Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 2/8 tsamba 30
  • “Walrus” ndi Malonda a Mankhwala Ogodomalitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Walrus” ndi Malonda a Mankhwala Ogodomalitsa
  • Galamukani!—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Zochitika Padzikoli
    Galamukani!—2014
  • Nyama za M’nkhalango Zomazimiririka za ku Africa—Kodi Zidzapulumuka?
    Galamukani!—1988
  • Kodi Tingapambane Pankhondo Yolimbana ndi Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Galamukani!—1999
  • Mmene Mankhwala Oletsedwa Amakhudzira Moyo Wanu
    Galamukani!—1999
Galamukani!—1990
g90 2/8 tsamba 30

“Walrus” ndi Malonda a Mankhwala Ogodomalitsa

CHINGAKHALE chovuta kulingalira za nyama zoyamwitsa ziŵiri zazikulu zosiyana kwambiri ndi walrus ndi njovu. Koma maseal ololomoka, aakuluwo okhala m’madzi owundana oyandama a Bering Sea ali ndi vuto lofanana ndi limene zinyama zazikulu za mu nkhalango za Africa zikukumana nalo: Katundu wawo wa mtengo kwambiri kaŵirikaŵiri amatanthauza imfa yawo ya mwamsanga. Zonsezo ziri ndi minyanga.

Mwinamwake kuposa njovu, walrus imakhalira moyo minyanga yake. Pamene imamira pansi pa nyanja kukafuna chakudya, imakhwekhwereka pa minyanga yake popeza kuti imayamwa clams ndi oysters ndi milomo yake. Pamene ikufuna kutuluka m’madzi kupita kumtunda kwa madzi owundana oyandama kukawothera dzuwa, imagwiritsira ntchito minyanga yake monga zisonga zogwirira kukoka thunthu lake lolemera makilogramu 900 kufika ku 1,400. Walrus yaikazi imagwiritsira ntchito minyanga yake kuphera wolowerera aliyense amene angawopsyeze ana ake.

Koma zomvetsa chisoni kwa walrus, minyanga yake imawonedwanso kukhala ya mtengo ndi munthu. Munthu ali ndi ludzu losatha kaamba ka minyanga. Ndipo walrus ya utali wa mamita 3 kapena 4 yomawothera dzuwa ku malo ozizira a arctic imakhala chandamali chopepuka cha munthu wokhala ndi mfuti ya semiautomatic. Chotero sichachilendo kwa anthu aku Alaska kuyendayenda m’bwato mu Bering Sea, kupha nyamazo kulikonse kumene zingatuluke, ndi kubwerera kunyumba ndi bwato lodzaza ndi mitu yokhala ndi minyanga, yodulidwa ndi macheka a unyolo.

Nkhaniyi ikumveka kukhala yozoloŵereka, koma iri ndi kusiyana komvetsa chisoni tsopano: mankhwala ogodomalitsa. Zikuwoneka kuti Aeskimo achichepere aku Alaska akugwiritsira ntchito minyanga ya walrus kulipirira kumwerekera kwawo ndi mankhwala ogodomalitsa. Ndipo monga mmene magazine a Newsweek akudziŵitsira kuti: “Mlingo wa kusinthanawo ngwotchipa kwambiri.” Nthumwi yapadera ya U.S. Fish and Wildlife Service inawuza magazinewo kuti ogulitsa pa misika yosalembetsedwa mwalamulo angagule minyanga iŵiri—yokwanira unyinji wa $800—ndi ndudu zisanu ndi imodzi za marijuana.

Lamulo limapereka chitetezo chachikulu kwa osaka osati kwa osakidwawo. Limalola anthu aku Alaska kusaka walrus kaamba ka chakudya chimene ingawapatse. Ndithudi, akhoza kusunga minyanga monga zotsalapo zodzagwiritsira ntchito kupanga zinthu zamanja. Lamulolo limamveka kukhala labwino, koma liri pothaŵirapo kwa adyera. Amalonda ena a minyanga osakhala a kudzikolo asamukirako ndi akazi a Chieskimo kokha kuti anene kuti minyanga yawo njogwiritsira ntchito kupanga zinthu zamanja.

Pamene kuphako kukupitiriza, kudera nkhaŵa kukukula. Awo amene amasaka walrus mwalamulo ndi awo amene akugwiritsira ntchito minyanga kaamba ka ntchito yopanga zinthu zamanja akuwona kuti njira yawo yopezera zothandiza m’moyo ikuwopsyezedwa. Aeskimo achikulire akupeza mliri wa kumwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa pakati pa achichepere awo kukhala chothetsa nzeru. Kodi bwanji ponena za walrus? Padakali 250,000 za izo mu Pacific, chotero sizikulingaliridwa kukhala zikuwopsyezedwa. Koma mazanamazana a mitembo yawo yopanda mitu amakankhikira kumtunda. Yambiri yafika kumagombe a Siberia kotero kuti Soviet Union yauza United States kuti ileke kuphako. Koma kodi walrus idzakhalako kwa nthaŵi yaitali motani isanasoloke pamene minyanga yake ikutanthauza ndalama kwa aumbombo ndi mankhwala ogodomalitsa kwa osadziletsa?

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

H. Armstrong Roberts

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena