dziko lonse m’mitengo yokhazikika zinali zochepera ndi theka la milingo ya nthaŵi ino. Kodi ndimotani mmene kuwonjezeka kwakukulu kumeneku kwa malonda a zida zankhondo kwakuyambukirani? Ripoti la kufufuza, World Military and Social Expenditures, lidzachitira chitsanzo:

1. Pa milingo yamakono ya kuwononga ndalama m’zida zankhondo kwa dziko, munthu wa msinkhu wapakati mmodzi angayembekezere kupereka zaka zitatu kufika ku zinayi za moyo wake akugwira ntchito kulipira kaamba ka iko.

2. Kugula zida kopambanitsa kwapanga mulu waukulu wa ngongole za anthu kaamba ka mibadwo ya mtsogolo.

3. Kunyalanyaza kwa zosoŵa za mayanjano m’kulondola mphamvu zankhondo kwasiya munthu mmodzi mwa 5 akukhala m’kusauka kwakukulu. Chiŵerengero cha dziko lonse chomavutika ndi kusadziŵa kuŵerenga ndi kulemba, umoyo woipa, ndi njala yopanda malire chikukula mosalekeza.

4. Kugogomezera kwa zankhondo pa luso la zopangapanga la pamwamba kumapanga ntchito zochepera kuposa ndi zimene zikapangidwa titayerekeza ndi chiwonkhetso cha ndalama zowonongedwa kaamba ka maphunziro, umoyo, nyumba za mkati mwa mzinda, ndi zosoŵa zina za anthu wamba. Kusalembedwa ntchito kumakwera.

5. Pali msilikali mmodzi pa anthu 43 m’dziko koma kokha sing’anga mmodzi pa anthu 1,030.

6. Zaka za kuchulukira kwa zankhondo zapanga malo ozungulira omwe ali osakhazikika mowonjezereka ndi angozi kwenikweni ku moyo wa anthu kuposa nthaŵi ina iriyonse m’mbiri yakale.

7. Zida za kuwononga kwakukulu, zokonzekera kuwomba mphindi iriyonse, zaika anthu onse mu ukapolo wa mantha.

“Kuba” Kwakukulu

Osauka a dziko ndiwo okhudzidwa kwenikweni ndi malonda a zida zankhondo—m’maiko olemera koposa limodzinso ndi osauka koposa. Dwight D. Eisenhower akuchiika icho m’njira iyi: “Mfuti iriyonse imene yapangidwa, chombo cha nkhondo chirichonse chotumidwa, rocket iriyonse yoponyedwa zimatanthauza m’lingaliro lomalizira kuba kuchokera kwa awo omwe ali ndi njala ndipo sakudyetsedwa, awo omwe ali ausiwa ndipo sakuvekedwa. Dziko m’zida zankhondo silikuwononga ndalama zokha. Ilo likuwononga thukuta la antchito ake, ukatswiri wa asayansi ake, nyumba za ana ake.” Kodi “kuba” kumeneku kumatanthauzanji kwa minkholeyo?

Kumawatengera kuphunzira kuchoka kwa iwo:

▪ Mtengo wa sitima ya m’madzi ya nyukliya yatsopano imodzi umalingana ndi bajeti ya chaka chonse ya maphunziro a maiko 23 otukuka kumene ndi ana amsinkhu wa kusukulu oposa 160 miliyoni.

▪ Bajeti ya U.S. Air Force iri yokulira kuposa chiwonkhetso chonse cha bajeti ya maphunziro kaamba ka ana oposa biliyoni imodzi mu Africa, Latin America, ndi Asia, kusaphatikizapo Japan.

Kumawatengera ndalama kuchoka kwa iwo:

▪ M’zaka za posachedwapa Maiko Otukuka Kumene atenga 75 peresenti ya zogula za zida zankhondo kunja kwa dziko zadziko—kugwiritsira ntchito kosasamala kwa ndalama zakunja komwe kwasiyira ambiri mtolo wa ngongole zakunja zosakhoza kubwezedwa.

▪ Podzafika 1988 ngongole zakunja zoikidwa pamodzi za maiko Otukuka Kumene zinafikira ukulu wa $1.3 triliyoni ($1,300,000,000,000).

▪ Bajeti ya zankhondo ya dziko chaka chirichonse imalingana ndi ndalama zolandiridwa za anthu chifupifupi 2.5 biliyoni m’maiko 44 osauka koposa.

Kumawatengera zakudya ndi zakumwa kuchoka kwa iwo:

▪ Chimatenga ndalama zokwanira $590,000 pa tsiku kugwiritsira ntchito chombo chapamadzi chokhala ndi bwalo la ndege chimodzi, pamene kuli kwakuti tsiku lirilonse mu Africa mokha, ana 14,000 amafa ndi njala kapena zochititsa imfa zina zogwirizanitsidwa ndi njala.

Kumawatengera umoyo ndi moyo kuchoka kwa iwo:

▪ Mphindi iriyonse avereji ya ana 30 amafa ndi matenda ofala kwambiri m’dziko. Awa angachinjirizidwe ndi katemera, miyezo ya kusamalira zonyansa, ndi kudyetsedwa kwabwino ngati zifuno za mayanjano ndi umoyo zinaikidwa kukhala zoyambirira pa mphamvu ya zankhondo.

▪ Programu ya katemera yomwe ikanatetezera ana 750 miliyoni molimbana ndi matenda oyambukira yayerekezedwa kutenga ndalama za zowonongedwa pa masiku aŵiri kaamba ka zida zankhondo za dziko.

▪ M’maiko osauka koposa, avereji ya utali wa moyo iri yaifupi ndi zaka 30 kuposa imene iri m’maiko olemera kwambiri, kochititsidwa m’mbali ina ndi kunyalanyaza zofunika za umoyo chifukwa cholondola zida zankhondo zowonjezereka.

Ndithudi, amalonda a zida zankhondo akunyamula thayo lalikulu kaamba ka mikhalidwe yochititsa chisoni ya dziko. Ndimotani mmene amadzimvera ponena za mikhalidwe imeneyi? “Tiribe vuto la chikumbumtima. Ife tikuthandizira ku kupita patsogolo kwathu,” ikunena tero nduna yachiŵiri yoyang’ana zakunja kwa dziko ya dziko lotsogolera m’kupanga zida zankhondo. Koma munthu wolingalira angafunse kuti, ‘Kodi iko kungaletsedwe?’ Tidzalingalira funso limenelo mu nkhani ziŵiri zotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena