Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 11/8 tsamba 26-29
  • Gawo 21: 1900 kupita mtsogolo—Zovala Zokhathamira Ndi Mwazi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gawo 21: 1900 kupita mtsogolo—Zovala Zokhathamira Ndi Mwazi
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupereka Nsembe Anthu kwa Mulungu Wonama
  • “Nakhetsa Mwazi Wosachimwa”
  • Liwongo la Mwazi la Chipembedzo
  • Chifukwa Chake Chipembedzo cha Dziko Chidzatha
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Babulo Wamkulu Azengedwa Mlandu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Chimene Matchalitchi Anakhalira Chete
    Galamukani!—1995
  • Kumasuka ku Chipembedzo Chonyenga
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 11/8 tsamba 26-29

Mtsogolo mwa Chipembedzo M’chiyang’aniro cha Nthaŵi Yake ya Kumbuyo

Gawo 21: 1900 kupita mtsogolo—Zovala Zokhathamira Ndi Mwazi

“Palibe maziko otsimikiza okhazikitsidwa pa mwazi.”—Shakespeare, wolemba ndakatulo ndi madrama Wachingelezi (1564-1616)

KODI mukukumbukira ngozi ya ku Jonestown, Guyana, ya zaka 11 zapitazo mwezi uno? Ziŵalo zoposa 900 za gulu lachipembedzo lotchedwa Kachisi wa Anthu zinadzipha m’chiŵerengero chokulira, ambiri a iwo modzifunira, mwa kumwa madzi a chipatso a paizoni.

Modabwa, anthu anafunsa kuti: ‘Kodi icho n’chipembedzo chotani chimene chimapereka nsembe miyoyo ya mamembala ake?’ Chikhalirechobe, mwazi wosachimwa wakhetsedwa m’dzina la chipembedzo kwa zaka chifupifupi 6,000. Komabe, m’zaka za zana lino la 20, mwazi wakhetsedwa kaŵirikaŵiri ndipo m’njira zosiyanasiyana kuposa pa nthaŵi iriyonse m’mbiri. Tangolingalirani kokha mbali yaing’ono ya umboniwo.

Kupereka Nsembe Anthu kwa Mulungu Wonama

Chiyambire 1914, nkhondo za dziko ziŵiri ndi nkhondo zazing’ono zoposa zana limodzi zakhetsa mwazi wambiri. Zaka zana limodzi zapita, mlembi wa ku France, Guy de Maupassant adati “dzira lomwe limabala nkhondo” ndilo mzimu wokonda dziko lanu, womwe adautcha “mtundu wa chipembedzo.” Ndiiko komwe, The Encyclopedia of Religion imati msuwani wake wa mzimu wokonda dziko lanu, utundu, “wakhala mtundu waukulu wa chipembedzo m’dziko lamakono, kutenga malo a makhalidwe abwino a mwambo achipembedzo owonongedwa.” (Kanyenye ngwathu.) Mwa kulephera kuchirikiza kulambira kowona, chipembedzo chonyenga chinapanga mpata wolowapo mzimu wautundu.

Kulibe kwina kulikonse komwe zimenezi zinawoneka bwino lomwe kuposa mu Nazi Germany, imene nzika zake pakuyambika kwa Nkhondo ya Dziko ya II, 94.4 peresenti ya iwo anadzinenera kukhala Akristu. Kuposa ndi malo aliwonse, Germany—kobadwira kwa chiphunzitso Chachiprotesitanti ndipo yotamandidwa ndi Papa Pius X mu 1914 kukhala kwawo kwa “Akatolika abwino koposa m’dziko”—iyenera kukhala inaimirako chabwino koposa chimene Dziko Lachikristu linali nacho monga chopereka.

