Kugwirira Chigololo—Anachinjirizidwa ndi Zimene Anaŵerenga
KODI nchiyani chimene muyenera kuchita pamene mwayang’anizana ndi wogwirira chigololo? Pali malangizo osagwirizana. Ena anena kuti kukana kumangosonkhezera wowukirayo, chikhalirechobe Baibulo limasonyeza kuti mkazi ayenera kukana. (Deuteronomo 22:23-27) Kodi nchiyani chomwe chiri chilangizo chabwino koposa?
Phunziro latsopano lofalitsidwa m’kope la January la The American Journal of Public Health limalingalira kukana. Nkhaniyo ikuti: “Kufufuza kwa zochitika kumagwirizana kuchirikiza nsonga yomaliza imodzi yofunika kwambiri: kukana kumachepetsa kuthekera kwa kukwaniritsidwa kwa chivulazocho.” Chomwe chinachitika September yatha kwa mkazi wina mu Japani chimachitira fanizo chimenechi. Iye anali atangobwerera mochedwa usiku kunyumba yake, kumene ankakhala yekha. Iye akulongosola kuti:
“Wogwirira chigololo anabwera mnyumba yanga nakhoma chitseko. Chifukwa cha kudabwitsidwa ndi kuchititsidwa mantha, ndinakhwethemuka kotheratu. Mwamunayo anayesera kundikokera m’chipinda chogona, koma ndinagwira mzati ndi kumukaniza iye.
“Panali pa nthaŵiyo pamene ndinakumbukira lemba la mu Deuteronomo mutu 22. Limanena kuti ngati mkazi safuula pamene awukiridwa, chimasonyeza kuti iye akuvomereza kwa mwamunayo ndipo akuchita chimo motsutsana ndi Yehova. Ndiponso, ndinakumbukira zimene ndinaŵerenga m’nkhani ya mu Galamukani! yakuti ‘Kugwiriridwa Chigololo—Ndimotani Mmene Mungadzichinjirizire Inu Eni?’—October 8, 1980, m’Chijapanese; July 8, 1980, m’Chingelezi.
“Chabwino, ndinaganiza kuti: ‘Ndifunikira kufuula ndi kumkaniza iye monga mmene ndingakhozere.’ Chotero ndinafuula kuti: ‘Yehova, ndithandizeni!’ mobwerezabwereza ndipo mosalekeza. Pamene wogwirira chigololoyo anakokera manja anga kulamanja, ndinakokera kulamanzere. Pamene anandikokera kutsogolo, ndinakokera kumbuyo, ndipo pamene anaphimba pakamwa panga kuyesera kundiletsa kulira, ndinamuluma. Pa mlingo uliwonse, ndinkamukanizabe iye.
“Mwa pang’onopang’ono ndinatopa. Chinali chovuta kwa ine kupuma, ndipo ndinaganiza kuti mtima wanga ukaleka, koma ndinapitirizabe kuchita zonse zomwe ndikakhoza kumukaniza iye ndi kupitirizabe kufuula kwa Yehova kundithandiza. Monga chotulukapo, wogwirira chigololoyo analeka, kuyenda mofulumira kupita ku khomo, ndi kutuluka.
“Ndikhulupirira kuti ndinali wokhoza kupeŵa kugwiriridwa chigololo chifukwa cha thandizo la Yehova ndi chifukwa cha kugwiritsira ntchito zimene ndinaŵerenga mu Galamukani! Ngati sindikanaŵerenga nkhaniyo mu Galamukani!, ndiganizira kuti chifukwa cha mantha ndikanangokhala chete ndipo mwachiwonekere kwambiri ndikanachitadi monga mmene mpanduyo ananenera. Zikomo, zikomo kwambiri.”