Kodi Nthaŵi Zonse Mumachedwa?
ANYAMATA aŵiri analemba ziitano kaamba ka kukumana kodzachitidwira kunyumba kwawo pa Loŵeruka ndi nthawi ya 2:00 p.m. Pokumbukira kuti mabwenzi awo aŵiri nthaŵi zambiri anali kufika mochedwa, mnyamata mmodzi ananena kuti: “Kodi bwanji tilembepo 1:00 pa ziitano zawo? Mwinamwake adzabwera pa 2:00, pa nthaŵi yakedi.” Ndipo zimenezo ndi zimenedi zinachitika!
Simavuto onse a kusunga nthaŵi amene amathetsedwa mopepuka chotero. M’chenicheni, kulephera kufika pa nthaŵi yake kungakhale ndi zovuta zake kwa wofika mochedwayo limodzinso ndi kwa aliyense wokakamizidwa kuwadikirira. Zowona, simiyambo yonse imene imaika chigogomezero pa kusunga nthaŵi. Komabe mosasamala kanthu za kumene mumakhala, mwachidziŵikire muyenera kudera nkhaŵa ndi kufika pa nthaŵi yake kaamba ka zinthu zonga ngati ulendo wa pandenge, misonkhano, mapangano a malonda, ndipo ngakhale kukumana kwinakwake kwa mayanjano.
Chotero ngati inu nthaŵi zambiri mumachedwa, kodi nchiyani chimene chingakuthandizeni kufika pa nthaŵi yake? Ndipo ngati kaŵirikaŵiri mumafunikira kudikirira ena, kodi nchiyani chimene chingakuthandizeni kuchita ndi chophophonya cha anthu chofala chimenechi mokhutiritsa?
Kodi inu mumazolowera kubwera mochedwa? Choyamba yambani mwayesa kudziŵa chochititsa. Kodi mumakokedwa mopepuka? Kodi muli ndi vuto lalikulu la kudzikonzekeretsa inumwini ndi banja lanu? Zisonkhezero zoterozo kulinga ku kuchedwa zingalakidwe ndi kuyesayesa kodera nkhawa. Mwachitsanzo, dziŵani nthaŵi ya zochita zanu za tsiku ndi tsiku ndipo konzani molinganamo, mukumasiyako nthaŵi yochulukira kaamba ka chirichonse. Fufuzani nthaŵi patapita ola limodzi kapena kupitirirapo. M’malo moyesera kufika pa nthaŵi yeniyeni kaamba ka mapangano ofunika, lunjikani pa kufika kumeneko mofulumira kuposa pamene mukuyembekezeredwa. Komabe, bwanji ngati kuchedwa kwanu kuli vuto lokhalirira?
Zochititsa za Maganizo
Nthaŵi zina pamakhala zolinga zobisika za kuchedwera—zija za kupewa zochitika zosafunika, kudziwonetsera, kupeza chisamaliro, kapena kupeŵa kufunika kwa kudikirira ena.
Dr. Dru Scott akuthira ndemanga pa chochititsa china chamachenjera cha kuchedwa: “Wamalonda amene wakonzeka kuti anyamuke kuchoka pa ofesi kaamba ka kukakumana ndi wogula wofunika koposa abwerera pakhomo kukatumiza ‘kokha foni imodzi.’ Loya amene wanyamuka kale kukakwera ndege amva chifuno cha kuchedwetsa ulendo wake kuti alembe ‘kalata imodzi yokha.’ Iwo amapeza chisonkhezero choipa kuchokera ku kuchedwa kumeneku. Iko mwachibadwa kumapangitsa chifuno cha kufulumira kwa mphindi yomalizira.”
Inde, kusangalatsidwa kwa mphindi yomalizira—ngakhale kuti nkoipa—kungapereke chisonkhezero chofunikira. Ngati mukulingalira kuti mungakhale “womwerekera” ku mtundu umenewu wa chisangalalo, kodi mungaulake motani? Dru Scott akulingalira kuti: “Chisonkhezero ndi chinthu chofunika, chimene tonsefe timafunikira. Kufunafuna icho sikumasonyeza kusoŵeka kwa uchikulire. Anthu aumoyo amazindikira kufunika kwake. Iwo amaphunzira mmene angasamalire icho mopindulitsa.”
M’mawu ena, yang’ananinso pa makonzedwe anu a mlungu ndi mlungu. Kodi mwaphatikizapo machitachita ena otsimikizirika odzutsa chikondwerero kapena chisonkhezero chanu? Kapena kodi ndandanda yanu iri ndandanda ya zinthu zimodzimodzi, zochita za tsiku ndi tsiku za nthaŵi zonse? Palibe aliyense amene ali ndi ulamuliro wotheratu pa zinthu zake, koma ngati mupanga nsonga ya kupereka chisonkhezero pomwe mungathe, mungalekerere mbali ya zinthu za tsiku ndi tsiku ya moyo popanda kukhoterera ku kuchedwa kuti mupeze chisangalalo.
“Koma Ndimachita Bwino Koposa Pansi pa Kudidikizidwa!”
Anthu ena amadzinenera kuti pamene adikirira mpaka mphindi yomalizira, amachita bwino koposa. Ndipo ngati zimenezo nzowonadi kwa inu, ziri bwino. Koma khalani wowona mtima ndi inu eni. Kodi mumachitadi bwino koposa pamene mudikira mpaka mphindi yomalizira?
M’bukhu lake lakuti Working Smart, Michael LeBoeuf analongosola kuti: “Oŵerengeka, ngati alipo konse a ife timachita ntchito yathu yabwino koposa pansi pa chididikizo, mosasamala kanthu za zimene timakhulupirira. . . . Choyamba, ngati mwakakamizidwa kugwira ntchito pa liŵiro lokwera, mumawonjezera kuthekera kwa kupanga zophophonya. . . . Chachiŵiri . . . , chinachake chofunikadi mwamsanga chingabwere ndi kukuberani mphindi zofunika zoŵerengeka zimenezo zoperekedwa ku kuchita ntchitoyo. . . . Chachitatu, mutalingalira kuti zonse zinayenda bwino ndipo munachita zambiri m’mphindi zoŵerengeka, zimangotanthauza kuti mumadziŵa kukhala wokhutiritsa koma mumangosankha kutero kokha pansi pa chididikizo. Mukudzinamiza nokha mwa kulephera kukhala yemwe inu muli.”
Kodi Mumadana Ndi Kudikirira?
Mwinamwake mumasunga nthaŵi koma mobwerezabwereza mumakakamizika kudikirira kaamba ka awo amene safika pa nthaŵi yake. Kodi mungathandize motani kapena kuchita ndi ziŵalo za banja, mabwenzi, kapena oyanjana nawo amene amachedwa mwachizoloŵezi?
Mungakhale wokhoza kuthandiza ochedwa mwachizoloŵezi mwa kuwakumbutsa pasadakhale za pangano lawo kapena kukambitsirana nawo mowona mtima ponena za vutolo. Zingachitike kuti ena ozolowera kuchedwa, chifukwa cha chiyambi chawo kapena zifooko zaumwini, samavomereza ku thandizo ndi kupitirizabe kuvutitsa ena mwa kulephera kufika pa nthaŵi yoyenera. Ngati mkhalidwe wanu umafunikira kuti mukhale kapena kugwira ntchito ndi anthu oterowo, mungalandire kuchedwa kwawo kukhala nsonga ya m’moyo ndi kukulitsa njira zochitira ndi vutolo mokhutiritsa.
Mwachitsanzo, mungayembekezere nthaŵi yodikirira ndi kukonzekera kaamba ka iyo. Mwinamwake mungakonze kukumana pa malo amene kudikirira kukakhala kosangalatsa, monga ngati pa sitolo kapena resitalanti. Kapena mubwere ndi ntchito ina kapena zinthu zoŵerenga kuti zikutanganitseni pamene mukudikirira. Khazikani mapangano anu ndi iwo mofulumira kotero kuti kuchedwa kwawo kolingaliridwa kusakupangitseni kuphonya zonulirapo zanu. M’zochitika zina, kuweruza kwanu kwabwino kungakulangizeni kusaphatikiza ozolowera kuchedwa pa makonzedwe anu.
Fupani Khalidwe Lanu Labwino
Ngati mulidi ndi vuto m’kufika pa nthaŵi yake, musakhululukire chifooko chimenechi kapena mwachisoni kuchilekerera, mukumalingalira kuti ena adzakudikirirani. Uku kungakhale kusalingalira miyoyo ndi kudzimva kwa ena. Lingalirani za mkwatibwi amene anafika maola atatu mochedwa kaamba ka ukwati wake. Monga chotulukapo, phwandolo linafunikira kusamutsidwira ku nyumba ina mofulumira, zikumatulukapo kusokoneza kwakukulu kwa opezekapo 200. Ndithudi, kulingalira ena kuyenera kutifulumiza kusunga nthawi!
Mosakaikira zoyesayesa zanu za kusunga nthawi zidzatulukapo osati kokha m’kukhala kwanu wofika pa nthawi yake komanso wofika msanga kaamba ka mapangano ambiri ndi zochita. Izi zitachitika, dzithokozeni! Dr. Scott akuti: “Nthaŵi yopezeka iri ngati ndalama zopezeka. Musaiike pa bajeti yanu ya tsiku ndi tsiku; ithereni pa chinachake chimene mudzasangalala nacho. Lingalirani za zinthu zonse zimene mungafune kuchita ngati munali ndi mphindi khumi zowonjezereka mmawa mulimonse, kapena theka la ola madzulo, kapena kokha mphindi zoŵerengeka apa ndi apo mkati mwa tsiku. Khalani ndi malingaliro ena okonzekera, kotero kuti mudzipatse inu eni mphatso yosangalatsa nthawi iriyonse mutafika msanga.”
[Bokosi/Zithunzi patsamba 30]
Njira Zolakira Kudikirira Mpaka Mphindi Yomalizira
1. Gawani ntchito zazikulu, zotopetsa kukhala zazing’ono zokhoza kuchitika.
2. Tengani sitepi lotsimikizika kulinga ku kumaliza ntchito. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kumaliza kuŵerenga bukhu, chotsani bukhulo pa shelufu ndi kuliika pafupi ndi mpando wanu wokondeka woŵerengera.
3. Pangani pangano ndi winawake. Uzani bwenzi kapena woyang’anira kuti mudzamaliza ntchito inayake pofika nthaŵi yakutiyakuti.
4. Dzithokozeni pamene mumaliza mbali iriyonse ya ntchito yaikulu.
5. Pamene mudzipeza mukuchedwa, vomerezani kwa inumwini kuti, ‘Ndikutaya nthaŵi yanga.’ Chokumbutsa chimenechi pomalizira pake chingatsogolere kukulamulira ndi kusankha kuleka kuchedwa.
6. Lingalirani mtengo wa kuchedwa: Kodi mtolo wa ntchito udzawonjezeka? Kodi zowononga za chuma zidzawonjezeka? Bwanji ngati mudzadwala pamene mphindi yomaliza yafika? Bwanji ngati ntchitoyo itenga nthaŵi yaitali kuposa imene munalingalira? Kodi pangakhale mpambo wa zosokoneza? Kodi ukoma wa ntchito yanu ya mphindi yomaliza udzayambukiridwa?—Kuchokera mu “How to Get Control of Your Time and Your Life,” lolembedwa ndi Alan Lakein.
[Zithunzi]
Kodi mumachimva chifuno cha ‘kuchita kokha chinthu chimodzi’ musananyamuke kaamba ka pangano?
Kodi mumachitadi bwino koposa pansi pa kudidikizidwa?
Gwiritsirani ntchito nthaŵi yodikirira kupumula kapena kukwaniritsa chinachake chimene mukufuna kuchita