Modziŵika, Adolf Hitler Wachikatolikayo anapeza chirikizo labwino pakati pa Aprotesitanti kuposa ndi pakati pa Akatolika. Maboma okhalidwa ndi Aprotesitanti ochuluka anampatsa iye 20 peresenti ya mavoti awo m’masankho a mu 1930, pamene maboma Achikatolika anampatsa 14 peresenti yokha. Ndipo chiŵerengero chokulira koposa choyamba cha Chipani cha Nazi mu masankho a dzikolo chinali mu 1932 mu Oldenburg, boma lokhala ndi 75 peresinti ya Aprotesitanti.

Mwachiwonekere, “malo osiidwa ndi makhalidwe a mwambo wachipembedzo owonongedwa” anali aakulu m’chiphunzitso Chachiprotesitanti kuposa m’chiphunzitso Chachikatolika. Nzosadabwitsa kukhala choncho. Nthanthi ya zaumulungu yolekelera ndi kusuliza Baibulo kwa ophunzira zinali kwakukulukulu zotulukapo za akatswiri a zaumulungu Achiprotesitanti olankhula chinenero chotchedwa German.

Chofunika mofananamo chiri chimene pomalizira chinalimbitsa chirikizo la Akatolika lofooka kwa Hitler. Katswiri wa mbiri yakale wa ku Germany Klaus Scholder akulongosola kuti “mwa mwambo Chikatolika cha ku Germany chinali chogwirizana mwapadera ndi Roma.” Powona kuti Chinazi chinali cholimba motsutsana ndi Chikomyunizimu, Vatican sinazengeleze kugwiritsira ntchito chisonkhezero chake kulimbitsa mphamvu ya Hitler. “Zigamulo zazikulu mowonjezerekawonjezereka zinasamukira ku Curia,” akutero Scholder, “ndipo ndiiko nkomwe malo Achikatolika ndi mtsogolo mwake mu Ulamuliro Wachitatu Germany pomalizira zinalingaliridwa kotheratu mu Roma.”

Mbali imene Dziko Lachikristu linachita m’nkhondo za dziko ziŵiri zonse inatsogolera ku kutayikiridwa kokulira kwa kutchuka. Monga mmene Concise Dictionary of the Christian World Mission ikulongosolera kuti: “Osakhala Akristu anawona ndi maso . . . umboni wakuti mitundu yokhala ndi zaka chikwi za chiphunzitso Chachikristu inalephera kulamulira zikhumbo zawo zoipa ndipo inadzetsa tsoka pa dziko lonse chifukwa chofuna kukhutiritsa zikhumbo zawo.”

Ndithudi, nkhondo zosonkhezeredwa ndi chipembedzo siziri zachilendo. Koma mosiyana ndi nthaŵi zakale pamene mitundu ya zipembedzo zosiyana inkachita nkhondo, m’zana lino la 20 mitundu ya chipembedzo chofanana mowonjezerekawonjezereka imakanthana mowopsya. Mulungu wa chiphunzitso cha utundu mowonekeratu wakhala wokhoza kusonkhezera milungu ya chipembedzo. Motero, mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya II, pamene Akatolika ndi Aprotestanti mu Great Britain ndi United States ankapha Akatolika ndi Aprotesitanti mu Italy ndi Germany, Abuda mu Japan ankachita chimodzimodzi kwa abale awo Achibuda kum’mwera cha kum’mawa kwa Asia.

Mosasamala kanthu za zimenezo, polingalira zovala zake zoipitsidwa ndi mwazi, Dziko Lachikristu silingatsanulire liwongo lake pa ena modzilungamitsa. Mwa kutamanda, kuchirikiza, ndipo nthaŵi zina kusankha maboma a anthu opanda ungwiro, odzinenera kukhala Akristu ndi osakhala Akristu mofananamo ayenera kugawana mlandu wa mwazi wokhetsedwa ndi maboma amenewa.

Komabe kodi n’chipembedzo chanji chomwe chikaika boma pamwamba pa Mulungu ndi kupereka ziŵalo zake monga nsembe zandale zadziko pa guwa la mulungu wa nkhondo?

“Nakhetsa Mwazi Wosachimwa”

Mawuwo, onena za Israyeli wopanduka zaka mazana apitawo, akugwira ntchito kwa zipembedzo zonse zonyenga ndipo makamaka kwa aja a Dziko Lachikristu. (Salmo 106:38) Musaiŵale mamiliyoni a miyoyo yophedwa m’Chipululutso, tsoka m’limene matchalitchi a Dziko Lachikristu anali aliwongo.—Onani Galamukani! April 8, 1989.

Atsogoleri achipembedzo a ku Germany nawonso anakhala chete pa nkhani ina, yosadziŵika kwambiri, koma yangozi mofananamo. Mu 1927, zaka ziŵiri pambuyo pa kundandalitsa kwa Hitler kwa malingaliro ake pa fuko mu Mein Kampf, mlembi ndi katswiri wa zaumulungu Wachikatolika Joseph Mayer anafalitsa bukhu lokhala ndi lamulo la tchalitchi lachilolezo pa zosindikiza ndi zofalitsa lomwe linati: “Odwala maganizo, openga m’makhalidwe, ndi anthu ena otsika alibenso kuyenerera kwa kubalana koma kutenthedwa.” Pasitala wa Lutheran Friedrich von Bodelschwingh anapeza kufula opunduka kukhala kogwirizana ndi chifuno cha Yesu.

Maganizo ameneŵa ochirikizidwa mwachipembedzo anathandizira kupatsa malo lamulo la Hitler la mu 1939 lotchedwa “euthanasia decree (kupha ovutika),” limene linachititsa imfa zoposa pa 100,000 pa nzika zodwala maganizo ndi kufula mokakamiza chifupifupi anthu 400,000.a

Mpaka 1985, zaka 40 pambuyo pa mapeto a nkhondoyo, ndi pamene nduna za Tchalitchi cha Lutheran mu Rhineland zinavomereza mwapoyera kuti: “Tchalitchi chathu sichinatsutse mwamphamvu kwenikweni kufula anthu mokakamiza, kupha anthu odwala ndi opunduka, ndi kuchita kuchiritsa koyesera kwa nkhanza pa anthu. Tikupeza chikhululukiro cha minkhole yokhalabe ndi moyo ndi cha achibale awo omwe adakalipobe.”

Nzowona kuti ndawala ya boma ya euthanasia inabwerera m’mbuyo mokulira pambuyo pakuti bishopu Wachikatolika wa ku Münster anapereka nkhani yotsutsa mwamphamvu pa August 3, 1941, akutcha lamulolo kukhala kupha. Koma nchifukwa ninji panapita miyezi 19 ndi kuchititsa imfa 60,000 chitsutso chapoyera chisanamveke?

Liwongo la Mwazi la Chipembedzo

Zipembedzo zambiri zimati zimalemekeza moyo ndi kukhala zofunadi kutetezera anthu ku ngozi. Koma kodi atsogoleri achipembedzo moyenerera amachenjeza nkhosa zawo ku ngozi zakuthupi zophatikizidwa m’kusuta; kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa, kuphatikizapo zakumwa zoledzeretsa; kuthiridwa mwazi; ndi chisembwere chakugonana? Chofunika koposa, kodi iwo amatsutsa ntchito za thupi zimenezi monga mmene Baibulo likuchitira, ndikumalongosola kuti izo zingatilande chivomerezo cha Mulungu?—Machitidwe 15:28, 29; Agalatiya 5:19-21.

Ndithudi, ena amatero. Ndipo Tchalitchi cha Chikatolika limodzinso ndi matchalitchi ena a Fundamental amasonyeza ulemu ku moyo ku mlingo wa kutsutsa kuchotsa mimba monga kukhetsa mwazi wopanda liwongo. Komabe, lamulo la kuchotsa mimba Lachikatolika ku Italy liri limodzi la malamulo olekerera koposa ku Europe.

Chiphunzitso cha Chibuda nachonso chimatsutsa kuchotsa mimba. Koma mu Japan m’chaka chimodzi chokha, 618,000 kunasimbidwa kukhala kunachitidwa, ngakhale kuti 70 peresenti ya chiŵerengero cha anthu ali Achibuda. Izizo zimadzutsa funso lakuti: Kodi ndi pamaziko otani amene tiyenera kuweruzirapo chipembedzo, pa zimene nduna zake ndi atsogoleri achipembedzo ake ena amanena kapena pa zimene unyinji wa ziŵalo zake zakaimidwe kabwino zimachita?

Chitsanzo china cholephera kuchenjeza woipa chimachita ndi kuŵerengera zaka kwa Baibulo limodzi ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo. Ziŵirizi zimasonyeza kuti mu 1914 Ufumu wa kumwamba wa Mulungu unakhazikitsidwa m’manja mwa Yesu Kristu.b Ngakhale kuti Dziko Lachikristu limasekerera tsiku lakubadwa kwa Kristu lolingaliridwa December iriyonse, atsogoleri achipembedzo sakumlengezanso iye monga Mfumu yolamulira monga mmene atsogoleri Achiyuda sanamlandire iye monga Mfumu Yolinganizidwa zaka mazana 19 zapitapo.

Atsogoleri achipembedzo, a chikhulupiriro chirichonse, omwe amalephera kuchenjeza za zotulukapo za kusamvera malamulo a Mulungu pa makhalidwe abwino ndi kukana kugonjera ku Ufumu wa Mulungu womalamulira, malinga ndi Ezekieli 33:8, akudzikundikira pa iwo eni liŵongo la mwazi. Kukhala chete kwawo kumangokulitsa umanjalende wawo pamene mamiliyoni a nkhosa zawo zikukhalanso ndi liŵongo la mwazi.

Motero, mwa kuwaza zovala zawo ndi mwazi wosachimwa, chipembedzo chonyenga chaluluza mwazi wokhetsedwa wa Kristu Yesu wopatsa moyo. (Onani Mateyu 20:28 ndi Aefeso 1:7.) Pa chifukwa chimenecho, mwaziwo wokhathamira ku zovala za chipembedzo chonyenga posachedwapa—mwamsanga ndithu—udzakhala wake weniweni!—Chivumbultuso 18:8.

“Chipembedzo Chonyenga—Chopambanidwa ndi Nthaŵi Yake Yakale!” sichidzapeza pothaŵira. Talolani kope lathu lotsatira likalongosole zonse.

[Mawu a M’munsi]

a Ichi m’njira inayake chiri chikumbukiro cha “mfiti” zoyerekezedwa kukhala 300,000 kufika ku 3,000,000 zomwe, kuyambira m’zaka za zana la 15, zinaphedwa modalitsidwa ndi papa.

b Onani Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, mitu 16-18, lofalitsidwa mu 1984 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Bokosi patsamba 28]

“Chipembedzo, m’mbali zambiri za dziko lerolino, chakhala mthandizi wa kusintha . . . Chikupitirizabe kusonkhezera kupha kokulira mu Northern Ireland ndi mofananamo pa kontinenti yaing’ono ya India ndi mu Philippines.”—The Encyclopedia of Religion

[Chithunzi patsamba 27]

Liŵongo lamwazi la chipembedzo chonyenga cha nthaŵi yakale, monga lasonyezedwa m’kudula nkhuni uku m’zaka za zana la 15 zotenthera otsutsa chikhulupiriro ambirimbiri, lichepa kutalitali ku cholembera chake mkati mwa zaka za zana la 20 lino

[Zithunzi patsamba 28]

Mabelu a tchalitchi a ku Germany anasungunulidwa kaamba ka zifuno za nkhondo mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya I

[Mawu a Chithunzi]

Bundesarchiv Koblenz

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena